Gawo #336, August 21, 2024

Kutumikira Ndi Ulamuliro: Upatseni Ulemu

Atsogoleri muutumiki, ngati atsogoleri ena onse, ali ndi ulamuliro komanso amagwilitsa ntchito ulamuliro. Ulamuliro ndi mphamvu yopelekedwa yomwe imawapatsa ufulu ochita monga mwa udindo wawo ngati mtsogoleri. Koma atsogoleri ambiri amatenga nkhani  ya ulamuliro mwa njila yosakhala bwino. Kodi ulamuliro ndi wabwino kapena ayi? Kodi zimayendelana bwino motani ndi mchitidwe otumikila ena? Muphunziro limeneli tiunikila momwe atsogoleri muutumiki ulamuliro amaonela ndi kugwilitsila ntchito ulamuliro. Poyamba, pongoonako pang'ono pamoyo wa Davide zikuonetsela kuti atsogoleri otumikila amapatsa ulemu ulamuliro omwe uli pamwamba pawo. Davide anadzodzedwa kukhala mfumu, koma  Saulo anali akadali pampando ndipo ankathamangitsa  Davide ndi gulu lake. Kawili konse, Davide anali ndi mwayi  osavuta oti aphe Saulo ndi kutenga ufumu. Mu imodzi mwa nthawizi, Davide anadula pambali pa mkanjo wa Saulo.

1 Samueli 24

5 Atachita izi, Davide anatsutsika mu mtima chifukwa anadula msonga ya mkanjo wa Sauli.

6 Tsono anawuza anthu ake kuti, “Yehova asalole kuti ndimuchite choyipa mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Ndisamupweteke pakuti ndi wodzozedwa wa Yehova.”

7 Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka.

Kuziletsa kwa Davide kukuonetselatu poyela ulemu wake pa ulamuliro wa Saulo ngakhale kuti Saulo ankafunafuna kumupha.Davide amazindikira kuti Saulo anali mfumu ndipo amalemekeza udindo wake ngakhale sankagwilizana ndi zochita za mfumu. Kuyankha Kwa Davide kukuonetsela atsogoleri muutumiki zotsatila za ulemu kwa omwe  akuwalamulira pamwamba pawo.

Ulemu ku ulamuliro umamanga khalidwe

Nthawi imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri mmoyo wa Davide pomwe anali kuthamangitsidwa ndi mfumu Saulo. Inali nthawi yomwe khalidwe lake linayesedwa ndi kuumbidwa munjila zamphanvu kwambili. Chofunika kwambili, Davide amaphunzila kuti asanakhale  muulamuliro, ankayenela kukhala kuphunzira kukhala pansi pa ulamuliro. Zimenezi nthawi zonse ndi phunziro lovuta kwambiri kwa atsogoleri ndipo zovutanso kwambiri pomwe munthu yemwe ali muulamuliro asali mtsogoleri wabwino! Koma atsogoleri muutumiki amapereka ulemu kwa ulamuliro omwe ulipo ndipo amalola Mulungu kuti awumbe khalidwe lawo pomwe akuonetsa ulemu wawo kudzela mumawu awo ndi ntchito zawo.

Ulemu ku ulamuliro umamanga chidaliro

Davide anachita zinthu ndi ulemu ku ulamuliro chifukwa chinali chinthu chabwino kutelo. Koma otsatira ake analinso kuona. Pomwe amaona ulemu wa Davide kwa Saulo anakula mu chidaliro chawo pa Davide. Anaona kuti anali "ovutika ndi chikumbumtima" atadula mkanjo wa Saulo. Anamunva akumufotokoza mdani wake ngati "odzodzedwa wa Mulungu". Pomwe ankamuonetsetsa kwambiri, anazindikira kuti Davide anali mtsogoleri yemwe akanadalira. Atsogoleri muutumiki amamanga chidaliro ndi omwe akuwatsata pomwe akupeleka ulemu kwa ku ulamuliro omwe uli pamwamba pawo.

Ulemu ku ulamuliro umamanga anthu

Machitidwe a Davide anabetchela ndi kuumba omwe ankamutsatira. Ngakhale sanali kugwilizana ndi zomwe ankachita ulemu wa Davide kwa Saulo kuwathandizila kukula. Davide amawathandiza kuwakuza powadzudzula pomwe zomwe ngodya zawo sizinagwilizane ndi zake. Pomwe anthu akewa anachitila umboni kumvela kwa Davide kwa Saulo, nawonso anayamba kukhala omvela kwambili kwa Davide. Anthuwa akatumidwa kunkhondo amatha kupita ndikukapanga chipambano chachikulu kwa Davide. Anadziwa kuti chifukwa Davide anali ndi ulemu kwa ulamuliro, sakadatha kugwilitsitsa ntchito ulamuliro molakwika atakhala pampando. Atsogoleri muutumiki amatumikira omwe akuwatsata popatsa ulemu ulamuliro omwe uli pamwamba pawo. Popanga zimenezi amamanga anthu owazingulira.

Zoti tilingalire ndi kukambirana:

  • Kodi machitidwe anga pa omwe ali pa ulamuliro pamwamba panga ndiotani? Kodi ndimatha kuwapatsa ulemu ngakhale sindikugwilizana ndi zisankho zawo? Kodi machitidwe anga amakhuza bwanji njila yomwe ndimatsogolera anthu?
  • Kodi malankhulidwe anga pa za omwe ali pamwamba panga muulamuliro ndiotani? Kodi zimenezi zikukhudza bwanji pa utsogoleri wanga pomwe omwe akutsatira akumva ndemanga zanga?
  • Kodi ndimafuna omwe ali pansi pa ulamuliro wanga awone motani utsogoleri wanga? Kodi ndili ndi kuona kofanana kwa omwe ali pamwamba panga? Kodi zimenezi zikukhudza bwanji kuthekela kotumikira omwe ali pansi panga?

 

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona mene atsogoleri muutumiki amavomelera ulamuliro.

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024