Atsogoleri muutumiki samasunga ulamuliro, amaupeleka! Amatsatira chitsanzo cha Yesu yemwe mau ake omaliza anali okhudzana ndi ulamuliro.
Mateyu 28
18 Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.
19 Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera,
20 ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”
Yesu anakwanitsa kunena moona mtima, "Ulamuliro onse kumwamba ndi dzikolapansi wapatsidwa Kwa ine." Koma pomwe anangotsiliza kunena mauwa, anapeleka ulamuliro wake kwa ophunzira ake. anapeleka chitsanzo champhamvu kwa atsogoleri onse muutumiki.
kupeleka ulamuliro kumaonetsa chidaliro
Kuti Yesu apereke ulamuliro kwa kagulu kochepa aka kunaonetsa chidaliro chozama mwa iwo komanso zomwe anaikiza yekha mumiyoyo yawo.
Yesu ankadziwa zolakwa zawo. Koma, anawadalira kuti apititse cholinga chake kudziko lonse. Atsogoleri ena amaona kuti ulamuliro wawo ngati chinthu chawo chopezela mpata koma osachipeleka. Amakakamila kugwila ntchito yonse okha. Sagwila ntchito yokuza kapena kukhwimitsa gulu lawo. Amayembekezela ungwilo mwa otsatira awo asanawapatse ulamuliro. Koma atsogoleri muutumiki amayamba ndi chikhumbo chopeleka ulamuliro ngati chinthu chachangu ndi choyenela mwamtima onse. Amasakasaka mwai othandiza gulu lawo kuti likule ndi kuyeselera kuwapatsa ntchito zina ndi Zina. Amayembekezela zolakwitsa zina ndi zina mkatimo ndipo amawalongosolera zolakwitsa. Koma amatumikira podalira omwe akuwatsogolera. Amaona kuthekela ndi kukhumba kuona kuthekelako kukukuzika mwa iwo kenaka kuwamasula amuke. Atsogoleri muutumiki amatumikira podalira omwe amawatsogolera.
Kupeleka ulamuliro kumapangitsa kufunsidwa pazomwe wachita
Ngakhale Yesu analankhula mau awa pomwe amachoka padziko lapansi, anakumbutsanso ophunzila "Ndili nanu nthawi zonse...." Chimenechi chinali chitonthozo chakupezeka komanso chowakumbutsa kuti pomwe ulamuliro wake anaupeleka, panalinso udindo omwe anawasiyila powatuma. Amayembekeka kuti apite ndi "kukapanga ophunzila...kubatiza....Kuphunzitsa..." Yesu sanawapatse ulamuliro kuti azikachita mulimonse momwe afunira. Anawapatsa malangizo omvekabwino ndipo azawafunsa kuti ayankhepo pa zomwe anachita. Atsogoleri ena amapereka ulamuliro popanda kalondolondo ndipo amaona ngati kutero ndekuti ndikuwadalila anthuwo kothelatu. Koma atsogoleri muutumiki amaphatikizilapo kalondolondo pomwe akupeleka ulamuliro. Amafotokoza bwino zomwe akuyembekezela pa ulamuliro omwe apatsidwawo ndiponso kuti ayembekezele kufunsidwa. Amatumikira popeleka ulamuliro ndi kuphatikizanso kuyankhapo.
Kupeleka ulamuliro kumatsimikizila kuchuluka
Njira yomwe Yesu anapelekela ulamuliro inapangitsa otsatira ake "kupita ndi kukapanga ophunzila ku maiko onse." Anamanga kuchulukitsa kupeleka kwake Kwa ntchito. Atsogoleri ena amagwira ntchito molimbika kuti bungwe lawo likule. Koma atsogoleri muutumiki amaonetsetsa kukula ndi kuchuluka popereka ulamuliro kwa omwe akuwatsogolera. Amazindikira kuti ngati akakamile kugwila ntchito yonse okha, ntchito yonse sizagwirika. Atsogoleri muutumiki amaonetsetsa kuchulukitsa popeleka ulamuliro.
|