|
Timoteo: Kulumikizitsa Mibadwo
Gawo #359, September 17, 2025
Chimodzi mwa utsogoleri wamphamvu wa Timoteo chinali kuthekela kolumikizana ndi anthu kuchokela ku Mibadwomibadwo. Onani uphungu uwu kuchokela kwa Paulo:
1 Timoteo 5: 1-2
Mkulu usamudzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale;akazi aakulu ngati amai;akazi aang'ono ngati alongo, mkuyela mtima konse.
1 Timoteo 4: 12
Munthu asapeputse ubwana wako ;komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupilira, mmau, mmayendedwe, mchikondi, mchikhulupiliro, , mkuyelamtima
Monga mtsogoleri Timoteo anatsatira malangizo amene anaphunzira, ngakhale mtsogoleri wachichepele, momwe angalumikizilane ndi kutsogolera omwe anali aakulu ndi omwe anali aang'ono.
Timoteo analumikizitsa mibadwo polemekeza mwachikumbumtima
Pamene Paulo ankalankhula kwa Timoteo za momwe angamakhalile ndi mibadwo ina anagwilitsa ntchito chitsanzo cha banja. Anamuuza Timoteo kuti aziwatenga anthu akuluakulu ngati makolo ake, ndipo ang'onoang'ono ngati achemwali ndi achimwene. Mabanja abwino amalemekeza makolo ndi ulemu komanso chisamaliro chofewa kwa omwe ali achichepele. Mabanja abwino amaonetsa ulemu mwachimtima kwa mibadwo yosiyanasiyana.
Atsogoleri ena amakhala ndi chidwi pa ntchito yomwe ikufunika kuti igwilidwe koma osalabadila ndi kuganizila msinkhu wamunthu yemwe akugwila ntchitoyo. Amayembekezela zotuluka zofanana ndipo amamutenga aliyense mofanana. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kukhala ndi chikumbumtima cholemekeza ndi kuwaona ofunika omwe ali obadwa nthawi yosiyanasiyana. Amawamvetsela kuti apeze nzeru kuchokela kwa omwe ali okulilapo ndipo amadziwa zambiri. Amawatenga achichepele moleza pomwe ali kuphunzila ndi kukula.
Timoteo analumikizitsa mibadwo polankhula mosamala.
Paulo akumuuza Timoteo kuti, "Usadzudzule munthu wamkulu mwaukali, koma amudandaulire ngati atate. " Kudzudzula ndi chinthu chimodzi chovuta kwambili mu utsogoleri ndipo kuzichita izi ndi anthu omwe ali a mibadwo wina sizophweka ! Timoteo akuphunzila kulankhula mosamala poganizila za munthu wachikulire ngati tate wake ndi kulingalira za momwe angasovele vuto atakhala kuti ndi bambo ake.
Atsogoleri kawilikawili amadzudzula kapena kukonza vuto osalabadilako za munthu yemwe akulandila chidzudzuloyo. Amaziona okha kuti ndi mabwana ndipo amayembekeza kuti ena asinthe pomwe iwo abweletsa chidzudzulo posatengela kuti achipeleka motani. Koma atsogoleri muutumiki amakhala ndi chidwi pa munthuyo monga munthu olengedwa ndi okhala ndi zofuna zawo zofuna kulemekezedwa ndi kupatsidwa ulemu. Mosamala amakhala ndi kuziletsa pofuna kudzudzula poganizila msinkhu ndi zokhumba za munthu aliyense.
Timoteo analumikizitsa mibadwo pokonda kothelatu.
Paulo anabetchela mtsogoleri wachichepele Timoteo kuti akhale chitsanzo mumagawo ambiri kuphatikizapo chikondi. Kusiyana kwa mibadwo kumafunika kulimbika kwakukulu kuti afike pomvetsetsa ndi kuyamika. Mtima wachikondi ndi ofunika kwambili kuti kusiyana kumeneku kumikizidwe.
Atsogoleri ena amaona ngati chikondi ndi chinthu "chofewa" pa zofunika zautsogoleri amachitenga chopanda pake. Koma pa mtima pa atsogoleri muutumiki pali chisamaliro chenicheni kwa ena, kukhumba kofuna kuwaona akuchitabwino ndi kupitapatsogolo. Chifukwa choti amakonda, atsogoleri muutumiki amalakalaka kuwamvetsetsa ndi kuwayamikira omwe ali ochokela kumibadwo yosiyanasiyana, omwe ali achikulile ndi omwe ali chichepele. Amamvetsela ndi kuwafunsa mafunso kuti apeze kumvetsetsa kenako amaonetsetsa muutsogoleri wawo kuti akufikila onse omwe amawatsogolera. Pomwe akupanga utsogoleri wabwino amamanga magulu amphamvu, asakaniza mibadwo.
Zoti tilingalire ndi kukambirana:
- Kodi ndingafotokoze bwanji utsogoleri wanga kwa omwe ali achikulile? Achichepele? Kodi ndimaona zophweka kulumikizana ndi omwe ali achikulile kapena omwe ali achichepele? Chifukwa? Kodi ndingapange bwanji kulumikizana kwamphamvu ndi anthu omwe ali ochoka kumibadwo ina omwe ndimawatsogolera?
- Lingalirani pa omwe mumawatsogolera. Kodi ndingapange chani kuti ndiwalimbikitse kupanga kumvetsetsa kwamphamvu pakati pa kusakanikila kwa mibadwo?
- Poonjezela kumavesi omwe tagwilitsa ntchito muphunziro limeneli, onani mavesi otsatirawa: 2 Timoteo 2: 22-26 and 3: 2. Kodi ndi nfundo zoonjezela ziti zomwe mukupeza mumavesi amenewa za momwe Timoteo anamvetsetsela ndi kutsogolera pomwe panali mavuto apadelawa a kusiyana kwa mibadwo?
Kuti mupitilize kuphunzila pa mutu umenewu, ndikukulimbikitsani kwambili kuwelenga buku la Tim Elmore, A New Kind of Diversity, lomwe limakamba zambiri za kusiyana kwa mibadwo zomwe panopa zikugwilantchito ndi phindu lomwe mbadwo uliwonse ukubweletsa ku Hulu. |