jpeg

Gawo #326, March 27, 2024

Dzikolapansi Lokoma: Kuyankha Pa Udindo Unapatsidwa Ndi Chilengedwe

Iyi tatumizanso titakonza yomwe tinakutumizilani ija mutu wapambamba.

Dziko la Mulungu lokoma linalinso ndi Milingo yofotokozedwa bwino monga taona kale. Mulungu anamuuza Adamu kuti panali mtengo umodzi omwe samayenela kudya. Zachisoni, sizinatenge nthawi kuti lamulo limenelo liphwanyidwe.

Genesis 3

6 Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso.

7 Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala.

8 Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo.

9 Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, “Uli kuti?”

10 Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.

11 Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?”

Adamu adadziwa kuti alakwa, anabisala mwamsanga pomwe anamva Mulungu akubwela. Koma chikadachitika nchiyani chifukwa cha zomwe anachitazo? Mulungu akuwaitana ndi kufufuza za zomwe zinachitika. Nkhani ikupitililabe (werengani Genesis 3:14-24) pomwe Pali nkhani yomwe ikufotokoza momwe Mulungu anawayankhila pa kusamvela kwawo. Kusinthana mau Kwa pakati pa Mulungu ndi banja loyambali likuonetsela chokometsela china chomwe Mulungu adamanga mu dziko lake lokoma, Kuyankha! Mfundo zoti atsatile zinali zomveka bwino, ndipo anayelela kuyankhapo chifukwa cha machitidwe awo. Atsogoleri omwe akutumikila amaphunzila kuti kuyankha ndi mbali imodzi yofunika pa utumiki wawo pamene akutipula dziko lapansi lokoma pozungulira pawo.

Kuyankha kumabweletsa kukoma povomeleza cholinga

Nkuona koyamba zitha kukhala ngati cholinga cha Mulungu pofunsa chinali choti alange ndipo anafotokoza momveka bwino zotsatila za zomwe anachitazo. Koma mtima wa Mulungu unaonetseledwa pomwe anafunsa , "Ulikuti?". Anafuna kubweletsa ubale omwe unaonongeka chifukwa cha kusamvela. Kubwezeletsaku sikudakatheka popanda kuyankhapo.P oipeleka nkhaniyo, Mulungu anaonetsa kuzama Kwa chikondi Chake pa Iwo ndi kufunikila kwakukulu komwe Mulungu anaika pa Iwo.Kufunsidwa kuti ayankheko kukuonetsa kuti machitidwe a Mulungi anali ofunikila !Zinaonetsanso kuti. Malamulo a Mulungu anali ofunikila! Ana a zaka ziwiri mwachangu amaphunzila ngati malamulo a makolo awo akutsatidwa pomayankha mafunso. Ndipo ngati palibepo Kuyankha pa zomwe wachita, mwana owonongeka amaumbika mwa Iye! Atsogoleri muutumiki amalenga kukoma pofunsa anthu kuti ayankhe pa zomwe achita.

Kuyankha kumabweletsa kukoma povomeleza zotsatila

Chigwele mamuna ndi mkazi oyamba, mwachilengedwe timakana kuyankhapo. Sitimafuna kufunsidwa pa zomwe tinachita! Koma atsogoleri muutumiki amavomereza dziko limene anthu amalimbika pozindikila kuti amayankhapo muzenizeni za maubale abwino. Amakhala ndi masomphenya a Malo ogwira ntchito omwe aliyense amamvetsetsa kuti ntchito yawo ndiyofunika koposa nchifukwa akuyenela kuti ayankhepo kapena apeleke malipoti. Amaona mmaso mwawo mipingo imene mamembala awo amamvetsetsa kuti ndioyenela kuti ayankhepo pa  zomwe akuyembekezela. Atsogoleri muutumiki amayembekezela kuchitabwino pomwe anthu akuyankhapo pa ntchito zomwe agwila.

Kuyankha kumabweletsa kukoma povomeleza zoikamo.

Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti ngati akuyenela kupanga ena kuti ayankhepo pa zomwe achita, iwowo akhale oyamba kukhala mdindo wabwino. Amavomeleza Udindo otsatila ntchito zawo ndipo amapempha chikhulukiro pomwe alephela. Kenaka amaonetsetsa kuti enananso ayankhepo pa zomwe achita. Samakhala ndi mantha kufunsa zomwe zinachitika. Amakhala achangu kupeleka mwai kuti ubale ulumbe podzeka munjila yofunsa  kuti mdindo ayankhepo. Ndipo pomwe anthu azindikila kuti zomwe akuchita zimalondedwa, amapita pamwamba ndi kuchitabwino! Atsogoleri muutumiki amalenga kukoma pa dziko lowazungulira pokhazikitsa kukhala mdindo.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi cholinga choyankhapo pokhala mdindo zinasokonezedwa bwanji mukuwona kwanu? Lingalirani makamaka za kaganizidwe mudela limeneli molingana ndi chikhalidwe chanu, banja lanu ndi mubungwe lomwe Inu mukutsogolera. Kodikuganiza  kotelo kwakhudza bwanji Inu ngati mtsogoleri? Kodi ndi munjila ziti zomwe mungakonze kaganizidwe kanu kuti mulingane ndi cholinga cha Mulungu?
  • Lingalirani kuti zotsatila zingakhale zotani ngati wina aliyense mubungwe lanu atamatsatila izi ndi kukhala motsatila ndondomeko zokhala mdindo omayankha pa ntchito zomwe wagwila. Lembani mfundo zosachepela zitatu.
  • Kodi muchitapo chani ngati mtsogoleri kuti anthu kunyumba kwanu, bungwe kapena mmudzi ayambe kutsatila ndondomeko yomayankha pa zomwe achita? Sankhani ndi ziti mwa   madela amenewa omwe Inu muikepo chindunji kenaka mulembe mfundo ziwiri kapena zitatu zomwe mutsate ndi madeti omwe muzachite zinthuzo.

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali tiona chokometsela china cha dzikolapansi lokoma: Kulephela Kumakhalapo.

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024