Timoteo: Kusiya Chikwama Chakatundu Mbuyo
Gawo #355, July 23, 2025
Timoteo, monga tonse a ife, anakhala mtsogoleri pamodzi ndi zonse zokumana nazo mmoyo, zikumbutso ndi nyengo zosiyanasiyana. Pomwe zambiri mwa izo zinali zabwino ndi zopindulitsa; Zina sizinali zothandiza ndipo zikanatha kukhala zotchinga ku kuthekela kwake kwa utsogoleri. Mophiphiritsa titha kuyelekezela ku ziñthu zomwe sanathe kuzikonza, zokhumudwitsa, zolakwitsa, ndi mantha pa zomwe anadutsamo ngati " thumba lakatundu" lolemetsa lomwe limatikokela pansi. Timoteo anayenela kusiya wina wa katundu wake pambuyo kuti akhale mtsogoleri wapambana. Onani mavesi otsatirawa omwe titawaunike kuti tipeze chomwe chikanatha kukhala thumba lakatundu la Timoteo ndimomwe analisiila mbuyo:
Machitidwe a Atumwi 16
1 Paulo anafika ku Derbe ndi Lusitra, kumene kumakhala ophunzira wina dzina lake Timoteyo. Amayi ake anali Myuda wokhulupirira, koma abambo ake anali Mgriki. 1 Timoteyo 4
12 Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima
1 Akorinto 16
10 Ngati Timoteyo afike kwanuko, onetsetsani kuti pasakhale zina zomuchititsa mantha pamene ali pakati panu, pakuti iye akugwira ntchito ya Ambuye monga ine.
Timoteo anamasula chikwama cha katundu wa banja.
Timoteo anachokela ku banja lophatikizana chikhalidwe, chipembezo, ndi mtundu ochokela, amai ake anali Myuda ndi Mkhrisitu pomwe bambo ake anali Mgriki ndi osakhulupilira. Timoteo akuyenela kuti anavutika ndi kochokela kwake ndikumva kusayenela kugwira ntchito pakati pa a Yuda ndi kupezeka paliponse ndi Paulo, yemwe ndi Myuda weniweni. Nthawi yomweyonso anthu amitundu akanatha kumuona ngati wachikunja!Koma Timoteo anasiya zonsezi mbuyo ndipo anakhala mtsogoleri wamphamvu ndi Paulo ndipo Kwa amitundu anaitanidwa kuti atsogolere. Mbiri yabanja ndi chikhalidwe Zitha kukhala chikwama cha katundu kwa aliyense, potsogolera mozionela pansi kapenanso mozitamandila. Machitidwe a pabanja atha kuwumba momwe timapangila pothetsa mkangano ndi momwe timachitila ndi zokumvaimva mthupi, ndi zina zotero. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kuzindikira ndi kulemekeza komwe anachokela komanso kuthana ndi zinthu zimene zimafuna kuthetsa ndi cholinga choti atsogolere ena munjira yabwino.
Timoteo anamasula chikwama chakatundu wa zaka zake
Paulo anakumbutsa Timoteo kuti ngakhale anali wamng'ono, akanatha kukhala chitsanzo ndi kutsogolera bwino. Timoteo anali wamng'ono ndipo anayenela kugonjetsa zobetchela za mmalingaliro zokhudzana ndi kutsogolera anthu omwe anali achikulile kuposa Iye. Momwe zimakhalira ankayenela kumuonela pansi ndipo akanati wavomeleza kuti akhazikike mu chinyamata chake ndi zochita zachinyamata utsogoleri wake ukanakhala osatetezeka. Atsogoleri ena atha kulolera msinkhu wao wachichepele kuti ziwaletse kukula ndi kutsogolera bwino. Ena atha kukhala azaka zapakatikati ndi kuyang'ana mbuyo ndi kulakalaka masiku omwe anali ndimphamvu zambiri ndi unyamata. Kwaomwe ali okulilapo atha kuyesedwa kuti angokhala mtambasale osapitiliza kukula mukuthekela kwawo Kwa utsogoleri kapena kukhala ozikuza pa zomwe anachita. Palibe àngazisinthe zaka zawo koma atsogoleri muutumiki amamasula katundu wammalingaliro yemwe ndi kukhala ndi chidwi cha kukula kwawo ndikusankha kuika chidwi pa kutumikira ena munthawi yomwe ali.
Timoteo anamasula chikwama chakatundu wa umunthu.
Paulo anapeleka malangizo kwa omwe Timoteo ankafuna kuwayendela kuti awone kuti "analibe mantha"ndi Iwo kapena " kumukhazika mtima pansi.” Kumalo ena akumulimbikitsa Timoteo kuti asakhale ndi Mzimu wamantha Izi zikusonyeza ngati mwachilengedwe anali ndi umunthu wamantha ndi othela zinthu mumtima. Umunthu wake ukànatha kumulepheletsa kukhala mtsogoleri wamphamvu, koma Timoteo anaphunzira kuyenda mopyola zimenezo ndi kutsogolera bwino. Pomwe umunthu wa Timoteo ukanatha kumupanga kukhala wamantha kwambili koposa momwe zimayenela kukhalira, maumunthu ena akanatha kukhala oti ndi owonjeza ndi amphamvu mopyola muyezo. Atsogoleri ena amalora umunthu wao ulamulire utsogoleri wao koma atsogoleri muutumiki amagwira ntchito yotukula umunthu wao munjira zomwe zimawalora kutumikira mwapamwamba ku zosowa za omwe amawatsogolera.
Zoti tilingalire ndi kukambirana_
- Kodi ndi katundu uti yemwe amabwela ndi mbiri yapadela ya banja langa, zaka zanga, ndi umunthu wanga? (Mulembe ndandanda pa chilichonse). Kodi izi zikhudza motani utsogoleri wanga? Kodi chofunika kwambili ndichiti kwaine kuti ndiyambe kuchisiya mbuyo tsopanolino?
- Lingalirani pa omwe mumawatsogolera. Kodi mavuto omwe ndimawaona akukumana nawo amakhudzana ndi katundu yemwe anachika naye kumabanja awo, zaka, kapena umunthu? Kodi ndingachite chani kuti ndiwalimbikitse kuti azindikile ndi kusiya mbuyo akatundu awo? Kodi angaganize zowelenga lingaliro limeneli ndikukambilana nane za izo?
- Poonjezela mavesi omwe tinagwilitsa ntchito muphunziro lino, onani mavesi otsatirawa: I Timoteo 5: 23 ndi 2 Timoteo 2: 22. Kodi ndi nfundo zina ziti zoonjezela zomwe mukupeza kuchokela mumavesi amenewa owonetsa kuti Timoteo ayenela kuti anatenga katundu mchikwama mu utsogoleri wake?
Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Timoteo anaphunzilira kudziletsa -yekha.
Dziwani: Muphunziro ili tikuona moyo wa Timoteo. Ndi nthawi yamtengo wapatali yowerenga mabuku awiri mu Baibulo omwe ali ndi dzina lake, lolembedwa kwa Iye ndi Paulo. Pomwe mukuwelenga, lingalirani zomwe Timoteo anachita kuti akule ngati mtsogoleri ndi momwe machitidwe ake akuthandizila ku kukula kwanu.
|