Kusankha Kwa Utsogoleri Kwa Paulo: Akondeni

Gawo #349, April 16, 2025

Taona momwe Paulo anakuzila Timoteo,  mmodzi mwa atsogoleri oyamba kumene a mugulu limeneli. Panali machitidwe ambiri adala a mtsogoleri muutumiki omwe Paulo anatsatira ndi Timoteo ndipo njira iliyonse ndiyopeleka malangizo. Koma muphunziro lomalizali tichoka ku zochitika zapadeladela kupita ku mtima omwe unawumba zochitika za Paulo: chikondi chake pa omwe amawatumikira.  

1 Akorinto 4

17 Chifukwa cha ichi ndikutumiza kwa inu Timoteyo,  mwana wanga amene ndimamukonda,  amene ndi wokhulupirika mwa Ambuye.  Adzakukumbutsani inuyo za moyo wanga mwa Khristu Yesu,  umene ukugwirizana ndi zimene ndimaphunzitsa paliponse mu mpingo uliwonse.  

Paulo akulankhula za Timoteo ngati "mwana wanga yemwe ndimamukonda. . . ." Chikondi chitha kuoneka ngati ka ukadaulo kapansipansi ka utsogoleri koma chikondi ndichamphamvu ndipo chinali maziko a zonse zimene Paulo anachita.  Chikondi Cha Paulo pa Timoteo chinayambira pomwe anamusankha Timothy ndipo zinaonetseledwa muzonse zomwe anachita kuti amutukule.  Chifukwa anamukonda Timoteo anamuonetsela njira,  anampatsa mphamvu, anamukulitsa,  anamumasula, ankamutsatira ndi kumulimbikitsa. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kuchokela kwa Paulo zomwe zimafunika kuti akhale ndi mtima wa chikondi pa omwe amawatumikira.  

Kukonda atsogoleri ena kumafunika kusazikundikira 

Paulo akulankhula za Timoteo munjira yomwe ikumukweza pamaso pa  omwe amawelenga uthenga wake. Timoteo "mwana wanga. . . .  yemwe ali okhulupilika. . . . azakukumbutsani. . . " Paulo anali ndi cholinga pa Timoteo, osati pa iyemwini.  Ankamutuma Timoteo kuti akamuimilire pa ntchito yovuta.  Moyo osazikundikirawu ndi chapamtima penipeni pa utsogoleri muutumiki. Atsogoleri ena safuna ziwadutse ndipo zonse zomwe amanena ndikuchita zimalozela ku  kuzipanga okha kuti aoneke  abwino.  Koma atsogoleri muutumiki amakhala ndi chidwi pa omwe amawatumikira.  Amagwilitsa ntchito mphamvu zao za utsogoleri kuti amange ena ndi kuvomeleza komanso kudalitsa mphatso zomwe zili mwamtsogoleri yemwe akuphuka kumene. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti utsogoleri sikuti ndi zonse okha,  ndi za omwe amawatumikira. Atsogoleri muutumiki amakonda chifukwa ndiosazikundikira.  

Kukonda atsogoleri ena kumafunika kuzisiya

Paulo anali ofuna kupeleka zina mwa mphamvu zake ndi ulamuliro pomwe anatumiza kalata yake kudzela kwa Timoteo kupita ku mpingo wa ku Korinto. " Ndakutumizirani Timoteo. . . " Paulo anapeleka ulamuliro wake kwa mtsogoleri wake wachichepele ndipo anamudalira kuti atumikira bwino.  Unali ukadziotche omwe unamuika Paulo munyengo yovuta kwambili,  koma anamukonda kwambili Timoteo ndikumpatsako mphamvu.  Atsogoleri ena amakhala ndi mantha kuti apeleke ulamuliro.  Koma atsogoleri muutumiki amapereka mphamvu ndi ulamuliro kuti awone ena atakwezedwa. Atsogoleri muutumiki amakonda kudzela mu kuzisiya.  

Kukonda atsogoleri ena kumafunika kusaopyezedwa.

Paulo anakwanitsa kumukonda Timoteo kuchokela ku kusakhala ndi mantha alionse mu utsogoleri wake. Samaophyezedwa ndi mphatso za Timoteo komanso kuthekela kwake.  Anali ndi kutsimikiza konse pokweza mphatso za Timoteo ndi maitanidwe ake omwe.  Kusakhala ndi mantha kwa Paulo kunazikika mu " moyowake mwa Khristu Yesu. " Utsogoleri wake unagwirizitsidwa molimba mu chinachake chozama kuposa udindo wake kapena mphatso yake, unali mu ubale wake ndi Yesu.  Atsogoleri ena amaopa kuti atsogoleri omwe akuphuka kumene azakhala abwino kuposa momwe aliri.  Amaona mphatso za ena ngati chiophyezo kwa Iwo.  Koma atsogoleri muutumiki amadziwa kuti iwo ndindani.  Amakhala mosatekeseka mu mphatso zawo ndi maitanidwe awo. Kuchokela ku kupanda mantha kumeneko atha kudalitsa ndi kuvomeleza mphatso za ena, ngakhale mtsogoleri oyamba kumeneyo atakhala wabwino kuposa iwowo. Atsogoleri muutumiki amamvetsetsa kuti kukhala ndi chidwi pa ena sikuzimitsa chomwe ali.  Mwalomwake atsogoleri muutumiki amakhala opandankhawa kutumiza  ndi kupatsa mphamvu ena.  Atsogoleri muutumiki amakonda chifukwa ndi osaopa.

 Atsogoleri muutumiki amapanga zithu zambiri kuti atukule  omwe ali nao pafupi.  Koma  pamtima pa zonse ndi  chikondi cha pa omwe amawatumikira.  

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Tikatenga sikelo ya 1 mpaka 10 Kodi utsogoleri wanga ndiowumbidwa ndi chikondi? Kodi chimenechi chakhudza utsogoleri wanga motani?
  • Kodi utsogoleri wanga choyambilira uli ndi chidwi pa ine mwini kapena pa omwe ndimawatsogolera? Kodi musabata yathayi zomwe ndachita ndiziti zowonetsela izi?
  • Kodi ndimapeleka ulamuliro kwa ena mophweka motani? Kodi chitsanzo chomwe chilipo ndichiti mu utsogoleri wanga chowonetsela kufuna kwanga(Kapena kusowa kwa kufuna kwanga)kotula mphamvu ndi ulamuliro kwa ena? Kodi ndipange ukadziotche pati powamasula omwe ndimawatumikira?
  • Kodi zochita zanga ngati mtsogoleri zimaonetsela kupanda mantha,  kapena zimaonetsela mantha olandidwa utsogoleri? Kodi musabatayi ndipangepo chani kuti utsogoleri wanga ugwilizitsidwe mungaka ya mu maziko ozama.

Muphunziro lotsatirali, Tiyamba phunziro poona moyo wa Timoteo, mbali Ina ya Kusankha Kwa Utsogoleri Kwa Paulo.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Kuti mulandile izi pa WhatsApp dinani apa

 

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Leaders Serve and Jon Byler. Copyright, 2025

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online