Paulo mwadaladala anaitana gulu la atsogoleri omwe akuphuka kumene kuti akhale momuzungulira ndipo ankayendela limodzi, kuphunzila ndi kukuzidwa muulendo wa utsogoleri kuchoka pa malo apa kupita pena. Monga tinaonela muphunziro lapitali panali nthawi yotuma Timoteo ndi ena kutuluka nkumabwelanso,kuwakuza ndi kukulitsa utsogoleri wawo.
Koma munthawi Ina, Timoteo anafika pokula ndi kukhwima ngati mtsogoleri. Kwakanthawi kena kake anaikidwa mundende (Onani Ahebri 13:23) kenaka anamasulidwa. Tsopano Paulo anamutuma ku mpingo wa ku Efisasi kuti akakhale mbusa wakumeneko.
1 Timoteyo 1:3
3 Monga ndinakupempha pamene ndinkapita ku Makedoniya, khala ku Efeso komweko kuti uletse anthu ena kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga,
Zomwe zinkachitika malingana ndi Paulo kusankha kwa utsogoleri kwa Paulo zinali ziti? Anali atasankha Timoteo, kumuonetsa kuti angatsogolere bwanji,kumpatsa mphamvu ndi kumutambasula. Tsopano inali nthawi yoti ammasule Timoteo kuti akagwire ntchito yomwe anaphunzira kuti akaigwire. Munthawi imeneyi Paulo anamutuma yekha kuti akagwire ntchito yotenga nthawi yaitali. Timoteo anali okonzeka ku ntchito yatsopano ndipo Paulo anammasula kuti akagwire ntchito yake. Mbiri yampingo imatchula Timoteo ngati bishop wa ku Efisasi. Atsogoleri muutumiki onelani kuchokela Kwa Paulo zomwe zimachitika pomwe atsogoleri amasulidwa kuti akagwire ntchito zatsopano.
Kumasula atsogoleri kumakulitsa kuthekela.
Mpaka munthawi iyi mu kukula ndi kupita patsogolo Kwa Timoteo muutsogoleri wake amaphunzila utsogoleri ndi Paulo kapena ndi ena a mugulu lawo. Paulo anamasula Timoteo kuti akagwire ntchito pa Iye yekha ngati njira Ina imodzi yochulukitsila atsogoleri ku ntchito. Pomwe Paulo anamasula Timoteo kuti akagwire ntchito ku Efisasi munthawi yomweyo amathanso kutuma Tito kuti akagwire ntchito ngati yomweyo ku Crete. (Onani Tito 1:5). Paulo anakuza kuthekela kwa payekhapayekha ndicholinga pomawamasula atsogoleri amugulu lake kuti azikagwila ntchito pawokha.
Atsogoleri ena amapangitsa kuti kukula kukhale kopinimbila kwa omwe alipansi pawo polephela kuwamasula kwatunthu kuti akagwire ntchito pawokha. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira kuti mtsogoleri aliyense yemwe akukula azafunika kuti munthawi Ina azamasulidwe kuti akathe kukula muutsogoleri kwatunthu mwa kuthekela kwa Iwo okha. Izi sizikuthanthauza kuwaleka okha monga tizaone muphunziro likubwelari, koma zikutanthauza kuti kuwamasula kuti akagwire ntchito.
Kumasula atsogoleri kumakulitsa kuthekela kochitabwino.
Zitatha zaka za maphunziro pansi pa Paulo, Timoteo tsopano ndi oyang'anira mpingo omwe Paulo anadzala. Zonse zomwe anaphunzila zaka zonsezi tsopano zimanoledwa ndi kuyengedwanso chifukwa anali wamkulu wapamalopo. Amatha kulumikizana ndi Paulo mwakamodzi kamodzi kudzela mu makalata,koma ankayenela kupanga zisankho ndi kugwira ntchito ndi anthu. Anali mtsogoleri tsopano. Palibe chinthu ngati kukhala mtsogoleri chomwe chimakuza kuthekela kochitabwino ngati mtsogoleri!
Atsogoleri ena amayesetsa kukulitsa kochitabwino kudzela mu maphunziro ndi uphungu. Pali ndithu mpata ndi nthawi yochita zimenezi, koma atsogoleri muutumiki amazindikiranso kuti makhala nthawi yomasula mtsogoleri kuti auluke pa Iwo okha.
Kumasulira atsogoleri kumakulitsa chidaliro
Kudalira kozama kwa Paulo pa Timoteo kunathandiza kukulitsa kuzidalira mwa Timoteo.Tangoganizani Timoteo kufika ku Efisasi, nthawi imeneyi osati ngati opelekeza Paulo koma koma ngati mtsogoleri wa mpingo. Nthawi yoyamba wina anamutcha "abusa" akuyenela kuti adabwa kukhala ngati anthu anasokoneza! Paulo analemba kalata ndi kumulimbikitsa kuti asalore ena amuyang'anile pansi chifukwa anali wachichepele (1 Timoteo 4:12). Koma pomwe Paulo anamumasula Timoteo kumpatsa udindo umeneu, anakula mukuzidalira Mumphatso yake yake ndi maitanidwe ake kuti achite ntchitoyo. Atsogoleri ena amalephera kumasula chifukwa alibe kutsimikizika kuti ena atha kugwira ntchito. Atsogoleri muutumiki amakuza ena kufikira atafika mulingo oti atha kumasulidwa ndi kuikiza kuzidaliramwa Iwo pamene akuchita izi.
Zoti tilingalire ndi kukambirana:
- Kodi ndine wachangu kumasula atsogoleri kapena ndine ochedwa kwambili? Kodi omwe andizingulira atha kuyankha motani pafunso limeneli? Kodi ndikufunika ndisinthe pati kuti ndikhale wapakatikati mudela limeneli?
- Kodi ndi atsogoleri ati omwe ndikuwakuza nthawi ino ndipo ndondomeko yotsatila ndiyotani mu kukula kwawo? Ndi ati ndi ati omwe ndi okonzeka kuti amasulidwe? (Lingalirani kuti izi zikutanthauza chani kwa munthu aliyense).
- Kodi ndi ndondomeko zapadela ziti zomwe ndingatsate kuti ndikuze kuzidalira mwa omwe ndakhala ndikuwakuza,makamaka mwa Iwo omwe ndili nawo kapena posachedwa nditawamasule?
|