Gawo #319, November 15, 2023

Dziko Lapansi Lokoma: Chikonzero Cha Mulungu

Mulungu anakonza dziko lapansi kuti lizikoma. Osati kuti tingopezeka kapena kungakhala ndimoyo ,koma kuti tichitebwino! Analenga dziko lapansi lokoma.

Genesis 1

1 Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.

20 Mulungu anati, “Mʼmadzi mukhale zamoyo zochuluka ndipo mbalame ziwuluke mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi.”

31 Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

Chithunzithunzitu chokoma ichi cha dzikolapansi! Kunali zofunikila zonse, zochuluka, kuchitabwino mmoyo, kuchuluka, moyo, thanzi, bata ndi kukongola. Dziko linali lodzala ndi mitengo yobiliwila mokoma, maluwa okongola ndipo kunali kusangalala ndimoyo ,linali dzikolapansi lokoma! Chimenechi chinali chikonzero cha Mlengi.

Mu phunziro iri tiona za zokometsela zomwe atsogoleri muutumiki amatipulira kuti alenge dziko lapansi lokoma. Choyamba, amalingalira za kufunikila Kwa chikonzero cha Mulungu Cha moyo wokoma.

Chikonzero cha Mulungu chimabweletsa kukoma ku dziko lapansi pozindikira cholinga.

Dziko lapansi lokoma lomwe Mulungu analenga silinachedwe kusinthika pomwe uchimo unalowa, koma cholinga  Chake cha Mulungu sichinasinthe. Chikonzero chake chinamangidwa mu zipangizo zobelekela dziko! Monga momwe Mulungu analengela kuthekela kopanga moyo ndi kukula, atsogoleri omwe amamvetsetsa chikonzero cha Mulungu amagwila tchitoyi pamodzi ndi Iye pobwenzeletsa dziko lokomali. Atsogoleri muutumiki amazindikira cholinga cha Mulungu pomwe akulenga ndi kuwumba ndikupanga Malo omwe amafanana ndi chikonzero Chake cha kuchitabwino.

Chikonzero cha Mulungu chimabweretsa kukoma pa dziko lapansi powona phindu.

Kodi dziko lapansi lokoma limaoneka bwanji mu bizinesi,mu mpingo, mu fakitale, kapena ku sukulu? Pomwe anthu akuchitabwino, amaima chilili ndi moongoka. Amayenda motsimikizika zedi ndi kutenga ulamuliro oyenelera pa ntchito yomwe yapatsidwa Kwa iwo Amazindikira kufunika Kwa ntchito yawo. Ndipo amapeza chimwemwe ndi kukhutila pa zomwe akuchitazo ndipo mochuluka amapereka mphatso zawo zapadeladela zomwe alinazo. Amaganizila za njira zopititsila patsogolo ndi kugawa nzeru zawo kwaulere. Amakula ndikukhala ochitachita ndi mtimaonse. Phindu la kuchitabwino kwa moyo wawo kumafalikila mpaka kumalo antchito, kumafika mpaka mmanyumba ndi mmadela omwe amakhala. Pozungulira iwo amalimbikitsa ena kukula ndi kukhala moyo ochitabwino. Atsogoleri muutumiki amazindikira kusiyana komwe kunabwela pokhala moyo ochitabwino kwa Iwo amene akuwatumikira ndipo amachita chilichonse chomwe angathe kuti apange danga lomwe lingawalimbikitse iwo kuchitabwino.

Chikonzero cha Mulungu chimabweretsa kukoma pa dziko lapansi  povomeleza zoikamo

Kodi chikonzero cha Mulungu chikuonetsera zoikamo zanji Kwa atsogoleri? Atsogoleri muutumiki amayang'ana ndi kuyembekezela kuchitabwino mu mabungwe awo. Kuchuluka ndi chiwelengelo si cholinga chawo chenicheni; Kuchitabwino ndiko! mulingo wa kupambana kwawo uli pa anthu omwe aima chilili ndi kukula. Atsogoleri muutumiki amavomerezanso mbali yawo mkati mwandime. Monga momwe Mulungu analengera malo omwe anatulutsa kuchitabwino, atsogoleri ali ndi udindo olenga ndi kuwumba malo ofanana ndi mmene Mulungu amachitira. Atsogoleri ali ngati alimi omwe amaonjezera zokometsela ku nthaka kuti mbewu zikulebwino. Atsogoleri amavomereza udindo wawo ngati omwe amakhala ndi chindunji pa "dothi"mu bungwe lawo ndipo amakhalabe akuwonjezela zokometsa kufikira aliyense akuchitabwino. Kodi zokometsela zimenezi ndiziti? Tizaona chokometsela chimodzi pa phunziro liri lonse mu mutu umenewu. Atsogoleri muutumiki amalenga dziko lapansi lokoma pomwe ali pomvetsetsa chikonzero cha Mulungu.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • werengani chaputala choyamba Cha Buku la Genesis kuti mupeze kukongola Kwa chikonzero Cha Mulungu. Ndipo miyankhe mafunso ali mmunsiwa
  • Kodi cholinga cha chilengedwe Cha Mulungu chasokonezedwa motani mukuona kwanu? Mulingalire makamaka kuganiza pa dela la mu chikhalidwe chanu,mubanja lanu, ndi mubungwe lomwe mumatsogolera. Kodi kuganiza koteleku kwabweretsa chani pa Inu ngati mtsogoleri? Kodi ndisinthe munjira yanji yamaganizidwe kuti ndilingane ndi cholinga cha Mulungu?
  • Lingalirani kuti zotsatira zizakhala zotani ngati aliyense mu bungwe lanu azagwilitsa ntchito kwathunthu ndi kuleka mmene zimayenela kukhalira potsata chikonzero cha Mulungu. Mulembepo mfundo zitatu.
  • Kodi mutenga masitepe ati ngati mtsogoleri kuti mugwiritse  ntchito molingana ndi  chikonzero cha Mulungu mubanja lanu, bungwe, kapena dela? Sankhani ndi magawo ati pa amenewa omwe mukuyenera kuikapo chindunji kenaka lembani ndandanda  wa ziwiri kapena zitatu zomwe mungatsate ndi masiku ake omwe muchitepo kanthu.

 

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona chokometsela chotsatira cha dziko lapansi lokoma: Anthu ndi a Mtengo wapatali.

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2023