Taona njira zambiri zomwe atsogoleri otumikira ayenera kuphunzira kuti akhale chete. Koma nthawi yovuta kwambiri kukhala chete ndi pomwe anthu akukulikha kapena kukunenezera kuti wachita cholakwika. Pomwe ichi chachitika, mwachibadwidwe timaziteteza tokha, nthawi zambiri mokuwa! Kudziteteza wekha kumawonedwa kuti ndi ufulu wa munthu aliyense. Koma pomwe Yesu adali kuyankha mulandu, adationetsera njira yosiyana kwambiri. ‘Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe iye; koma sadaupeze zingakhale mboni zambiri zonama zidadza, koma pambuyo pake adadza awiri, nati, uyu adanena kuti, ndikhoza kupasula kachisi wa mulunguyu, ndikummangaso masiku atatu. Ndipo mkulu wa ansembe anaimilira, nati kwa iye, suvomera kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa akunenera iwe? Koma Yesu adangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa iye, ndikulumbiritsa iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiwuze ife ngati ndiwe Khristu, mwana wa Mulungu’ (Mateyu 26: 59-63). Kuthekera kwa Yesu kukhala chete munyengo imeneyi ndi zopatsa chidwi ndipo kuli ndi zambiri zomwe tingaphunzitsidwe malingana ndi mphamvu yokhala chete mu kudziteteza wekha.
Kukhala chete mukudziteteza wekha kumavumbulutsa kudzichepetsa. Kukhala chete kwa Yesu kudavumbulutsa kudzichepetsa kozama. Kumunenezera komwe adamchitira iye kudatanthawuzidwa molakwika pa zomwe adalankhula mu Yohane 2: 19. Zoona zake Yesu adayenera kukonza zinthu! Koma modzichepetsa adakhala chete, kukana kudziteteza yekha. Anthu odzikweza amalimbana ndi anthu pa mulandu wawo, amadziteteza okha mokuwa. Sangavomere kunenezedwa kulikonse komwe kungawonetse iwo kukhala oyipa kaya ndi koyenera kapena ayi. Koma atsogoleri otumikira amaonetsera kudzichepetsa pomwe akukhalabe chete pamene akunenezedwa molakwika.
Kukhala chete mu kudziteteza wekha kumaonetsa kutsimikizika mtima. Yesu adawonetsera kutsimikizika mtima kwabwino kwambiri mu uchete wake. Sadafune kulimbana zokhudzana ndi iye ngati Mesiya. Sadasowe kudziteteza kuti iye adali ndani. Ankadziwa kuti iye adali ndani. Kukhala chete kwake kudafuula kuti iye adalibe kanthu kotsimikizira. Kukhala chete kumalankhula mofuula kwambiri kumaposa kukuwa ndi kukangana. Kumavumbulutsa kutsikimizika kozama kuti sindikufuna kudzionetsera kuti ndine olondola; ndikudziwa ndine olondola. Nthawi zina phokoso la mphamvu kwambiri ndi kukhala chete. Atsogoleri otumikira amalankhula kutsimikizika kwawo pokhala chete pomwe akunenezedwa.
Kukhala chete mu kudziteteza kumayenera kudalira mwa Mulungu. Kukhala chete kwa Yesu pomwe adali kuyesedwa kumaonetsa kuti chidaliro chake chidali osati mu chigamulo cha mwamunthu wina aliyense yemwe angamtsutse kapena kumumasula. Adadziwa kuti adali Mulungu yekha yemwe akadatha kupanga tsogolo lake. Petro, patangotha mphindi zochepa chikhalireni chete Yesu, adzadziteteza yekha mwamphamvu (Onani Mateyu 26: 69-75). Koma zaka zotsatira pomwe akukumbukira za imfa ya Yesu adati, ‘Amene pochitidwa chipongwe sadabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sadaopsa, koma adapereka mlandu kwa iye woweruza kolungama’ (1 Petro 2: 23). Kukhala chete kwa Yesu kudachititsa Petro yemwe tsopano akutibetchera ife kutsatira chitsanzo cha Yesu. Atsogoleri omwe amazidalira okha amayenera kulankhula mofuula ndi mokopa podziteteza okha. Koma atsogoleri omwe amadalira chiweruzo cha Mulungu angathe kuyembekezera mwa kachetechete chigamulo cha Mulungu. Atsogoleri otumikira amaonetsera chidaliro mwa Mulungu pomwe akhala chete mu kudziteteza okha. Kodi ilopo nthawi yomwe mtsogoleri ayenera kulankhula pomwe akunenezedwa? Yesu, atangochoka pokhala chetepa, adalamulidwa ndi wamsembe wamkulu kulankhula. Pa nthawi iyi, modekha adalankhula choonadi choti iye adali ndani. Zilipo nthawi zomwe ndi koyenera kulankhula potetezera choonadi mmalo mwa ife eni. Koma atsogoleri otumikira amagwiritsa ntchito ufulu uwu atatha kuphunzira ululu wamwambo okhala chete. Amalira kwa Mulungu kuti awapatse mzeru zotha kudziwa nthawi yolankhula ndi nthawi yochititsa ena kudzera mkukhala chete. Utsogoleri wa chete umalankhula mofuula mukudziteteza wekha! Atsogoleri otumikira amakwera pamwamba potseka pakamwa!
|