Masomphenya a Paulo ankafunikila kusankha utsogoleri komwe kukanapitiliza kudzutsa atsogoleri okhwima. Choncho,monga taona kale, tinawasankha, tinawakonzekeletsa, tinawaonetsa njira, ndinso tinawapatsa mphamvu. Njira imodzi mwa njira zomwe anapatsila mphamvu ena ndikuwapatsa ntchito zomwe zinawakulitsa. Chitsanzo cha ichi chikuoneka pomwe anatumiza atsogoleri awiri ophuka mwamphamvu kuti atsogole.
Machitidwe a Atumwi 19
22 Iye anatuma anthu awiri amene amamuthandiza, Timoteyo ndi Erasto ku Makedoniya, pamene iye anakhalabe ku Asiya kwa kanthawi.
Kenako, Paulo amatha kutuma Timoteo payekha ku Efisasi kuti akatsogolere mpingo omwe Paulo anadzala kumeneko.Ntchito zonsezi, ndizina zambiri, zinatambasula Timoteo kuti akule ndi kukhala mtsogoleri. Paulo mosamala ankakonza ntchitozi mpaka ku mulingo wokhwima omwe Timoteo anali nawo. Amatha kutambasula Timoteo koma osamuphwasula. Ntchitozo ankazikonza kuti zizivutilavutilabe, kutambasula Timoteo kuti azipitiliza kukula. Paulo akuonetsela kwa mtsogoleri muutumiki mphamvu yotambasula omwe ali mukusankha kwa utsogoleri wathu.
Kutambasula atsogoleri kumapangitsa kuonjezela
Paulo mwadaladala ankawalera omwe anamuzungulira,koma anazindikira kuti amafunikanso ntchito zina zovutilako zomwe zikanawathandiza kuti akule muutsogoleri paokha.Pomwe Paulo ankatuma Timoteo ndi Erasto kuti atsogole ku Makedoniya,anali kumanga kuthekela kwawo kwa utsogoleri poonjezela luso lawo ndi kuthekela kwawo kuti zituluke. Anali ataona Paulo akutsegula dela latsopano ndikupanga maubale ndi otembenukamtima kumene, tsopano amatha kupanga izi pawokha. Paulo anawatuma ngati gulu pa ntchito yomwe anapatsidwayi, mwinamwake pozindikila kuti akanafuna kuthandizilidwa,chilimbikitso ndi thandizo la wina ndi mzake kuti akwanilitse ntchitoyi. Amatha kuthandizana wina ndinzake kukula ndi kupita patsogolo.
Atsogoleri ena amakhutitsidwa kukhala ndi otsatira omwe amapanga ntchito yawo bwino. Koma atsogoleri muutumiki amasakasaka kuonjezela kuthekela kwa omwe amawatsogolera ndikuwapatsa ntchito zomwe zimawatambasula.
Kutambasula atsogoleri kumapangitsa kupangila limodzi
Timoteo ndi Erasto anali kale atsogoleri odalilika amugulumo ndi ozipeleka ku masomphenya a Paulo. Koma ntchito iyi inazamitsa mulingo wa kupanga nao zithu pomwe anadzuka ndikugwira ntchito yomwe Paulo anaika patsogolo pawo. Amayenela kuganiza pawokha ndi kupeza njila yaoyawo yothana ndi zinthu zomwe anakumana nazo ku Makedoniya. Monga momwe Paulo anazindikira kufunika kochuluka kwa ogwira ntchito yemwe wakumana ndizokhoma, atsogoleri muutumiki lero amazindikira kuti anthu ogwira ntchito omwe amakumana ndi mavuto kawirikawiri komanso opasidwa mphamvu pa ntchito yawo ndi omwe amazakhala zida zodalilika za bungwe.
Atsogoleri ena amakhala okhutitsidwa kukhala ndi anthu ogwira ntchito omwe samasiya ntchito koma amawapatsa ntchito zoti agwile kuti zithandize gulu lawo kutengambali kwatunthu.
Kutambasula atsogoleri kumapangitsa kufikira madela ena
Zotsatila za Paulo potambasula atsogoleri achinyamatawa ndichoti gulu linapitilira kukula.Potha pa ulendo wa utsogoleri wa Paulo,anali atawumba atsogoleri omwe akanatha kuwatuma mmalo mwake kupita ku madela osiyanasiyana. Kasankhidwe ka utsogoleri ka Paulo kanamupatsa kuthekela kotsegula mipingo mudziko lonse Aroma ndipo anaika maziko a kukula omwe akupitilirabe lero!
Atsogoleri ena amalakalaka kukula powonjezela mamembala kugulu lawo. Atsogoleri muutumiki amatambasula atsogoleri omwe alinawo kuti awone kukula kukuchitika chifukwa cha kupanga motero.
Zoti tilingalire ndi kukambirana:
· Kodi ndi mtsogoleri uti yemwe ndikuikizamo za utsogoleri yemwe azapindule mu ntchito yotambasula? (Mukapeza munthuyo ,gwiritsani ntchito mafunso enawa kuti mupange pulani yochitapo kanthu)
· Ndichani mumbiri ya munthuyu chomwe chikuonetaa kuti ndiokonzeka kuntchito yatsopano?
· Kodi ndinjila ziti zomwe ndizomutambasula munthchito yamunthuyu?
· Kodi ilipo imodzi mwa njilazi yomwe ndiyophweka kwambili yomupangitsa kumutambasula? zilipo njira zina kodi zomwe ndizovuta kuti kupambana kungakhale kovuta?
· Kodi ndinjira iti yomwe ikuonetsa kuti ndi mwayi oyenela kwa mtsogoleri ameneyu?
· Kodi ndingatani kuti njira iyi ndigwiiritse ntchito ndipo ndiliti lomwe ndizayambepo njira yoyamba? |