jpeg

Gawo #279, March 3, 2021

Ntchito yosankha atsogoleri: Ntchito ya uMulungu

Kusankha atsogoleri ena ndi chinthu chimodzi cha zobetchera zikuluzikulu za utsogoleri. Atsogoleri ambiri akhalapo ndi chipambano ndipo mwachidziwikirenso alepherapo mu gawo ili. ‘Mtengo’ wa kulephera ndi wokwera pomwe ndondomeko yosankha siyibweretsa munthu woyenera. Kodi njira yabwino ndi iti yopezera ena omwe angamange gulu ndi kuthandizira kukwaniritsa masomphenya?

Nthawi zambiri, chikhalidwe chathu kuphatikiza ndi zomwe tadutsamo kale, zabwino ndi zoipa zomwe, zimawumba momwe tingasankhire atsogoleri. Atsogoleri amalonda angathe kuphunzira kudalira pa njira yomwe idatsimikizika yosankhira munthu yemwe akuwoneka kuti angakhale oyenera. Atsogoleri ampingo mwIna angathe kutsamira kwambiri ku njira ya ‘uzimu’ yomwe imagwira ntchito bwino pomwe ali. Kenako adzayang’ana ku mpingo oyamba nkufuna kuona ngati njirayi ndi ya ‘mbaibulo’. Koma tikayang’ana mpingo oyamba mu Machitidwe ukuphunzitsa atsogoleri otumikira kuti pali pafupifupi njira zinayi zosiyana zosankhira atsogoleri.

Atsogoleri otumikira amaphunzira kuti njira zonsezi zitha kukhala zofunikira pamene zagwiritsidwa ntchito mmalo ndi njira yoyenera.

Njira yoyamba yosankhira atsogoleri mu bukhu la Machitidwe ndi pomwe Mulungu ayitana mtsogoleri mwachindunji. Ichi chidachitika kwa Paulo panthawi ya kupulumutsidwa kwake (Onani Machitidwe 9: 15-16) komanso pomwe iye ndi Barnabasi ankatumidwa ku ntchito ya utumwi pomwe adali ku Antiokeya.

2 Ndipo pakutumikira Ambuye iwowa, ndikusala chakudya, Mzimu woyera adati, mundipatulire ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.3 Pamenepo, mmene adasala chakudya ndi kupmphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke (Machitidwe 13:2-3).

Ndondomeko yosankha kudzera mkuyitanikwa kwa uMulungu. Ndi njira iyi, palibe kulowelera kwa chindunji kochokera kwa munthu mu ndondomekoyi. Mulungu adalankhula momveka bwino kudzera mwa mzimu ndi kuitana Barnabasi ndi Saulo. Ndizoona, anali oyenerezedwa mwa padeladela komanso otsimikiziridwa kale mu utsogoleri, koma padalibe ndondomeko yoti alowere pa ntchitoyo ndipo padalibe masankho!

Atsogoleri otumikira amavomereza kuti Mulungu payekha amatsogolera chisankho cha utsogoleri. Ndi ofuna kutenga nthawi nkusala ndi kupemphera pofuna chitsogozo chake. Ndipo pomwe Mulungu walankhula momveka bwino, amaika manja pa munthuyo ndi kumudalitsa!

Mphamvu yosankha kudzera mkuyitanidwa kwa uMulungu. Kuitanidwa kwa uMulungu kuli ndi ubwino opezekeratu: Mulungu walankhula! Ndi ndani yemwe angalimbane nazo? Njira iyi ingathe kukhala yogwiritsidwa ntchito nthawi zambiri mu mpingo kusiyana ndi malo a malonda. Koma ngakhala kumalo a malonda, pomwe atsogoleri otumikira akufuna kutsatira chitsogozo cha mzimu wa Mulungu, zingathe kupezeka nthawi zina zomwe liwu la Mulungu lingathe kuposa liwu la nthawi yowona anthu ogwira ntchito!

Atsogoleri otumikira amavomereza kuti Mulungu ndi amene ali ndi ulamuliro wonse ndipo kuti chitsogozo chake ndi chomveka bwino, mwakufuna kwawo amamvera!

Makhwekhwe kamba kakuyitanidwa kwa uMulungu. Kusankha atsogoleri kudzera nkuyitanidwa kwa uMulungu kulinso ndi zobetchera zowonekeratu.

Choyamba ndi chobetchera chakumva molondola ndi momveka bwino liwu la Mulungu. Zambiri zingathe kuonongeka pomwe mtsogoleri agwiritsa ntchito chilankhulo cha kuitanidwa kwa uMulungu pofuna kuyenereza chisankho chomwe chaperekedwa. Atsogoleri otumikira ayenera kukhala osamalitsa ponena okha, ‘Mulungu adandiuza ine kuti munthu uyu akhale mtsogoleri.’ Ku Antiokeya, padali chidziwitso chochokera ku gulu.

Kuopsa kwina kogwiritsa ntchito njirayi ndi koti pomwe mtsogoleri wasankha njirayi chifukwa chosafuna kuchita ntchito yovuta yofuna kudziwa kuti munthu woyenera ndi uti. Mwina sakufuna kapena sadapatsidwe kuthekera kowunguza mphatso, zomwe munthu wayendamo ndi maitanidwe a mtsogoleri woyenera. Choncho, amabwezera chisankhocho kwa Mulungu!

Zopatsa chidwi, mu Machitidwe 1, Matiasi adasankhidwa poponya mayere, njira ya uMulungu. Koma choyambilira, atumwi adaika zomwe amafuna molingana ndi ntchitoyo ndipo adasankha anthu awiri omwe adakwaniritsa zoyenerazo. Kenako adalora Mulungu kupanga chisankho chotsiriza kudzera mu kuponya mayere. Atsogoleri otumikira amaphunzira kudzera mu izi kuti ngati zinthu zoyenereza zoyambilira sizinakwaniritsidwe, padzakhala mavuto ambiri ndi njira imeneyi!

Atsogoleri otumikira amawona njira yosankhira atsogoleri kudzera nkusankha kwa uMulungu monga njira imodzi yomwe Mulungu angalamulire pomanga magulu awo. Koma amazindikiranso kuti pali nthawi zomwe Mulungu adzawatsogolera kusankha njira ina. Mu gawo lotsatira, tidzawona njira imodzi mwa izi: Kusankhidwa ndi gulu.

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

 

  • Kodi zomwe ndadutsamo kale komanso kuganiza kwa omwe andizungulira zawumba bwanji kaonedwe kanga ngati kusankhidwa kwa uMulungu ndi njira yabwino yosankhira atsogoleri kapena ayi?
  • Kodi mwachidziwikire ndingagwiritse ntchito njira iyi posankha atsogoleri? Ngati ndi chachidziwikire kuti ndidzagwiritsa ntchito njirayi, kodi ndapewa modziwa bwino makhwekhwe a njirayi? Ngati ndi zokaikitsa kuti ndingagwiritse ntchito njirayi, ndi munjira iti yomwe mwina Mulungu akundiitana kuti ndilingalire kamba ka nyengo zanga?
  • Ndi nyengo ziti zomwe mwina kusankhidwa kwa uMukungu kungathe kukhala njira yabwino yosankhira atsogoleri kwa ine? Ndi nyengo ziti zomwe mwina kusankhidwa kwa uMulungu kungathe kukhala njira yoipa kwa ine?

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatira chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembatsa mwaulere komanso kuwona magawo akale. Mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.  Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi Abusa Joseph Saizi, josephsaizi2017@gmail.com
 

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2021

Modify your subscription    |    View online