Barnaba anali mtsogoleri wamphamvu ndipo taonapo zinthu zambiri zazikulu kuchokela mmoyo wake. Koma sanali osalakwitsa! Zinthu ziwiri zinalembedwa zomwe zikuonetsela zolakwitsa zake.
Machitidwe a Atumwi 15
36 Patapita masiku ena Paulo anati kwa Barnaba, “Tiyeni tibwerere kuti tikaone abale ku mizinda yonse imene tinalalika Mawu a Ambuye ndipo tikaone mmene akuchitira.” 37 Barnaba anafuna kutenga Yohane, wotchedwanso Marko, kuti apite nawo. 38 Koma Paulo anaganiza kuti sichinali cha nzeru kumutenga Yohane chifukwa iye anawathawa ku Pamfiliya ndipo sanapitirire nawo pa ntchito. 39 Iwo anatsutsana kwambiri kotero kuti anapatukana. Barnaba anatenga Marko ndipo anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. 40 Paulo anasankha Sila. Abale atawapempherera kwa Ambuye kuti alandire chisomo, ananyamuka. 41 Iye anadutsa ku Siriya ndi ku Kilikiya kupita akulimbikitsa mipingo.
Atatumikira pamodzi ngati gulu lamphamvu kwa zaka, Paulo ndi Barnaba sanagwilizane kuti atamutenge Maliko pa ulendo womwe unalipo! Mkangano waukulu osathawu ndi omaliza kuunva pa Barnaba mubuku la Machitidwe!
Kapena mkangano oziwika bwinowu usanachitike, panalinso kutsutsana pa nkhani ya mdulidwe ku Antiokea. Petulo anachita mwachinyengo ndipo anadzudzulidwa pagulu ndi Paulo. Polemba zomwe zinachitikazi, Paulo anatinso:
Agalatiya 2
13 Ayuda enanso anamutsata pochita zachinyengozi, kotero kuti ngakhale Barnaba anasocheretsedwa chifukwa cha chinyengo chawocho.
Mmene zilirimu, Barnaba ndi Petulo akuonetselatu kuti analakwitsa (werengani). Koma zolephela za Barnaba zikuonetsela kwa atsogoleri kuti ngakhale mukulephela kwathu, tikhoza Kutumikira ena.
Kulephela kwa Barnaba kumatumikila poonetsela kuti kulephela kumakhalapo.
Paulo anaganiza mwapamwamba za Barnaba mpaka anati "ndi Barnaba yemwe anasocheletsedwa". Akutanthauza kuti Barnaba anali munthu omalizila yemwe amayembekezela kuti sangapange kulakwitsaku! Koma Barnaba analakwitsa ndipo zikuotsa atsogoleri onse kuti aziyembekezela kulephela. Mwachidziwikile, sichimakhala cholinga kapena kukonzekela kulephela, koma tizidziwilatu. Atsogoleri ena amaona ngati kulephela ndi chizindikilo choti zakukanika, choncho amamva kukakamizika kuti aziphimbe, kukana kapena kusalabadila kulephela. Koma atsogoleri muutumiki amavomereza umunthu wawo ndi choonadi ichi choti atsogoleri onse amalephera. Amazipatsa okha chisomo ndi kupempha chisomo kuchokela kwa ena akalephela. Popanga zimenezi, amatumikira ena poonetsela kuti kulephela kumakhalapo.
Kulephela kwa Barnaba kumatumikila kuti kulephela sikutha kwako.
Nkhani ya Barnaba yomwe inasungidwa ikuthela pa kusamvana pakati pa iyeyo ndi Paulo koma ntchito yake sinathele Barnaba anatenga Marko pa ulendo wake wautumwi ndipo pamene sitikudziwa zotsatila, mwachidziwikile tikuyembekezela kuti mipingo yomwe inadzalidwa inalimbikitsidwa ndiponso Ina inadzalidwa kudzela muntchito zawo. Atsogoleri ena amaona ngati kulephela ndi kutha kwa ntchito yawo koma atsogoleri otumikila amamvetsetsa kuti kulephela sipothela. Amaphunzila kupitiliza ulendo pa kulephela kulikonse ndipo amatumikira poonetsa kuti kulephela sikutha.
Kulephela kwa Barnaba kumatumikila poonetsela kuti kulephela kutha kupangitsa kukula
Paulo ndi Barnaba onse anakula kudzela kusamvana kwawo. Paulo patsogolo pake anafunsa Marko kuti amuthandize( Onani 2 Timoteo 4:11). Barnaba anali ngati mtsogoleri wa gulu pomwe ankayenda ndi Marko. Mulungu anagwilitsa ntchito kusamvana kwawo kuti atumize magulu awiri mmalo mwa limodzi ndipo anabweletsa kukula mmipingo mwawo. Pa nkhani ya mdulidwe onse Barnaba ndi Petulo anaona zolephela zawo ndipo anakonza. Atsogoleri ena amaona ngati kulephela ndi kutha kwa kukula koma atsogoleri muutumiki amaona kulephela kwawo ngati mwai oti akule. Amafunsa chimene chinalakwika ndi chomwe angaphunzile. Amabweza, amasintha ndi kutengela ngati nkofunika kutero basi nkumapitiliza cholinga! Amatumikira magulu awo pokula kudzela mukulephela. |