Gawo #335, August 7, 2024

Barnaba: Kutumikira Ndi Khalidwe

Taonapo machitidwe angapo omwe anapanga Barnaba kukhala mtsogoleri otumikila wamphamvu. Pomwe tikumalizitsa kuonanso moyo wake, tiona mbali Ina yomwe inapanga maziko a machitidwe ake abwinowa. Mu imodzi mwa zomwe tinatchulapo za moyo wake tinaphunzila kuti anali 'munthu wabwino.

Machitidwe a Atumwi 11

22 Mbiri imeneyi inamveka ku mpingo wa ku Yerusalemu ndipo iwo anatumiza Barnaba ku Antiokeya.

23 Atafika ndi kuona chisomo cha Mulungu pa iwo, anakondwa ndi kuwalimbikitsa anthu onsewo kuti apitirire kukhala woona mu mtima mwa Ambuye.

24 Barnabayo anali munthu wabwino, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro ndipo gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Ambuye.

Barnaba anali "munthu wabwino," Umboni wa khalidwe lake. Khalidwe lake linali maziko omwe makhalidwe ena onse odabwitsa a moyo wake amatumphukira. Anaonetsa atsogoleri onse muutumiki kuti kutumikila ena kumayambira ndi chomwe tili.

Khalidwe limatumikira poonetsa zizindikilo za chomwe tili

Barnaba anali odzala ndi "chikhulupiliro komanso Mzimu." ichi chinali ngodya ya chomwe anali. Makhalidwe ake abwino anapeleka chizindikilo cha chomwe chinadzadza mkati mwake. Atsogoleri ena amayesetsa kusamalira chomwe anthu amaona mwaiwo ndipo amalimbikila kuti awumbe makhalidwe awo, kuwaona ngati aphimba chenicheni cha chomwe ali mkati mwawo. Koma tikafika pothina, chomwe chili mkati mwawo chimatulukila kunja mwa mau a ganyavu, mokwiya kapena kulimbila udindo Ntchito sizisonyeza khalidwe, koma zimavumbilutsa khalidwe. Atsogoleri muutumiki amaika chindunji chawo pa kuzidzadza okha ndi  zinthu zoyenera. Amakhala osamala pa zomwe amawelenga, zomwe amaona,ndi zomwe amalingalira. Amazindikira kuti khalidwe lawo limapereka chizindikilo ku dziko choti iwo ndi ndani.

Khalidwe limatumikira powumba zomwe timachita

  "...anali okondwa ndipo anawalimbikitsa kuti akhalebe muchoona kwa Ambuye ndi mitima yawo yonse." Pomwe Barnaba anafika pa mpingo wa ku Antiokea, anaona zomwe zinkachitika ndipo anayankha ndi kulimbikitsa. Chifukwa? Sanafune kuima ndinkuganiza kaye kuti mayankhidwe abwino akhale otani. Anangolola kuti khalidwe lake liwumbe mayankhidwe abwino. Analimbikitsa chifukwa anali mlimbikitsi. Zotsatira zamphanvu zinatsatira, "anthu ambiri anabwela Kwa Ambuye." Atsogoleri ena mosamala amaika pasikelo kuluza kapena kupindula komwe kulipo kudzela muntchito zawo ndipo amapanga ziganizo kudzela muzomwe zingapititse patsogolo kapena kuletsa zolinga za iwo Koma atsogoleri muutumiki amatipula khalidwe labwino kenaka amalola chimenecho kuti chiwumbe zomwe amachita.Amachita zomwe zili zabwino, osati zomwe zili zopeleka ntebelele. Amachita zomwe zikufunikira, osati chomwe zili zosangalatsa anthu. Khalidwe lawo limawathandiza kuika chindunji chawo pa phindu lotenga nthawi mmalo mwa mphindu la nthawi yochepa. Akhoza kudalira mopanda nkhawa pa khalidwe lawo kuti liwumbe zomwe amachita.

Khalidwe limatumikira poongolera komwe timapita

Barnaba anatumidwa ndi atsogoleri ampingo kuti akatumikire ku Antiokea. Anazindikira ubwino wa khalidwe lake motelo anatsegula makomo a maudindo ena apamwamba pa iye. Anamudalira chifukwa amadziwa khalidwe lake. Kudalira kumeneko kumatsogolera ku ntchito Ina ine yoti agwile. Atsogoleri ena amafunafuna kupita patsogolo podzilika mosamala pamodzi ndi anthu oyenela kapena kuona komwe amapita kudzela mu zotsatila za  zokhumba zawo. Koma atsogoleri otumikila amatipula khalidwe lomwe limatsegula makomo Kwa Iwo ndipo limawawongolera ku njira yoyenera. Khalidwe lawo limagwira ntchito ngati chida chowazindikilitsa komwe angatumikilire bwino.

Moyo wa Barnaba tausanthula ngati yemwe anatumikilira bwino chifukwa cha chomwe Iye anali. Akubetchela atsogoleri onse muutumiki kuti azipanga khalidwe lawo ndikulolera khalidwe lawo litumphuke kuchokela mu chimenecho.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi khalidwe la Barnaba likundiphinzitsa chani ngati mtsogoleri? Kodi ndingachitepo chani msabatayi kuti ndikhale motsatila Iyeyu?
  • Kodi ndine odzadzidwa ndi chani! Kodi Umboni  Ndi chotani mu chomwe ndili pa ngodya za mmoyo wanga? Kodi ndimachita chani kuti ndikhale odzadzidwa ndi chomwe chimatulutsa khalidwe labwino mu moyo wanga?
  • Kodi chomwe chimawumba ntchito zanga ndichani? Kodi ndimalora khalidwe langa liwumbe chomwe chili chabwino kuchichita kapena kodi ndimaika chindunji changa pa momwe ena alankhulire kapena momwe chisankho chipititsile patsogolo zolinga zanga?
  • Kodi chomwe chimatsogolera chipambano changa ndichani? Kodi ndi luntha langa kupanga dongosolo lomwe linditengele komwe ndikufuna kupita, kapena ndi khalidwe langa lomwe limatsegula makomo a utumiki?
  • Kodi ndikuchitapo chiyani kuti ndilimbitse khalidwe langa? Kodi pali madela ena a khalidwe langa omwe ndikufunika kumupempha Mulungu ndi ena kuti andithandize kukula?

 

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiyamba Mutu watsopano! Ndi thawi yopambana yoitanira ena kuti ajoine  pagulupa. Muwatumizileko ndi kuwaitanira kuti aone Mutuwu ndipo dinani apa.

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024