Timoteo: Kukhazikitsa Maubwenzi Abwino
Gawo #358, Sept. 3, 2025
Taona kale zinthu zingapo zomwe zinathandiza Timoteo kuti akule mukuthekela kwake kwa utsogoleri. Anali ndinjala yophunzila, anapeleka dipo la utsogoleri, anaphunzira mau ndi momwe angaganizile ndi kulingalira. Timoteo anasiya zotchinga mbuyo ndi kuphunzila kudziletsa- yekha pomwe anakhala chitsanzo. Muphunziro ili tiona chinthu china chomwe chinathandiza kupanga Timoteo kuti akhale mtsogoleri wopambana-anakhazikitsa maubale amphamvu. Onani mavesi awa:
2 Timoteyo 3
2 Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero. 3 Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino, 4 opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu. 5 Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.
1 Timoteyo 1
2 Kwa Timoteyo mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro. Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu zikhale ndi iwe.
2 Timoteyo 4
21 Uyesetse kubwera kuno nthawi yozizira isanafike. Eubulo akupereka moni, ndiponso Pude, Lino, Klaudiya ndi abale onse nawonso akupereka moni.
Mavesi amenewa akuwonetsa kuti Timoteo anapambana pokhadzikitsa maubwenzi omwe anali athanzi ndi opindulitsa Kwa Iye ndi Kwa ena omwe anakhuzidwa. Atsogoleri muutumiki amafunafuna kuchita chimodzimodzi kuti akuze maubwenzi amphamvu.
Maubwenzi abwino a Timoteo anathela ku kusankha.
Paulo akumukumbutsa Timoteo kuti pali anthu ambiri omwe sakakhala abwenzi amphamvu. Akumuwuza Timoteo motsindika kuti " anthu amenewa uziwapewa. " Timoteo anaphunzira kusankha bwino abwenzi. Anamvetsetsa kuti zisankho zomwe amapanga mumaubwenzi ake akanatha kukhala olimbikitsa kapena owonela pansi utsogoleri wake.
Atsogoleri ambiri salingalira mosamala ku kusankha kwawo kwa abwenzi. Atha kusankha abwenzi potsamila pa ubwino omwe akuuona kapena pa momwe ubwenziwo ungawapindulire. Kapena atha kulola ubwenzi kungoyambika popanda kukhala ndi kulingalira kulikonse. Koma atsogoleri muutumiki amaganizira mozama za omwe amakhala nao nthawi zambiri. Pomwe akufunafuna kukonda ndi kutumikira aliyense, amasankha maubwenzi awo mwakufunakwawo ndi moganizilabwino.
Maubwenzi abwino a Timoteo ankafunika kuzipereka
Paulo sanakhalepo ndi ana obeleka yekha koma ankamutcha Timoteo "mwana weniweni. "Kodi Timoteo anayenela kukhala pa malo pokondedwapa ndi Paulo chifukwa chiyani? Anali ataonetsa kumvela kwake ndi kukhulipilika kwa Paulo kwa zaka, kuonetsela kuzipeleka kwake ku ubwenzi wawo. Pomwe analipila dipo la ubwenzi wabwino ndi Paulo, anaphunzira momwe angakhalile ndi maubwenzi abwino ndi ena.
Atsogoleri ena amafuna phindu la ubwenzi wabwino koma sakhala ofuna kuikiza nthawi, mphamvu ndi kuzipeleka komwe kumafunika. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti maubale abwino ndi odula koma amayenelana ndi kuikiza. Amaika chidwi chawo pa kukonda ndi kutumikira bwino ndi kuona kuzipeleka kwao kutalandira mphotho ya maubwenzi abwino.
Maubwenzi abwino a Timoteo anamasula kuyendelalimodzi
Pomwe Paulo anali mundende kudikila kuphedwa, analembela mzake okhulupilika Timoteo kumpatsa mau otsiliza osanzikana kuonetsela kuzama kwa ubwenzi wawo. Ndipo anapeleka moni Kwa omwe amakondana ndi Timoteo mozama. Patadutsa zaka za kusankha mosamala maubwenzi oyenera ndi kuikiza mozama mwa iwo, Timoteo -ndi anzake -anakolora mphotho ya kuyendelalimodzi kwenikweni, chinthu chimene aliyense amachilakalaka kuti achikwanilitse.
Atsogoleri ambiri amafika pamathelo a moyo wawo ndi kuzindikira modzidzimutsa kuti alibe ndithudi anzawo oyendanawo ulendo ozipeleka omwe azakhale nawo. Atsogoleri muutumiki, monga Timoteo, amasankha abwenzi awo mosamala, kusamalira maubwenzi amenewo mwabwino popeza umakhala ndi maubale athanzi potsatila pake.
Zoti tilingalire ndi kukambirana:
- Kodi ndingafotokoze motani "maubwenzi abwino" ndi "maubwenzi onyentchela?”
- Ndikamalingalira za maubwenzi omwe ndilinawo pano kodi ndine okhutila motani za thanzi la maubwenzi amenewa? Kodi ndi chiti, ngati chilipo, chomwe ndikuyenela kusintha?
- Kodi ndilimbitse ubwenzi umodzi uti mwezi uno ndipo ndiikize mwacholinga motani mu ubwenzi umenewu?
- Lingalirani pa omwe mumawatsogolera. Kodi ndichite chani kuti ndiwalimbikitse kuti apange maubwenzi abwino?
- Poonjezela mavesi omwe tinagwilitsa ntchito muphunziro lino, onani mavesi otsatirawa: 1 Timoteo 4: 6-7;5: 1-2, 21, 24-25; 2 Timoteo 1: 2, 15-18; ndi 4: 9-12. Kodi ndi nfundo zina zoonjezela ziti zomwe mukupeza kuchokela mumavesi amenewa zowonetsa momwe Timoteo anatipulira maubale abwino ndi zotsatira za machitidwe ake?
Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Timoteo ankakhalira ndi mibadwo yosiyanasiyana.
Mu mitu imeneyi takhala tikuona moyo wa Timoteo. Ndi nthawi yopambana yoti muwerenge mabuku awiri mu Baibulo omwe ali ndi dzina lake, lolembedwa kwa Iye ndi Paulo. Pomwe mukuwelenga, lingalirani zomwe Timoteo anachita kuti akule ngati mtsogoleri ndi momwe machitidwe ake akuthandizila ku kukula kwanu. |