Timoteo: Kuphunzila Kulingalira
Gawo #354, July 9, 2025
Timoteo anali munthu wachinyamata, okhala ndi chikhumbo chofuna kutumikira dziko pomwe analumikizana ndi tate wake munzimu, Paulo. Koma mkati mwanjila anaphunzira kuti utsogoleri si okhudzana ndi ntchito kokha. Inde utsogoleri umakhudzana ndi ntchito zomwe atsogoleri amagwira komanso mtima ndi zolinga zomwe zimakhala kunsi kwa ntchitozo. Koma utsogoleri umaphatikizananso ndi ubongo, kuganiza, kuunguza, ndi kulingalira. Izi ndi zinthu zomwe Timoteo akanaphunzira pa ulendo wa yekha. Taonani malangizo omwe Paulo anapeleka kwa Timoteo.
2 Timoteyo 2 7 Lingalira zimene ndikunenazi, pakuti Ambuye adzakuzindikiritsa zonsezi.
2 Timoteyo 4 5 Koma iwe, khala tcheru nthawi zonse, pirira mʼzovuta, gwira ntchito ya mlaliki, gwira ntchito zonse za utumiki wako.
Paulo akumuuza Timoteo kuti "lingalira" ndi kuti "khala tcheru.” Timoteo ankafunika kuti aphunzile kaganizidwe ngati mtsogoleri, kukhala ndi nthawi yophunzila kufunika kolingalira ndi kuganiza. Chitsanzo chimenechi chikuphunzitsa atsogoleri muutumiki kumvetsetsa mphamvu ndi mchitidwe wa kulingalira.
Kulingalira kumamasula kumvetsetsa Paulo akumuuza Timoteo kuti kulingalira kumatulutsa kumvetsetsa. Paulo akadatha kungomuuza chabe Timoteo matanthauzo, Koma ankafuna Timoteo kuti akule mukuthekela kolingalira ndi kuzipezela yekha matanthauzo! Kuthekela kolingalira kunkafunika kuti kuchitike kuti Timoteo apeze kumvetsetsa. Kulingalira kumamuchotsa mtsogoleri pa ntchito yoti igwilidwe ndipo kumalora kaonedwe kena ka zinthu. Kulingalira kumapeleka mpata kwa mtsogoleri kuti apeze kumvetsetsa komwe kumathandizila kuti atsogolere. Kumvetsetsaku kukhoza kukhala kufunika koti zinthu zisinthe momwe zimayendela kapena chindunji chooneka bwino pa zoyenera kuchitika poyambilira. Chitha kukhala chinthu chachikilu chozizindikilitsa -wekha pomwe mtsogoleri akulingalira pa zoti achite paokha ndinso momwe utsogoleri wawo umakhuzila ena. choti timvetsetsecho chitha kukhala ganizo latsopano lomwe limathandiza kuthana ndi vuto lozunguza mutu. Kumvetsetsa komwe kwapezekaku mwachidziwikile kumapindulira bungwe lonse ndipo munjira imeneyi kulingalira ndi imodzi mwa mphatso yaikulu yomwe mtsogoleri atha kupeleka kwa omwe amawatsogolera. Atsogoleri ambiri amatsogolera ndi kumvetsetsa kochepa! Ena amafunafuna chidziwitso kuchokela kumalo ambiri, mwina nkutheka kuchokela kunjira zabwino, komabe omwe ndi madulira ku mchitidwe wa kulingalira. Koma atsogoleri muutumiki amapeza chidziwitso pomwe atenganthawi yokhala padela ndi kulingalira. Saganiza kuti akutsogolera ngati sakuganiza!
Kulingalira kumabweletsa zotsatira za kukhazikika Paulo akumuuza Timoteo kuti "khala tcheru nthawi zonse. " Akumuuza Timoteo kuti akhale mtsogoleri okhazikika yemwe sakakhala omangothamangira ku njira zambiri nthawi imodzi kapena kusintha zochita chifukwa cha kanthu kochepa. Ankafunika kuti akhale olunjika mmutu mwake! Kulingalira kumabweletsa kukhazikika ku utsogoleri. Atsogoleri omwe saleka kulingalira kawirikawiri salakwitsa posintha zochita poganizilako za momwe zimakhudzila omwe amawatsogolera. Amaphunzila kuti kutsogolera kokha ndi kuchitapo kanthu kawirikawiri kumabala mtsutso!Koma atsogoleri muutumiki amayima ndi kulingalira, kenaka kutsogolera pamalo odekha ndi a bata.
Kulingalira kumafunika nthawi. Kulingalira kuli ndi maphindu akulu koma ndi machitidwe omwe amafuna nthawi. Kulingalira kumafunika kuyamba waima kaye, kusiya kaye mmene umachitila ndi kuganiza mozama ndi kuunguza. Kulingalira sikufunika kuthamangira kapena kungopanikiza pa zochitika za patsiku. Ichi ndi chobetchela cha atsogoleri omwe ali ndi zoti achite zambiri nthawi imodzi. Pali ntchito zopanikiza zomwe zimafunika kuti zigwiridwe, zolinga zomwe zikuyenela kukwanilitsidwa, anthu oti akaonedwe ndi malo oti apitidwe! Zikakhala motere ndi zovuta kuima ndi kulingalira. Zitha kuoneka ngati kutaya nthawi. Choncho, mchitidwe wa kulingalira, monga momwenso zochitika zina zokhudzana ndi kutsogolera, zizikhala zofuna iwe mwini ndi kuziika pamapulani a pakalendala.
Atsogoleri ambiri satenga nthawi yosiya ntchito kuti aganize ndi kulingalira kaye. Amapitilizabe ndi ntchito zomwe akugwira opanda ndawi yolingalira pa ntchitoyo. Koma atsogoleri muutumiki amanvetsetsa kuti phindu la kulingalira limaposa mtengo ndipo amamanga nthawi ya kulingalira machitidwe awo zautsogoleri.
Zoti tilingalire ndi kukambirana • Kodi ndingayambe bwanji mchitidwe wa kulingalira pa moyo wanga? Kodi ndili ndi nthawi mu tsiku, sabata, pa miyezi itatu, ndi pa chaka yoima kaye ndi kulingalira? Kodi ndingapititse bwanji patsogolo nthawi yanga yolingalira? • Lingalirani za omwe mumawatsogolera. Kodi ndingachite chani kuti ndiwalimbikitse kuti apange kuthekela kwao kwa kulingalira? Kodi ndiwaitanile kuti azilingalira monga Paulo anachita kwa Timoteo, kapena ndifulumize kwambili kuwauza zomwe ndasanthula? Kodi angakayankhe bwanji funso Ili? • Kodi ena atha kufotokoza utsogoleri wanga ngati " okhazikika " ndi " otsimikizika" ndipo izi zizikhudza bwanji utsogoleri wanga? • Poonjezela mavesi omwe tinagwilitsa ntchito muphunziro lino, onani mavesi otsatirawa: 1 Timoteo 4: 2, 15-16, 2 Timoteo 1: 13-14. Kodi ndi nfundo zina ziti zoonjezela zomwe mukupeza kuchokela mumavesi amenewa za momwe Timoteo anaphunzilira kukhala olingalira momwe Paulo anamulangizila?
(Muphunziro lino tikuona za moyo wa Timoteo. Ngati simunawelengepo kale, iyi ndinthawi yapambana yoti muwerenge mabuku awiri mu Baibulo omwe ali ndi dzina lake, lolembedwa kwa Iye ndi Paulo. Pamene mukuwelenga, lingalirani pa zomwe Timoteo anachita kuti akule ngati mtsogoleri ndi momwe machitidwe ake akuthandizila ku kukula kwanu. )
Muphunziro lotsatirali, tiona zinthu zomwe Timoteo anaphunzilira kuzisiya pambuyo. |