jpeg

Gawo #280, March 17, 2021

Ntchito yosankha atsogoleri: Kusankhidwa ndi gulu

Atsogoleri amasankha atsogoleri ena kuti akhale nawo mu gulu ndi kuwathandiza kukwaniritsa masomphenya. Koma ndondomeko yomwe amagwiritsa ntchito imasiyana potengera momwe zinthu zilili.

Buku la Machitidwe limatipatsa pafupifupi njira zinayi zomwe mpingo woyamba udasankhira atsogoleri. Imodzi mwa iyo idagwiritsidwa ntchito pomwe ntchito ya atumiki idafunika.

‘Koma masiku amenewo, pakuchulukitsa ophunzira, kudauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye awo adaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku. Ndipo khumi ndi awiriwo adaitana unyinji wa ophunzira, nati sitikuyenera kuti ife tisiye kulalikira mawu a Mulungu ndi kutumikira podyerapo. Chifukwa chake abale, yang’anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri ya bwino, wodzala ndi mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi. Koma ife tidzalimbika nkupemphera ndi kutumikira mawu. Ndipo mawu amene adakonda unyinji wonse; ndipo adasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiliro ndi mzimu woyera ndi Filipo ndi Prokoro ndi Nikanore ndi Timoni ndi Parmenasi ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya’ (Machitidwe 6: 1-5)

Atsogoleri otumikira amazindikira kuti kupereka mphamvu kwa ena kupanga chisankho nthawi zina kungathe kukhala njira yabwino kwambiri yosankhira atsogoleri.

Ndondomeko yosankha kudzera mugulu. Mu nyengo imeneyi, atumiki asanu ndi awiri adasankhidwa. Koma atumwi sadapange chisankho; adaitana gulu kuti lisankhe anthu omwe adzakhale atsogoleri. Uku kudali kusankhidwa pogwiritsa ntchito gulu, zofananirako ndi ndondomeko ya demokirase pomwe chisankho chimachitika. Ili likadakhala khwerero loopsa kwa atumwi. Chikadachitika ndi chani ngati anthuwo akadasankha munthu wolakwika?

Njira iyi imagwiritsidwa mu mipingo yambiri momwe mavoti amawerengedwa ndipo ‘opambana’ amalengezedwa. Izi mwina sizingachitikechitike mu malonda, koma tsogoleri wotumikira yemwe ndi mwini wake kapena mtsogoleri angathe kuwafunsa ena kutengapo mbali pa chochitikachi popereka maganizo awo, momwe azionera kapena pochita kalondolondo. Ngakhale kuti chiganizo chenicheni sichichokera ku mavoti, mtsogoleri wotumikira ndi okhumba kulora ena kupezeka mu ndondomeko iyi. Njira iyi imasowekera kudzichepetsa ndi chikhulupiliro chozama mwa anthu ndi Mulungu! Atsogoleri otumikira ali ofuna kumasula mphamvu zawo kwa ena.

Mphamvu yosankha kudzera mugulu. Njira iyi ili ndi maubwino ambiri. Ubwino umodzi owonekeratu ndi woti iwo omwe adzatsogoleredwa amapatsidwa mphamvu potenga nawo mbali. ‘ndipo mawu amene adakonda unyinji wonse’ pomwe anthu atenga nawo mbali popanga chiganizo, sangadandaule kwambiri kamba ka zotsatira!

Sichokhachi, koma atsogoleri omwe asankhidwa kudzera mu njira iyi amamva thandizo la anthu omwe adzawatsogolere kuyambira pa chiyambi. Amayamba kutsogolera molimba mtima kuti womwe akuwatsogolera ndi omwe akufuna kuti iwo atumikire ntchito imeneyo. Ubwino wina wa njira iyi ndi woti anthu omwe apanga chiganizo chachidziwikire adzakhala pafupi ndi atsogoleriwa mosiyana ndi atsogoleri omwe ali pamwamba pa bungwe. Atsogoleri otumikira amavomereza kuti siwokhawo omwe angathe kusankha atsogoleri ndipo kuti ena mwanzeru angathe kutengapo mbali.

Makhwekhwe kamba kosankha pogwiritsa ntchito gulu. Atsogoleri otumikira amavomereza kuti pali zinthu zina zoopsa mu ndondomeko ya demokirase. Kuopsa kumodzi ndi kokuti kusankha kodzera mu gulu kungathe kusiya Mulungu kunja kwa ndondomekoyo! Chisankho chingathe kudza chifukwa chakudziwika kwa mmunthuyo.

Kuopsa kwina ndi koti tcheru chofuna kusangalatsa anthu chingathe kukhala chofunika kwambiri kusiyana ndi maitanidwe otsogolera anthu. Ichi ndi chiopsezo makamaka kwa iwo omwe chikhalidwe chawo chimakonda kusangalatsa ena.

Koma atsogoleri otumikira mwamzeru angathe kuchititsa ndi kutsogolera ndondomeko ya chisankho ngakhale kuti ena ndi omwe angapange ziganizo. Atumwi adaika zinthu zina zoyenera apa masankho asadayambe; ankafuna anthu omwe adali ‘odzala ndi mzimu ndi mzeru.’ Atsogoleri angathe kulengeza kusala ndi kupemphera ndondomeko isadayambe komanso pomwe ndondomeko ili mkati. Angathenso kupereka malangizo pa mtundu wa atsogoleri omwe akufuna.

Atsogoleri otumikira amaona njira yosankha kudzera mugulu ngati imodzi mwa njira zomwe Mulungu amawauza pomanga gulu lawo. Komanso amazindikira kuti pali nthawi zina zomwe Mulungu adzawatsogolera iwo kusankha njira ina. Mu gawo lotsatira tidzawona imodzi mwa njirazi: kuloza

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

 

  • Kodi zomwe ndadutsamo kale komanso kuganiza kwa omwe andizungulira zawumba bwanji kaonedwe kanga ngati kusankhidwa ndi gulu ndi njira yabwino yosankhira atsogoleri kapena ayi?
  • Kodi mwachidziwikire ndingagwiritse ntchito njira iyi posankha atsogoleri? Ngati ndi chachidziwikire kuti ndidzagwiritsa ntchito njirayi, kodi ndapewa modziwa bwino makhwekhwe a njirayi? Ngati ndi zokaikitsa kuti ndingagwiritse ntchito njirayi, ndi munjira iti yomwe mwina Mulungu akundiitana kuti ndilingalire kamba ka nyengo zanga?
  • Ndi nyengo ziti zomwe mwina kusankhidwa ndi gulu kungathe kukhala njira yabwino yosankhira atsogoleri kwa ine? Ndi nyengo ziti zomwe mwina kusankhidwa ndi gulu kungathe kukhala njira yoipa kwa ine?
  • Mu gawo lotsatira, tidzawona kusankhidwa kwa atsogoleri poloza.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatira chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembatsa mwaulere komanso kuwona magawo akale. Mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.  Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi Abusa Joseph Saizi, josephsaizi2017@gmail.com
 

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2021

Modify your subscription    |    View online