Kusankha Kwa Utsogoleri Kwa Paulo:  Alimbikitseni

Gawo #348, April 2, 2025

Taona njira zingapo zomwe Paulo anapanga kuti apititse patsogolo kasankhidwe ka utsogoleri wake pokhazikitsa ndondomeko zomwe zinkapangitsa kusintha anthu kuchoka pa mulingo wina kupita pa mulingo wina wa utsogoleri mu kuthekela kwawo. Njira imodzi yomwe Paulo ankatsatila mosalekeza inali yowalimbikitsa iwo amene Iye ankafuna kuti akule muutsogoleri. Onani zitsanzo izi kuchokela mu kulankhulana kwake ndi Timoteo:

2 Timoteyo 1

6 Nʼchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti upemerere monga amachitira moto,  mphatso imene Mulungu anakupatsa nditakusanjika manja.

1 Timoteyo 4

12 Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata,  koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe,  pa makhalidwe,  pa chikondi,  pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.

Afilipi 2

19 Ngati Ambuye Yesu alola, ndikukhulupirira kuti ndidzamutuma Timoteyo msanga kwanuko,  kuti mwina ndingadzasangalale ndikadzamva za moyo wanu.

20 Ndilibenso wina monga iyeyu amene ali ndi chidwi chenicheni pa za moyo wanu.

21 Pakuti aliyense amangofuna zokomera iye yekha osati zokomera Yesu Khristu.

22 Koma inu mukudziwa kuti Timoteyo wadzionetsa yekha,  chifukwa watumikira ndi ine pa ntchito ya Uthenga Wabwino monga mwana ndi abambo ake.

1 Atesalonika 3

2 Tinatuma Timoteyo,  mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu,  kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu,  

Paulo ankalimbikitsa Timoteo ndi mau kumbali ngakhalenso pagulu kutsimikizila za mphatso zake ndi maitanidwe ake. Anali ndi kumvetsetsa koti chilimbikitso chimabweletsa zotsatila za atsogoleri abwino ndipo chitsanzo chake chikuonetsa atsogoleri muutumiki kuti chilimbikitso chimabala.

Kulimbikitsa atsogoleri kumatulutsa kukula mwa ena

Paulo analimbikitsa Timoteo kuti akule ndi kupita patsogolo, cholinga "chompatsa moto" pa mphatso zomwe anali nazo. Tangoganizani kuti izi zinathandiza motani kwa Timoteo ponva kuchokela Kwa Paulo kuti anali ndi mphatso mkati mwake.  Mtsogoleri yemwe akuphuka kumene kawirikawiri saganizako za kuthekela kwa utsogoleri komwe alinako ndipo zimatengela wina wake kuti atchule za mphatso zomwe alinazo.  Pomwe mtsogoleri okhazikika anena za mphatso zomwe mtsogoleri oyamba kumene alinazo ndi chilimbikitso chachikulu ndipo zimapeleka chikhumbokhumbo chokula.  Paulo anaitananso poyela chomwe chimadzakhala patsogolo lawi la moto,  makamaka pobutsa motowo mwa kamodzi kenaka kubutsanso choncho nkumakula nkudzakhala lawi la moto.  Koma Paulo anali ndi chindinji pa chimene Timoteo adzakhale. Kulimbikitsatu uku nkwamtengowapatali kuti munthu akule ndi kupita patsogolo! Atsogoleri ena amaloza mphatso zawo koma atsogoleri muutumiki amatsindika mphatso zomwe zili ndi omwe amawatsogolera.  Popanga zimenezi amapititsa patsogolo atsogoleri omwe akukula.  

Kulimbikitsa atsogoleri kumatulutsa kuzidalira mwa ena

Pomwe Paulo analimbikitsa Timoteo, anadzakhala mtsogoleri wamphamvu yemwe " anaonetsa yekha." Kulimbikitsa kwa poyela komwe Paulo ankapeleka Kwa Timoteo kukuyenela kuti  kunampatsa chilimbikitso ndi mphamvu ndipo kunatakasa kuzidalira mwa iye. Chilimbikitso champhamvu chotani ichi choti  ndi mtsogoleri okhwima yemwe akhulupilire mwa ine kuti nditha kuchita ichi!

 Atsogoleri ena amakhulupilira kuti kuloza zofooka za ena zizawathandiza kukhala amphamvu. Atsogoleri muutumiki samalekelera zifooko, koma amalimbikitsa ndi kutsimikiza zizindikilo za kukula. Ndipo pomwe akulimbikitsa, atsogoleri muutumiki amamanga atsogoleri ozidalira.  

Kulimbikitsa atsogoleri kumatulutsa kubeleka

Paulo analimbikitsa Timoteo ndipo sizodabwitsa kuti Timoteo amatha"kupatsa mphamvu ndi kulimbikitsa"okhulupilira a ku  Tesalonika. Chilimbikitso ndichopatsilana kuchokela kwa mtsogoleri wina kupita kwa winanso.

Atsogoleri ena amaganiza kuti atha kubeleka atsogoleri powapatsa maphunziro.  Koma atsogoleri muutumiki amabeleka kudzela mu chitsanzo chawo, amaonetsa njira. Amazindikira kuti utsogoleri kwambili umagwilidwa kuposa kuphunzitsidwa.  Kotero amalimbikitsa,  ndipo amabeleka alimbikitsi!

Kodi mukufuna atsogoleri okula, odalilika ndi obeleka? Tsogolerani ndi chilimbikitso! 

 Zoti tilingalire ndi kukambirana:

·         Kodi omwe amanditsatila akhoza kundifotokoza kuti ndine mtsogoleri olimbikitsa?  Chifukwa chani  kapena kapena ayi chifukwa chani?

·         Kodi kawirikawiri ndimapeleka mau a chilimbikitso mwanseli kapena poyela?  Kodi nditsate ndondomeko ziti kuti zonsezi ziziyendela pamodzi?

·         Kodi ndimunthu uti yemwe amanditsatira amene ndingakonde kumulimbikitsa? (Ngati mwampeza munthuyo yankhani mafunso otsatirawa okhudza munthuyo)

·         Kodi ndi mphatso ziti zomwe ndimaona mwa munthuyo?

·         Kodi mphatsozo zidzabala chani mtsogolo?

·         Kodi ndinganene ichi motani mseri?

·         Kodi ndinganene ichi motani pagulu?

·         Kodi ndiliti lomwe ndizapange ichi?

Muphunziro lotsatirali,  tiona kasankhidwe ka utsogoleri ka Paulo powakonda

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Kuti mulandile izi pa WhatsApp dinani apa

 

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Leaders Serve and Jon Byler. Copyright, 2025

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online