Kuika munthu woyenera pa malo oyenera ndi chinthu chimodzi mwa zobetchera za utsogoleri. Tingathe kuwona kusankha kwa atsogoleri kudzera ku nthambi yoona za anthu apantchito omwe amawona mbiri ndi zomwe munthu wachita. Atsogoleri otumikira mosamalitsa angathe kugwiritsa ntchito zinthu izi, koma amafunanso posankha atsatire chitsogozo cha Mulungu. Adzaloza ku mpingo oyamba pofuna kuwona ngati njira yawo ya kasankhidwe ka atsogoleri ndi ya ‘mbaibulo’ ndipo kuti ndi njira yoyenera. Koma kodi ndi chani chomwe Machitidwe amaphunzitsa atsogoleri otumikira pa njira yoyenera yosankhira atsogoleri? Pali njira pafupifupi zinayi zosiyana zomwe atsogoleri adasankhidwira mu mpingo oyamba. Taona kale zitatu ‘kusankhidwa ndi Mulungu’ ndi ‘kusankhidwa ndi gulu la anthu’ ngati njira zosiyana zomwe atsogoleri ankasankhidwira mu mpingo oyamba. Koma apa pali njira ina.
21’pamena dalalikira uthenga wabwino pamudzipo , nayesa ambiri ophunzira , adabwera ku Listra ndi Ikonio ndi Antiokeya,22nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe mchikhulupiliro, ndi kuti tiyenera kulowa muufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.23Ndipo pamene adawaikira akulu mosankha mu mpingo uliwonse, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, naikiza iwo kwa ambuye amene anamkhulupilirayo.’(Machitidwe 14: 21-23)
Mu nyengo iyi, atsogoleri a mpingo, Paulo ndi Barnabasi, adaloza atsogoleri mu mpingo uliwonse. Tiyeni tilingalire za kusankha atsogoleri kwa mtundu uwu.
Ndondomeko yosankha posankhidwa ndi utsogoleri. Ndondomeko yomwe idagwiritsidwa ntchito ndi Paulo ndi Barnabasi ikuwoneka yophweka, iwo ‘adangowaikira akulu’ mmipingo imeneyi. Sizikuoneka kuti iwo adapempha mamembala a mpingo kuti ayikepo mawu ndipo sadachite masankho. Komabe, ‘kupemphera ndi kusala’ zidali gawo la ndondomekoyi. Atsogoleri otumikira amaphunzira kuchokera ku chitsanzo chawo kuti posankha atsogoleri mu njira iyi ndi zothandiza kwambiri kusaka chitsogozo cha Mulungu. Atsogoleri otumikira samagwiritsa ntchito njira iyi pofuna kuika amzawo kapena a pabanja lawo mu ntchito ya utsogoleri. Amagwititsa ntchito njira iyi machitidwe abwino omwe akathandizira anthu omwe akakhala pansi pa atsogoleri omwe asankhidwa kumene. Pomwe atsogoleri otumikira agwiritsa ntchito njira iyi mmalo a malonda, amakhala osamalitsa kulingalira kukhudza komwe kudzakhalako pa anthu otsatira kamba ka chiganizo chawo.
Mphamvu yakusankha posankhidwa ndi utsogoleri. Pali ma ubwino angapo kamba kosankha posankhidwa ndi utsogoleri. Ndi njira yosavuta ndipo ingathe kuchitika mwachangu ngati pali chinthu choti chichitike mwachangu. Mu nyengo zina, mtsogoleri yemwe akusankhayo angathe kudziwa bwino mphatso, maitanidwe ndi kuthekera kusiyana ndi omwe akumutsatira. Monga momwe zidalili ndi mipingo imeneyi, Paulo ndi Barnabasi mwina adazindikira mulingo wa kukhwima mwa okhulupilira atsopano kuti sikunali kokwana ndi kwamphamvu kusankha mtsogoleri woyenera. Choncho, njira iyi ingathe kukhala yabwino ku gulu longoyamba kumene. Atsogoleri omwe adasankhidwa mu njira iyi adali ndi thandizo loonekeratu lochokera kwa Paulo ndi Barnabasi, omwe adadzala mpingo ndipo ndi omwe amaoneka ngati owaimilira. Atsogoleri otumikira amaphunzira kuchokera ku chitsanzo ichi kuchita mosamalitsa polingalira mphatso, ndi maitanidwe amunthu ndi kufunanso chitsogozo cha Mulungu asadachite chilichonse. Kenako motsimikizika amasankha atsogoleri kuti onse zikawachitile ubwino.
Makhwekhwe kamba kosankha posankhidwa ndi utsogoleri. Pomwe mwina tingathe kuona kuti palibe vuto ndi kusankha komwe Paulo ndi Barnabasi adachita, njira iyi iyenera kugwIritsidwa ntchito mosamala. Mphamvu yosankha ena osaikapo maganizo awo ingathe kupanga mtsogoleri kukhala odzikonda ndipo angathe kusankha molakwika. Kusiya anthu kunja kwa ndondomekoyi zingathe kugwira mu nyengo zina koma malo ena zotsatira zake anthu adzakwiya ndi atsogoleri osankhidwawo. Ndipo munthu wosankhidwayo atha kumapereka ulemu wake kwa yemwe adamusankhayo mmalo modzipereka potumikira anthu a pansi pake. Atsogoleri otumikira mwanzeru amapewa makhwekhwe osankha pogwiritsa ntchito utsogoleri. Monga Paulo ndi Barnabasi, amafuna chitsogozo kuchokera kwa Mulungu ndi kusankha gulu mmalo mwa munthu mmodzi. Iwo samalora kuti iyi ikhale njira yokhayo yosankhira atsogoleri.
Atsogoleri otumikira amaona njira yosankha pogwirritsa ntchito utsogoleri ngati imodzi mwa njira yomwe Mulungu angalamulire pa mamangidwe a gulu lawo.komanso amazindikira kuti pali nthawi zina zomwe Mulungu adzawatsogolera kusankha njira ina. Mu gawo lotsatira, tidzawona njira yotsitiza yosankhira atsogoleri. |