Timoteo: Kuphunzila Mau
Gawo #353, June 25, 2025
Chimodzi mwa zinthu zimene Timoteo ankasowekela kuti aphunzile ngati mtsogoleri wampingo chinali kumvetsetsa, kugwilitsa ntchito ndi kuphunzitsa malemba. Ngati otsatira wa Yesu, ili linali buku lofunika la moyo ndi utsogoleri. Onani mau amatamando ochoka Kwa Paulo: 2 Timoteyo 3 15 Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu. 16 Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo 2 Timoteyo 2 15 Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola.
Titha kumva mau a Paulo ngati malangizo kwa ife ndipo ndichoncho ndithu. Koma kuseli kwa malangizo ake Paulo akuonetsa zomwe Timoteo anachita kwa nthawi ya moyo wake pa Malemba a Chiyuda anthawi yakale.
Timoteo anaphunzilira kudziwa Mau. Paulo anamukumbutsa Timoteo kuti "kuyambira uli wamng'ono wakhala ukudziwa Malemba Oyera. . . " Paulo anaona chikhalidwe chomwe Timoteo ankakhala kwa zaka. Popanda kutailila kolikokela kumbali kwa shelefu buku kunyumba kwake, Timoteo anaikiza nthawi yophunzila Mau. Ankatha kutenga nthawi yopita penapake, kumvetsela, kuwerenga, kuloweza ndi kuganizira tanthauzo la bukuli. Akuyenela kuti ankakambirana ndi aphunzitsi ake matanthauzo ndi kalalikidwe ka ndime zakale. Mumau anaonamo miyoyo ya atsogoleri ochitabwino ndi osachitabwino. Anaphunzira kuti atsogoleri ena amaika chidwi pa Iwo okha pomwe ena amaika chidwi pa omwe amawatsogolera. Pamene anali kuphunzila kudziwa Mau makhalidwe ake, kuganiza kwake, ndi zochita zake zautsogoleri anali pang'ono pang'ono akuumbika. Utsogoleri wake unazikika mu zenizeni zoposa Iye mwini. Atsogoleri ena sapeleka danga lakulingalira mosamala mtundu wa utsogoleri oyenera kuutsatira. Mmalo mwake, amafunafuna kuchita zomwe zikuoneka ngati nzabwino komanso zomwe zikupeleka chiyembekezo chotulutsa zotsatira zomwe amakhumba. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira kuti zomwe amawerenga, kupanga sitade, ndi kulingalira zimaumba kaganizidwe ndi zochita zao. Amasakasaka choonadi cha Mau ngati maziko a ulendo wao wa utsogoleri.
Timoteo anaphunzilira kukhala molingana ndi Mau. Paulo anazindikilanso kuti malemba "amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa. ." ndipo ndi othandiza "pophunzitsa za chilungamo." Timoteo sanangophunzira kudziwa Mau; anaphunzilira kuchita zomwe anali kuphunzila. Anasamutsa kudziwa kuchokela mmutu mwake kupititsa mmanja ake, kukhala chimene anaphunzira. Anazindikira kuti asanauze ena kuti angatsogolere bwanji, amayenela kukhala wachitsanzo pa zomwe ankafuna kuti Iwo achite. Atsogoleri ena amafuna kudziwa ndi cholinga chongoti adziwe basi komanso kuti ena akhutitsidwe nawo. Koma atsogoleri muutumiki amafunafuna chidziwitso chomwe chimaumba zochita zawo. Amaonetsa kaye njira asanaphunzitse njirayo.
Timoteo anaphunzira kuphunzitsa Mau Paulo sanali okhutitsidwa kuti Timoteo adziwe mau basi nkuthela pompo, ankafuna kuona kuchulukitsidwa! Kotero, anamuuza Timoteo kuti Mau "ndi othandiza pophunzitsa. . ." Timoteo amafunika kugwilitsa ntchito moyo wake ndi utsogoleri wake kuti adzutse atsogoleri ena kugawana nao zoonadi zomwe anaphunzira ndi kuzichita. Pomwe atsogoleri ena amakhala ndi chidwi pa kukula kwa iwo okha ndi kutukuka kwa Iwo okha, atsogoleri muutumiki nthawi zonse amafuna ena oti awatukule. Amaika moyo wao posiyila atsogoleri achichepele zomwe aphunzila ngati momwe Paulo anachitira ndi Timoteo. Atsogoleri muutumiki amawumba miyoyo ya ena pomwe akuphunzitsa njira Ina yakakhalidwe. Pomwe izi zikuchitika mwabwino, utsogoleri umayenda bwino ndi m'badwo uliwonse!
- Zoti tilingalire ndi kukambirana
Kodi ndingachite mochuluka bwanji kuti ndione Mau ngati gwelo loyambilira la maphunziro anga a utsogoleri? Kodi ndikutenga nthawi yoti ndiwadziwe bwino? Kodi ndimaganizira mozama zomwe malangizo, nkhani ndi zitsanzo zikundiphunzitsa pa mbali ya utsogoleri?
- Lingalirani pa omwe mumawatsogolera. Kodi ndingachite chani kuti ndiwalimbikitse kuti azigwilitsa ntchito Mau ngati gwelo la kukula ndi kukhwima kwao? Ngati ndikutsogolera anthu omwe sagawana chikhulupiliro changa, kodi ndingawalozele bwanji ku gwero limeneli popanda kuutsa mkwiyo?
- Kodi nditha kunena molimbamtima kuti moyo wanga ndi wachitsanzo Kwa ena kuti awutsatire? Ngati sichoncho, kodi ndikufunika kusintha pati kuti ndizichita Mau?
Kodi ndimunjira ziti zomwe ndikuphunzitsa atsogoleri achichepele modekha pa momwe angakhalire ndi kutsogolera? Kodi ndingachite bwanji ichi mwanjira yopambana?
- Pongoonjezela pa mavesi omwe tinagwilitsa ntchito muphunziro lino, onaninso otsatirawa: 1 Timoteo 4: 12, 15-16; 2 Timoteo 2: 25-26; 4: 2 Kodi ndi nfundo zina ziti zoonjezela zomwe mukupeza kuchokela mumavesi amenewa za momwe Timoteo anaphunzilira Mau?
Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Timoteo anaphunzilira kuganiza ndi kulingalira.
Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo, |