Gawo #322, January 17, 2024

Dzikolapansi Lokoma: Ntchito Ndi Ya Cholinga

Mulungu analenga dziko lapansi lokoma lodzala ndi moyo komanso kukongola. Analenga zomela zochuluka ndi nyama zamitundu yonse kenaka anaphatikizapo anthu olengedwa mchifanizo chake. Mulungu anapeleka ntchito zosiyana Kwa mamuna ndi mkazi.

Genesis 1

28 Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.

Genesis 2

15 Yehova Mulungu anatenga munthu uja ndi kumuyika mʼmunda wa Edeni kuti awulime ndi kuwusamalira.

Mulungu anapatsa ntchito Adam ndi Eva zomwe zinali ndi cholinga. Anawauza kuti "adzadze dzikolapansi" , "muligonjetse", ndi "mulamulire" chilengedwe, "mugwiremo ntchito" ndi "muliyang'anile". Mulungu anakonza ntchito ndi tanthauzo komanso cholinga ngati chokometsela mu dzikolapansi lokoma. Kugwa kwa munthu komwe kuli pa Genesis 3 kunasokoneza chikonzero chimenechi ndipo kunaonjezela thukuta ndi kuvutika ku ntchito ya Adam. Atsogoleri otumikila amagwila ntchito yobwezeletsa chikonzero cha Mulungu Cha poyamba mu malo omwe akutsogolera pothandizila omwe akuwatsogolera kuti apeze cholinga mu kugwila ntchito kwawo.

Ntchito ya cholinga imabweretsa kukoma pozindikila cholinga

Cholinga cha Mulungu chinali choti Adam ndi Eva apititse patsogolo ndi kuwumba dziko lapansi lomwe Iye adalenga. Amayenela kuti atulutse chakudya kuchokela munthaka. Koma amyenelanso kuganizira ndi kukhala ndi loto la njila zomwe chilengedwe chingaumbidwile kuti chitulutse kukongola koposa ndi chituluko. Mulungu adampatsa munthu udindo ofufuza, kulenga, kupanga pulani ndi  kutukula dziko lapansi. Kunali golide ndi miyala Ina yamtengo wapatali mudziko lapansi zomwe zinkafunika kuti zizindikilidwe ndi kuwumbidwa kukhala zinthu zogwilitsidwa ntchito. Ndipo ankayenela kupanga zonsezo monga nthumwi za Mulungu. Ntchito yawo inali yopitiliza ntchito Yake!

Atsogoleri otumikila amazindikira kuti Mulungu anaika khumbo la ntchito yokhala ndi tanthauzo mkati mmagazi a munthu aliyense. Palibe munthu yemwe amasangalala ndi kugwira ntchito ndicholinga chongolipira mabilu ndi kudya kuti akhale ndimoyo. Lingaliro lirlilonse, choumbidwa chilichonse, chozindikilidwa chilichonse chopangidwa ndimunthu chili ndi cholinga chowonjezela kupambana Kwa dzikolapansi la  Mulungu ndi kuthandiza anthu akhale moyo okoma. Ndipo chifukwa cha ichi, munthu aliyense agwire ntchito yodzala ndi cholinga.

Ntchito ya cholinga imabweretsa kukoma pozindikila phindu.

Anthu ambiri amaona ntchito ngati choipa chongoyenera kuchitika kapena njira chabe yongopangila ndalama koma chikonzero cha Mulungu chinali choposela ichi. Anthu si makina ongopangila ndalama chabe. Analengedwa kuti asonkhanitse mphatso zawo ndi zapamtima pawo kuthandizila kulenga dzikolapansi lokoma.

Atsogoleri otumikila amalingalira makampani, midzi ndi mabanja omwe munthu aliyense amasonkha mbali yawo ku chochitika chowoneka chenicheni. Amalingalira malo ogwira ntchito omwe anthu amabweretsa uphumphu wawo kuntchito yomwe ilipo, malo omwe anthu amabweletsa pamodzi malingaliro pa zoti zisinthe ndi pomwe maganizo awo amalandilidwa. Amakhala ndi masomphenya a kampani yomwe ngakhale munthu yemwe akuchita ntchito ya pansi amamvetsetsa kuti ntchito yawo ikuthandizila kusintha zinthu mdziko lapansi. Mudziko ili lokoma nzelu zili mwa munthu zimapelekedwa, malingaliro amapatsidwa mphamvu, ndipo phindu lalikulu limaonjezedwa ku dzikolapansi.

Nchito ya cholinga imabweretsa kukoma povomeleza zotsatila.

Atsogoleri otumikila amazindikira kuti ntchito ya cholinga si ya mwachikhalidwe. Amazindikila kuti amafunika Kuti agwire ntchito molimbika kuti apange dziko lawo kukhala lopambana. Amayamba ndi kufotokoza momveka bwino cholinga chachikulu chamaziko a bungwe lawo. Amasuntha chindunji chawo kuchoka pa gawo longotulutsa kupita ku kusintha komwe angabweletse ku dzikolapansi. Kenaka, amagwila ntchito molimbika kuzindikilitsa aliyense mubungwe lawo kufikila wina aliyense atamvetsetsa za momwe nchito yawo imathandizila ku cholinga. Amagawana nkhani za momwe bizinesi yawo ukupindulila kapena bungwe lawo kudziko lapansi. Atsogoleri otumikila amalenga dzikolapansi lokoma pozungulira pawo pogwira ntchito ndicholinga.

Zoti tilingalire ndi kukambirana:

  • Kodi cholinga chogwira ntchito ya cholinga chakhala chikusokonezedwa motani mukuona kwanu? Lingalirani makamaka mmene anthu amaganizila molingana ndi chikhalidwe chanu, banja lanu, ndi mubungwe lomwe Inu mumatsogolera. Kodi kuganiza koteleku kwakhudza bwanji Inu ngati mtsogoleri? Kodi mukuyenera kusintha njila ziti ndi ziti za kaganizidwe kanu kuti mulingane ndi cholinga cha Mulungu.
  • Ganizani kuti phindu lingakhale lotani ngati aliyense mu bungwe lanu atamatsatila izi ndi kuleka maganizidwe akale kuti ntchito ikhale yacholinga. Lembani mfundo zosachepela zitatu.
  • Ganizilani za bungwe lomwe mumatsogolera. Kodi cholinga chake ndichani? Kodi muli ndi sitetimenti yolembedwa ndikufotokozedwa bwino ya chifukwa chomwe bungwe linayambitsidwila? Kodi anthu omwe mumawatsogolera amamvetsetsa chifukwa chomwe ntchito yawo Ili yofunikila mdziko lapansi? Kodi mumakamba mochuluka za cholinga monganso momwe mumakambila za zachuma?
  • Kodi mutsatila ndondomeko ziti ngati mtsogoleri kuti  mubweletse cholinga ku ntchito yomwe ili kunyumba kwanu, bungwe kapena mmudzi? Sankhani ndidela liti la magawo amenewa omwe Inu muikepo ndidwi chanu kenaka mulembe mfundo ziwiri kapena zitatu zomwe mutsate ndi ma deti omwe muzachite ntchitoyo.

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler,

Muphunziro lotsatirali, tiona chokometsela china cha dzikolapansi lokoma: Milingo Imafotokozedwa.

 

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024