Gawo #321, December 15, 2023

Dziko Lapansi Lokoma: Kusiyanasiyana Ndi Chilengedwe

Chokometsela chachiwiri mu dzikolapansi lokoma ndi choti kusiyana ndi chilengedwe. Mulungu analenga dziko lomwe linali lokongola ndi lokoma... ndi losiyana!

Genesis 1

27 Ndipo Mulungu analenga munthu m╩╝chifanizo chake. Anawalengadi m╩╝chifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.

Kuyambila pa chiyambi Mulungu analenga anthu onse mu chifanizo chake; Koma si onse omwe analengedwa anali ndendende "analenga Iwo mamuna ndi mkazi." Chilengedwe Cha Mulungu chinamangidwa pa kusiyanitsa ndipo mu chikonzero chake kukoma Kwa dziko kumachitika pomwe kusiyanaku kulipo.

Chilengedwe chosiyanasiyana chimabweletsa kukoma pozindikila cholinga .

Mulungu anawalenga Iwo "Mamuna ndi mkazi" Kodi cholinga chake chinali chotani? Bwanji Mulungu sanangopanga munthu wina ofanana? Chifukwa chani mmalo mwake analenga munthu osiyana ndipo pa nthawi yomweyo, wamkazi? Tengani nthawi kuganiza dziko lodzadza ndi amuna okhaokha. Tsopano ganizilani dzikolapansi lodzadza ndi akazi okhaokha. Kodi mau awa akanakhala motani? Sizitengela munthu kukhala ndi maphunziro a ukachenjede kuti tizindikile kuti munjila iliyonse sizikanapangitsa dzikolapansi lokoma! Mulungu anamanga Kusiyanasiyana mwachikonzero chake kuti zitithandizile kuzindikila kuti sitili athunthu patokha. Kusiyana kwapadeladela kwa wina aliyense sikunakaonetseledwa munthu aliyense akanakhala ofanana ndi mzake. Kusiyana  ndi kofunika.Mulungu anamanga kusiyana mu dzikolapansi ndi cholinga choti tizindikile kufunika kwathu kwa ena. Iyi ndi mbali ya chifukwa chomwe anthu onse amafunila kukhala pamudzi ndi pa ubale ndi ena. Pomwe talowa mu ubale ndi ena timaonetsela kwathunthu chifanizo cha Mulungu ndipo kusiyana kwathu kumatulutsa dziko lapansi lokoma. Atsogoleri muutumiki  amavomereza chikonzero cha Mulungu pa Kusiyanasiyana ndipo amazindikira kuti sangakhale okwanila paokha.

Chilengedwe chosiyanasiyana chimabweletsa kukoma poona phindu.

Dziko lathu ndi lodzadza ndi zosiyanasiyana, koma kawilikawili timavomela kusiyanaku kutigawe mmalo moti kuyanjanitse. Timavomeleza kusiyana kuti kukhale chotipangitsa kukhulana ndi kukangana mmalo mwa ubwino. Nkhondo zimakhalapo pakati pa mitundu ndi maiko. Anthu kawilikawili amamenyana pa kusiyana kwawo mmalo moti akondwele. Magulu osiyanasiyana amalimbana chifukwa cha maufulu awo. Anthu osiyanasiyana amayambitsa magawano ndi kupatukana mmalo mwa kugwilizana ndi umodzi. Koma atsogoleri muutumiki amayang'ana Kwa chikonzero cha Mulungu ndi kuganizira dziko lomwe kusiyana ndi chikonzero Chake. Amakhala  akufuna  mabanja omwe abambo ndi amayi amakhala ndi kuwelengeledwa kofanana ndi kutamandidwa mofanana. Amaona masomphenya amabungwe omwe magulu amphamvu amabweletsa kusiyana kwawo poyela ndi kugwilana manja kuti agwile ntchito pamodzi ndicholinga chokwanilitsa zotsatila zambiri, zabwino ndi zofulumilirapo kusiyana ndi zotsatila pa  mphamvu za munthu mmodzi. Ndipo atsogoleri muutumiki amalota za zotsatila zabwino izi kuchoka ku banja lina kufikila pa linzake, kuchoka pa mpingo umodzi kufikila pa unzake ndinso pa bizinesi imodzi kufikila pa inzake.

Chilengedwe chosiyanasiyana chimabweletsa kukoma povomeleza zoikamo.

Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti kuchitapo kanthu ndikofunika kuti zitheke zamangovomeleza kusiyana kokha; komanso amakulandila! Choyambilira anazindikila chosowa chawo choti amafuna ena. Amamvetsetsa kuti kulibe atsogoleri omwe ndi ozizungulira okha, koma kuti pali  magulu omwe amazunguliridwa bwino. Kotero amaitana ena kugulu lawo omwe ndiothandizila koma osiyana. Amagwira ntchito molimbika kuti avomeleze ndi kuyamikila anthu osiyanasiyana mmaonedwe azinthu ndi mfundo zowo. Amaika chindunji pa kuthekela kwapadela komwe wina aliyense alinako payekha. Amaika chidwi pa mphamvu zosiyanasiyana zomwe munthu aliyense amaika mu gulu lawo ndipo amatumikila powathandizira kupeza malo abwino oti mphatso zimenezo zionetseledwe. Atsogoleri muutumiki amalenga dzikolapansi lokoma pozungulira Iwo povomeleza kusiyana.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi cholinga cha kusiyana mchilengedwe mwakumvetsetsa bwanji mukuwona kwanu? Lingalirani makamaka mmaganizidwe a mbali iyi,muchikhalidwe chanu, mubanja lanu, ndi mubungwe lomwe Inu mumatsogolera.Kodi guganiza kotelo kuli ndi zotsatila zotani pa Inu ngati mtsogoleri? Munjila ziti zomwe mungakonze kaganizidwe kanu kuti kafanane ndi cholinga Mulungu?
  • Lingalirani momwe zotsatila zingakhalire ngati wina aliyense mubungwe lanu atamagwiritsa ntchito kwathunthu ndi kukhala moyo ovomeleza kusiyana muchilengedwe. Lembani mfundo zosachepela zitatu.
  • Kodi ngati mtsogoleri muchitapo chani kuti kuvomeleza chilengedwe chosiyanasiyana munyumba mwanu, mubungwe kapena mudela mwanu  zizichitika? Sankhani kuti ndimbali iti ya zinthu ziwili kapena zitatu zomwe muchite ndi madeti omwe muzachite zinthu zimenezi.

 

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wa paulendo ,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona za chokometsela china cha dzikolapansi lokoma: Ntchito ndi Ya Cholinga

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2023