|
Timoteo: Kuphunzila Kuphunzitsa
Gawo #360, October 1, 2025
Timoteo anaphunzira mwachangu kuti mbali yofunika ya utsogoleri ndi kupatsila kwa ena zomwe amadziwa ndi kukhulupilira. Anaphunzira kuphunzitsa. Lingalirani za malangizo otsatirawa ochoka kwa Paulo kupita kwa Timoteo:
2 Timoteo 2:24
Ndipo kapolo wa Ambuye sayenela kuchita ndeu, koma akhale oyenera, waulere pa onse, odziwa kuphunzitsa, woleza,
2 Timoteo 4:2
Lalikira mau ;chita nao panthawi yake;tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.
2 Timoteo 2:1-2
Ndipo iwe, mwana wanga, limbika mchisomo cha m'Khristu Yesu. Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupilika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.
1 Timoteo 6:2
Ndipo iwo okhala nawo Ambuye okhulupilira, usawapeputse, popeza ali abale ; koma makamaka awatumikire, popeza ali okhulupilira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze.
Timoteo anali ndi mphatso ya uphunzitsi ndipo anatumikila bwino pophunzitsa bwino. Atsogoleri onse, ngakhale omwe uphunzitsi si choyambilira cha mphatso zawo, angathe kuphunzila kuchokela kwa iye momwe angatumikilire bwino omwe amawatsogolera kudzela mukuphunzitsa kopambana.
Timoteo anaphunzira Kuphunzitsa pofotokoza cholinga chake
Timoteo poyambilira anafunika kuphunzila Kuphunzitsa chifukwa pa zifukwa zoyenera ndi mtima waubwino kwa omwe ankawatsogolera. Choncho, Paulo akupatsa malangizo Timoteo kuti aziunguze zolinga zake pophunzitsa. Atsogoleri ena amaphunzitsa ndicholinga chofuna kuwina mtsutso kapena kufuna kuonetsa kuti ndi olondola. Koma Timoteo anaphunzira kuti atsogoleri muutumiki safunika kukhala "amkwiyo.” Atsogoleri ena muutumiki amaphunzitsa ndi nkwiyo kwa omwe amadziwa mochepa kusiyana ndi momwe iwo amadziwira ndipo sakhala odekha kwa ophunzira. Timoteo anaphunzira kuti atsogoleri muutumiki ndi omwe ali "osakwiya" ndipo ali ndi "kudekha kwakukulu." Atsogoleri muutumiki amaika mitima yawo mumalo abwino asanatsegule milomo yawo kuti aphunzitse.
Timoteo anaphunzira Kuphunzitsa potsimikiza uthenga wake
Timoteo kenako anaphunzira kuganiza mokuya za zomwe chiphunzitso chake chinkanena. Anaphunzira kwa Paulo kuti akhale ndichidwi pa.” Zinthu zomwe unanva ine ndikunena. . . . izi ndi zinthu zomwe uzikaphunzitsa." Timoteo anaphunzira kuti si ulaliki uliwonse omwe umakhala ndi kufunika kofanana. Anaphunzira kuti aziganizila mosamala pa zomwe akufuna akaphunzitse. Atsogoleri ena amaphunzitsa zilizonse zomwe zili pamwamba pa malingaliro awo mu nthawi imeneyo. Koma atsogoleri muutumiki amalingalira mosamala pa zomwe chiphunzitso chawo chikunena ndipo motsata ndondomeko amagawa zomwe zili zofunika kwambili. Atsogoleri muutumiki amakhala ndi chindunji cha uthenga wao pa zinthu zomwe zili zofunika pa bungwe lawo, makamaka masomphenya, cholinga, ndi ngodya.
Timoteo anaphunzira Kuphunzitsa popanga njila zake zophunzitsira
Ndi cholinga chabwino ndi uthenga olondola, Timoteo anaphunzilanso momwe angagwilitsile njila zabwino ngati mtsogoleri. Anamunva Paulo akutsindika kuti akhale "okutha kuphunzitsa" ndi kuwaphunzitsa omwe amawatumikilira kuti"afike povomelezeka kuphunzitsa ena.” Timoteo anamvetsetsa kuti Kuphunzitsa ena bwino kumafunika kukula kopitilira mukuphunzila kuti udziwe ndi njila ziti zomwe zingagwilizane bwino ndi anthu ukuwaphunzitsawo. Atsogoleri ena amangoyelekeza kuti ndintchito ya omwe akuwaphunzitsa kuti azindilile okha zomwe akutanthauza ndi zomwe zikufunika kutsatidwa atamaliza kuphunzila. Koma atsogoleri muutumiki amalimbikila kugwilitsa ntchito njila zophunzitsila zimene zimapangitsa uthenga kukhala ogwilika bwino. Amaphunzira kuchokela mu kulakwitsa kwawo ndi kukonza njila zakaphunzitsidwe kawo ndi cholinga chotumikilabwino anthu omwe akuwaphunzitsa. Amaonetsetsa ndi kuphunzila kuchokela kwa ena omwe ali aukadaulo ophunzitsa momwe angapelekere uthenga mwaukadaulo. Ndipo amafunsa kuchokela kwa ena za momwe chiphunzitso chawo chinaliri ndicholinga chofuna kuti alimbikitse njira zawo za kaphunzitsidwe chifukwa amanvetsetsa kuti kuphunzitsa bwino ndiko kutumikira bwino.
Zoti tilingalire ndi kukambirana:
- Kodi ndingapititse bwanji patsogolo kuthekela kophunzitsa ena mumoyo wa ine mwini? Mumagawo atatu omwe taunikira(zolinga, uthenga wanga, ndi njira)Kodi ndili wamphamvu kwambili pati? Ofooketsetsa? Ndikaunika ndekha mtima wanga ndi cholinga chophunzitsa ena, kodi ndikupeza chani? Kodi ndimasamalira motani zomwe zili muchiphunzitso chomwe ndimaphunzitsa kwa ena? Kodi ndazindikila chani? Kodi ndinjila ziti zomwe ndingatsate kuti ndilimbikitse kuthekela kwanga kophunzitsa bwino?
- Lingalirani pa omwe mumawatsogolera. Kodi ndinjila ziti zomwe ndingatsate musabata ino zomwe zingawathandize kuti apeze okha njira zakuthekela Kuphunzitsa ena?
- Poonjezela kumavesi omwe tagwilitsa ntchito muphunziro limeneli, onani mavesi otsatirawa: 1 Timoteo 6: 2-5;2 Timoteo 1: 6, 13-14; ndi 2: 14. Kodi ndimfundo zoonjezela ziti zomwe mukupeza mumavesi amenewa za momwe Timoteo anaphunzilira kuphunzitsa?
Muphunziro limeneli takhala tikuona moyo wa Timoteo. Ngati simunaone kale iyi itha kukhala nthawi yabwino kuti muwelenge mabuku awiri a mbaibulo omwe ali ndi dzina limeneli, olembedwa kwa iye ndi Paulo. Pomwe mukuwelenga, lingalirani pa zomwe Timoteo anachita kuti akule ngati mtsogoleri ndi momwe zomwe anachitazo zingathandizile kukula kwa inu ngati mtsogoleri.
Muphunziro lotsatilari, tiona pa chomaliza cha utsogoleri wa Timoteo, momwe anaphunzilira kumenyankhondo! |