Timoteo: Kutsimikizila Maitanidwe
Gawo #352, May 28, 2025
Timoteo anali ndi mphatso ndi maitanidwe ku ntchito za utsogoleri omwe anatumikila, makamaka mu utsogoleri wake wa mpingo wa ku Efisas. Koma kunali zaka zambiri za kukula ndi kukhwima ndi kugwila ntchito zomwe zinapyola ntchito yomwe anatumidwa ndipo munthawi imeneyi Timoteo ankatsimikizila za maitanidwe ake. Onani malangizo omwe Paulo anapeleka kwa Timoteo:
1 Timoteyo 4 14 Usanyozere mphatso yako yomwe inapatsidwa kwa iwe kudzera mʼmawu auneneri pamene gulu la akulu ampingo linakusanjika manja. 1 Timoteyo 1 18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa langizo ili molingana ndi maulosi amene aneneri ananena za iwe. Pamene ukumbukira mawu amenewa udzatha kumenya bwino nkhondo 2 Timoteyo 1 6 Nʼchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti upemerere monga amachitira moto, mphatso imene Mulungu anakupatsa nditakusanjika manja.
Mundime zimenezi Paulo anamulimbikitsa Timoteo kuti amvetsetse bwino za maitanidwe omwe analandila kuti akhale mtsogoleri. Pali ndondomeko zingapo zomwe Timoteo anatsata kuti atsimikizile za maitanidwe ake zomwe zikupeleka chitsanzo kwa atsogoleri onse muutumiki.
Timoteo anazindikira maitanidwe a kutsogolera Paulo akukumbitsa Timoteo kuti panali nthawi yomwe thupi la akulu ampingo linamusanjika manja ndi mwauneneli linazindikila maitanidwe ndi mphatso zomwe zinali mwa Timoteo. Sitingathe kudziwa kwenikweni kuti izi zinachitika liti koma poti patsogolo pake Paulo akumukumbutsa Timoteo kuti akumbukile maitanidwe ake, zikuonetsa kuti inali nthawi yoyambilira ya ulendo wake wa utsogoleri, kapena pomwe anasiya nyumba yake kuti ayende ndi Paulo. Munjira iliyonse, pomwe izi zinachitika zinali chiyambi cha kuzindikila mphatso ndi maitanidwe ake. Ngati atsogoleri ambiri Timoteo samatha kuona kuthekela kwake ndipo ankafuna ena kuti alankhule mmoyo wake kuti atsimikizile za mphatso yake. Atsogoleri muutumiki amachilandila ichi ngati mbali ya ulendo wawo wa utsogoleri ndipo amafunanso kuchita chimodzimodzi kwa ena omwe awazungulira.
Timoteo analimbikitsa maitanidwe a kutsogolera Paulo analimbikitsa Timoteo kuti "Asanyozele" ndi "kupatsa moto "mphatso yomwe inali mwaiye. Ichi ndi kumuzindikilitsa kuti ayang'anile ndi kukuza chomwe chazindikilika. Padzakhala masitepe ambiri ophunzila ndi kukula omwe anali ofunika Timoteo aditsemo asanakonzekele kutsogolera mpingo wa ku Efisas ndipo tizaona zambiri za izi kutsogolo kwa maphunzirowa. Kwanthawi ino, tichitenge ichi kuti mphatso mwa Timoteo zinapatsidwa motsimikizidwa bwino koma zinkafunikanso kuti zilimbikitsidwe. Ankafunika kuti aphunzile kutsogolera monga mwa mauneneli omwe ananenedwa. Ankapanga izi komanso osalephela amatha nthawi zina kulakwitsa koma anapitilizabe kuphunzila ndi kukula. Timoteo amathanso kuphunzila kuvomeleza kuti sanali ndi mphatso mumbalizonse yekha, anali ndi mbali yomwe Iye anali bwino koma sakanakhala okhozabwino mbali zonse za utsogoleri. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti anaitanidwa ndi kupatsidwa mphamvu kuti atsogolere komanso munthawi yomweyo amazindikira mphatso zosiyanasiyana zomwe zimafunika zomwe zili mwa owazungulira. "Amapatsamoto" mphatso zawo pamenenso akuphunzira kutsogolera bwino.
Timoteo anakumbukira maitanidwe a kutsogolera Paulo akumukumbutsa Timoteo kuti " akumbukile" mauneneli omwe ananenera pa iye zaka zoyambilira. Kodi cholinga cha chikumbutsochi chinali chani? Zikhoza kutheka kuti Timoteo ankadutsa munyengo zowawa pa ulendo wake wa utsogoleri ndipo ankafunika chilimbikitso kapena ankazimva kuchitabwino kwambili komwe kumapangitsa kuiwala cholinga chimene ali muutumiki. Timoteo, ngati atsogoleri onse muutumiki, akufunika kuti aleke ndi kulingalira kuti akuchitilanji zomwe akuchitazo. Akufunika kuti akumbukile maitanidwe awo omwe ndikutumikira ena ndi mphatso zawo za utsogoleri. Paulo ankafuna kuti Timoteo atsale ku Ephesus. . . . kapena kunali zovuta mpaka Timoteo akanva ngati angozisiya. Tikufunika kukumbukira cholinga cha kutumikira kwathu. Chilimbikitso chimafunika.
Zoti tilingalire ndi kukambirana
- Kodi ndi liti lomwe ndinazindikira kuti ndinali ndi mphatso ndi kuitanidwa ku utsogoleri? Panali ena omwe anatsimikizira ichi mwa ine, ndipo ngati ndichoncho, ndinaonetsala chiamiko changa kwa iwo chifukwa cha mphatso imeneyi?
- Kodi ndi ndani ondizungulira yemwe ali ndi mphatso ya utsogoleri yomwe ndingaizindikile ndi kuitsimikizira? Ndingapange motani ndipo liti lomwe ndizachite izi?
- Kodi mphamvu zanga za utsogoleri ndiziti ndipo pakadali pano ndikuchita chani kuti ndizikuze?
- Kodi ndi mokuya motani momwe ndavoleza kuti sindichitabwino mumbali zonse za utsogoleri koma nditha kubweletsa gulu londizungulira kuti lindithandizile zofooka zanga? Kodi zimenezi zikukhudza bwanji utsogoleri wanga?
- Lingalirani pa omwe mumawatsogolera. Kodi ndingachite chani kuti ndiwalimbikitse kuti atsimikizile za maitanidwe Iwo eni?
Poonjezela mavesi omwe tinagwilitsa ntchito muphunziro limeneli, onani mavesi otsatirawa: 1 Timoteo 4: 15-16;6: 11-12, 20; ndi 2 Timoteo 2: 14. Kodi ndi mfundo zoonjezela ziti zomwe mukupeza zokhudzana ndi momwe Timoteo ankatsimikizila za maitanidwe ake?
Muphunziro lino tikuona za moyo wa Timoteo. Ndinthawi yopambana kuwerenga mabuku awiri mu Baibulo omwe ali ndi dzina lake, lolembedwa kwa Iye ndi Paulo. Pomwe mukuwelenga, lingalirani zomwe Timoteo anachita kuti akule ngati mtsogoleri ndipo momwe zomwe ankachita zikuthandizila ku kukula kwanu.
Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Timoteo anaphunzilira Mau.
|