Atsogoleri amachititsa ena powakopa. Angathe kukopa ena kutsatira masomphenya awo, kuthandizira zolinga, ndiponso kukhala gawo limodzi la gulu. Pafupifupi nthawi zonse, timayesetsa kukopa ena ndi mawu, makamaka mawu amphamvu ndi ofuula omwe amathera ndi mifuuliro! Koma nthawi zina kuchititsa kwakukulu pofuna kukopa ndi kukhala chete! Petro akulangiza akazi omwe ali ndi amuna osakhulupilira, ‘Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.’ (1 Petro 3:1-2). Mu nyengo ngati iyi, mwamuna sagwirizana ndi zikhulupiliro za mkazi wake. Chokhumba cha mkaziyo ndi kukopa mwamunayo kamba ka choonadi chomwe akuchidziwa. Mwina tingamulangize iye kuti awumbe mfundo zokhazikika zakupezeka kwa Mulungu komanso chifukwa chosowekera chipulumutso ndiponso kuzipereka izi molimbika mtima. Koma Petro akumulangiza iye kukhala chete! Kukhala chete kophatikiza ndi khalidwe la umulungu, zidzakopa mwamunayo ‘popanda mawu.’ Atsogoleri otumikira amaphunzira mphamvu yokopa pokhala chete.
Kukopa kwa chete kumavumbulutsa ulemu. Petro akulimbikitsa akazi kugonjera ‘opanda mawu’. Makangano ofuula adzaonetsa kupanda ulemu ndikupangitsa kuti mwamuna achoke. Koma kukhala moyo wake mwachete osamkakamiza iye kuvomereza, zimaonetsa ulemu kwa iye ngati munthu. Atsogoleri abwino amaonetsa ulemu kwa ena, makamaka kwa iwo omwe sagwirizana nawo. Amaonetsera ulemu kwa wina, nthawi zina pongopitiriza ubale popanda kukumbutsa mowirikiza za kusagwirizana kwawo. Amazindikira kuti ulemu udzatsegula khomo la kuchititsa. Atsogoleri otumikira nthawi zambiri amaonetsa ulemu kamba kokhala chete. Amalora nthawi ya Mulungu ndi danga kugwira ntchito mmiyoyo ya anthu ena. Nthawi zina, nthawi ndi danga limenelo zimasintha malo awo! Atsogoleri otumikira amazindikira mphamvu ya ulemu pokopa kudzera nkukhala chete.
Kukopa kwa chete kumaitana kuyang’anitsitsa. ‘Pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu. Kukhala chete kwa mkazi kudzapangitsa mwamuna kuwona! Kukhala chete kumapangitsa mwamuna kutembenuza mutu wake ndikuona zomwe mkazi wake akuchita, akuganiza kapena kulankhula mopanda mawu. Mawu amalimbikitsa anthu kuyang’ana pakamwa pathu kapena kuyang’ana kumbali; kukhala chete kumalimbikitsa kutembenuka ndi kuyang’anitsitsa. Atsogoleri amawumba njira asadalengeze njirayo. Amalora miyoyo yawo kulimbikitsa owatsatira kuyang’anitsitsa. Atsogoleri otumikira amachititsa kudzera mukukhala chete pomwe akulimbikitsa kuyang’anitsitsa.
Kukopa kwa chete kumasintha mitima. Kukhala chete kwa mkazi, kophatikizidwa ndi khalidwe labwino lowirikiza, kungathe ‘kukola’ mtima wa mwamuna. Mwamuna amayembezera kulimbana ndi kutsutsana kuchokera kwa iye. Akachita makani, mwamunayo ayankha munjira yomweyo ndipo mwachidziwikire adzapambana nkhondoyo! Koma mmalo mwake, iye amangopeza kuti kuli ‘chiyero ndi kuopa’ kwa chete. Kukhala cheteko ndi kosayembekezereka ndipo kuli ndi mphamvu zodabwitsa. Mapeto ake, mphamvu ya chete imamphwanya kutsutsa ndipo kenako amavomereza udindo wa mkazi wake. Atsogoleri otumikira amaphunzira, makamaka pomwe pali kusagwirizana, kuti kukhala chete kuli ndi mphamvu yokopa. Atsogoleri otumikira amavomereza kuti pomwe Mulungu angathe kugwiritsa ntchito mawu awo kusintha zinthu, angathenso kugwiritsa ntchito uchete wawo kusintha mtima wa wina. Atsogoleri otumikira nthawi zina amachititsa kudzera mukukhala chete ndipo amaona Mulungu akusintha mitima. Chachidziwikire, pali nyengo zambiri zomwe atsogoleri amafunsidwa kunena maganizo awo ndipo amakhala ndi mtsutso woyenera pa nkhaniyo. Koma palinso nthawi zomwe atsogoleri amachita bwino akatenga malangizo a Petro ndi kutsogolera mwa chete. Atsogoleri otumikira amalilira kwa Mulungu pofuna nzeru zofuna kudziwa nthawi yomwe angakope ndi mawu ndiponso pomwe angathe kukhala chete ndi njira yoyenera. Atsogoleri otumikira amaphunzira kuti utsogoleri wa chete umalankhula mofuula pokopa! Amapita pamwamba potseka pakamwa! |