Timoteo: Njala yofuna Kuphunzila
Gawo #350, April 30, 2025
Muphunziro lapitali tidaona za momwe Paulo anachitila ngati mtsogoleri muutumiki kuti kasankhidwe kake ka utsogoleri kakhale kapamwamba. Cholinga chathu choyambilira chinali pa zomwe Paulo adachita kuti amuthandizile Timoteo kukula muutsogoleri. Mumaphunziro tayambawa tiika chidwi chathu pa Timoteo ndi kuona zomwe anachita zomwe zinathandizila muutsogoleri wake. Ngakhale tilibe mau ena aliwonse osungidwa a Timoteo, moyo wake ndi chitsanzo kwa ife pophunzila momwe tingakulile ndi kupititsila patsogolo utsogoleri wathu ndinso momwe tingalimbikitsile mtima ndi machitachita a Timoteo mwa omwe timawatsogolera. Onani mau a Paulo kwa Iye okhudzana ndi kuphunzila:
2 Timoteyo 3
14 Koma iwe pitiriza zimene waziphunzira ndi kuzivomereza, chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa zimenezi. 15 Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu.
Pamtima pa ulendo wa utsogoleri wa Timoteo panali chapamtima cha moyowake nthawi ya moyo wake wonse chomwe ndi kuphunzila ndinso kukula. Moyo wake ndi chitsanzo kwa atsogoleri onse muutumiki.
Timoteo anazindikira kuika kuphunzila kukhala choyambilira
Timoteo anali ali wa chaka chimodzi ngati si ziwiri mu chikhulupiliro chake chatsopano pomwe Paulo anamupempha kuti akhale mmodzi wa mugulu lake. Anali akadali wang'ono komanso anali oti sanazolowele, ndipo anazindikira kuti anali ndi zambiri zofuna kuphunzila. Anakhala moyo wina watsopano yemwe anali kale mtsogoleri wamphamvu. Koma Timoteo anazindikira kuti maphunziro a Paulo akadakhala ndi phindu ngati anali ophunzira olakalaka.
Atsogoleri ena amakhala okhutitsidwa kuti aphunzile mokwana kuti ntchito igwiridwe, koma sakhala ndi njala yofuna kuphunzilabe. Amaona kuti kuphunzila ndi chida choti akwanilitsile ntchito kapena afikile chinthu choikika chomwe chilipo. Koma atsogoleri muutumiki amaona kufunikira koika maphunziro kukhala choyambilira ndi kuyamba kutsatira kukula -kwamoyo wao onse ndicholinga choti akhudze ndi kutumikira anthu ambiri. Amazindikira kuti kukula kwawo kuzakhudzanso kukula kwa omwe awazungulira. Mtsogoleri muutumiki amadziwa kuti kupanda kukula ndi kupita patsogolo Iwo eni, sangathe kukuza bwino ndi kukweza ena.
Timoteo anavomeleza kudutsa ndondomeko zakuphinzira
Timoteo anavomeleza chenicheni choti kuphunzila kwake kukhala kodutsa mundondomeko. Izi zinayambila posankha anthu abwino ndi oyenela kuphunzilapo..” . . . chifukwa umadziwa iwo kuchokela kwa omwe anaphunzitsa chinthucho. "Timothy ankaonetsetsa moyo wa Paulo mosamala, komanso anaphunzila zambiri kuchokela kwa agogo ake amuna ndi akazi. (Onani 2 Timoteo 1: 5). Timoteo anazindikira kuti ndondomeko yakuphunzila ikhala yopitilira.” . . . pitiliza mu zomwe waphunzila. . . "Timoteo tsopano anali mtsogoleri wokhathamila bwino pa iye yekha. Koma ankafuna kupitilizabe kukula. Anazindikira kuti izi ndi zotenga nthawi yamoyo wake wonse. Atsogoleri ena amayesetsa kutenga njila zamadulira mu ndondomeko ya nthawi yophunzira ndipo amalakalaka kukula pomwe akumana ndi chinthu chomwe sangathe kuchigonjetsa. Koma atsogoleri muutumiki amasankha kukula mopitilira podziwa kuti chotsatila chake nchopambana.
Timoteo anatengela chotsatila cha kuphunzila.
Pomwe Paulo ankaonetsetsa moyo wa Timoteo pa nthawi iyi, anazindikira kuti Timoteo anatengela kutsimikizika kozama kuchokela mu kuphunzila kwake..” . . iwe. . . wakhala pofika potsimikizika. . . "Timoteo anayamba ulendo wake mwachikaiko ndipo alibe ukadaulo., koma podutsa panthawi, pomwe anali kuphunzila ndi kukula, anayamba kuzidalira. Kuzidalira kumeneku sikunali mwano, koma kutsimikizika kokhazikika kuti anali okonzeka ndipo othekela kutsogolera ena. Kutsimikizika uku kunakula kuchokela mu ulendo okuphunzila mopitilira omwe anatsatira moyo wake onse.
Atsogoleri ena satengera kuzidalira mumphatso zawo, maitanidwe ndi kuthekela ndipo samakwanitsa kutumikira ena zenizeni. Popanda kuzidalira amakhala ndiphamvu ndi kugwilitsa ntchito udindo ndizolinga zaiwoeni. Koma atsogoleri muutumiki amatengela kuzidalira kudzela mu kuphunzila kwa moyo onse ndipo amapeleka mphamvu ndi ulamuliro kwa omwe amawatumikira.
Zoti tilingalire ndi kukambirana:
- Kodi ndili ndi njala yotani ine ngati mtsogoleri? Kodi njala yanga ikuchuluka kapena kuchepelachepela pa kudutsa kwa nthawi? Kodi izi zikukhudza motani kuthekela kwanga ngati mtsogoleri?
- Kodi ndingakulitse bwanji njala yofuna kuphunzila mu moyo wanga? Kodi ndizitsatila ndondomeko zoziletsa ziti ndi ziti pa tsiku kapena pa sabata zomwe zingandithandizile kuti ndizikulabe? Kodi ndikuyang'ana pa ndani mkati mwanga ngati munthu yemwe amandithandiza kukula?
- Lingalirani omwe mumawatsogolera. Kodi ndingachite chani kuti ndiwalimbikitse ndi kukulitsa njala mwa Iwo yophunzira? Kodi ndikupangapo mbali yanga kuti ndipange kuphunzila kukhala kotheka ndi koyembekezeka kwa Iwo?
- Poonjezela pa mavesi omwe tagwilitsa ntchito muphunziro lino, onani mavesi otsatirawa kuchokela ku moyo wa Timoteo: 1 Timoteo 4: 12, 15-16; 1 Timoteo 6: 20-21; ndi 2 Timoteo 1: 6, 13-14. Kodi ndi zinthu ziti zoonjezela zomwe mukupeza kuchokela mumavesi amenewa omwe akuonetsa kuti Timoteo anali ndi njala yofuna kuphunzila ndi kukula?
- Muphuro iri tikuona za moyo wa Timoteo. Ndinthawi yabwino yoti muwelenge mabuku awiri a mu Baibulo omwe ndi a dzina lake, omwe Paulo anamulembela. Pomwe mukuwelenga, lingalirani pa zomwe Timoteo anachita kuti akule ngati mtsogoleri ndipo momwe machitidwe ake akukhudzila kakulidwe ka iwe mwini?
|