jpeg

Gawo #333, July 10, 2024

Barnaba: Kutumikira Ndi Kudzichepetsa.

Palibe ndime yapadela mu baibulo imene imakamba za kudzichepetsa Kwa Barnaba, koma pali zizindikiro zochuluka zomwe zikuonetsa kuti anatumikira ndi kudzichepetsa. Poyamba, mmene anali munthu odziwika mu moyo wa mpingo,pomwe anthu adasankha madikoni oyamba, dzina lake panalibe.(Werengani Machitidwe 6:1-6). Izi zikadatha kukhala zokhumudwitsa kwambili kwa Iye, koma palibe ndi malo amodzi omwe akusonyeza kuti anakhumudwa posawelengedwa. Komanso chizindikilo china cha mphamvu chosonyeza kuti anali odzichepetsa ndi ubale wake ndi Saulo. (Yemwe anatchedwa Paulo) ndi momwe olemba mbiri (histole) Luka yemwe analemba buku la Machitidwe analembela za iye.Poyambilira munkhani dzina la Barnaba limatchulidwa poyabilira nthawi zonse. Anali mtsogoleri Paulo asanatembenuke zomwe zikusonyezelatu kuti dzina lake linali lodziwika ndithu. Kumpingo wa ku Antiokea, dzina la Barnaba limatchulidwa poyabilira.

(Machitidwe 13:1)Pomwe anali pa ulendo oyamba okadzala mpingo anapita ngati "Barnaba ndi Saulo"(Onani Machitidwe 13:6). Barnaba anali patsogolo. Koma izi sizinachedwe kusintha. Paulo anakhala otsogolera wamkulu pa gulupo, ngakhale ku Cypras, kumudzi  Kwa Barnaba. Nthawi yomwe anachoka ku Cypras, Paulo akulemba motere, "Paulo ndi gulu lake" (Machitidwe 13:13) ndipo pomwe Maliko anachoka, analemba motere "Paulo ndi Barnaba"(Machitidwe 13:42) Kuyambira pamenepa mpaka mtsogolo maina awo pàliponse amachulidwa mu  ndondomeko imeneyi. (Onani ndimwezi mu Machitidwe 14:14 ndi 15:2 ,25.). Pambuyo pa kusamvana kwa Paulo ndi Barnaba mu Machitidwe 15(pomwe tione mu phunziro lotsatirali) Barnaba anapita kokadzala mpingo komwe Luka sanalembe nkomwe mu mbili ya mpingo ndipo dzina la Barnaba silikutchulidwanso. Ndi mtsogoleri odzichepetsa yekha amene angapitilize Kutumikira ngakhale atasiya kumuwelengera. Kudzichepetsa kwake sikumupangitsa kukhala mtsogoleri ofooka koma mtsogoleri otumikila yemwe amaika chidwi chake pa ena osati pa iye mwini. Barnaba akuonetsa atsogoleri onse momwe angatumikilire ndi kudzichepetsa.

Kudzichepetsa kumatumikila pozindikila mphatso za ena

    Barnaba anazindikira mphatso ya Paulo poyambilira pa ubale wawo ndipo anapitiliza kukoka Paulo kupita naye kumadela omwe azikagwilitsa ntchito mphatsozo. Anabweletsa Paulo ku Jerusalem kenaka anamuitana kuti akhale naye limodzi pa ulendo opita ku Antiokea. Barnaba anali ndi mphatso ya utsogoleri, koma anapereka mpata kwa  mphatso za Paulo kufikila zitazindikilika ndi onse.

   Atsogoleri ena amafuna kuti mphatso zawo zokha zizindikilidwe ndipo amaopa mphatso zomwe zili mwa ena. Koma Atsogoleri muutumiki saophyezedwa ndi mphatso zomwe zili mwa ena. Samaikapansi  mphatso zawo koma amaitananira  chidwi ku mphatso zomwe zili mwa ena. Modzichepetsa amavomereza  ndi kuzindikila kuti enanso ali ndi mphatso zomwe Iwo alibe ndipo amafunitsitsa zoti enanso adziwe za mphatsozo.

Kudzichepetsa kumatumikila polimbikitsa mphatso za ena

   Barnaba sanangoona za mphatso za Paulo zokha, komanso anagwila ntchito molimbika kuti mphatsozo ziyendele pamodzi ndi zake. Ankayenda pambali pa Paulo ndi kubweletsa mphatso zakezo kuti ziyendele pamodzi ndi ntchito pagulu lawo. Ankayenda,kulalika ndi kutsogolela ndi Paulo. Ngakhalenso pomwe Paulo anatenga utsogoleri, anafuna mphatso za Barnaba. Atsogoleri ena amayang'ana ena kuti alimbikitse mphatso zawo. Atsogoleri muutumiki amayang'ana njila zomwe angalimbikitsile mphatso za ena.

Kudzichepetsa kumatumikila pogonjela kumphatso za ena

   Barnaba anafufutika mu  muzochitika zake pomwe anapatsa mpata Paul kuti adzuke ndikukhala  mtsogoleri. Anapereka mphatso zake ku ubwino waukulu ndi cholinga cha gulu. Atsogoleri ena amakana kupereka mphatso zawo ku zolinga zazikulu. Koma atsogoleri muutumiki amatula pansi mphatso zawo kuti  zolinga za gulu lawo zikwanilitsidwe. Pomwe, ngati Barnaba, zomwe zikusonyeza kuchokamo muzochitikazo, amavomela izi ndi kudzichepetsa. Ngati alipo omwe ali ndi mphatso ya  " Paulo" amapeza njila zozindikilira kupezeka kwa omwe ali ndi mphatso  ya  "Barnaba" pa gulupo zomwe amazindikira kuti ndizofunikira kuti pakhale chipambano.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi kudzichepetsa Kwa Barnaba kukundiphunzitsa chani ine ngati mtsogoleri? Kodi ndingachitepo chani msabatayi kuti ndikhale motsatila Iyeyu
  • Ndimunjila iti yomwe ndingazindikilire mphatso za ena lero mmalo mwa zanga?
  • Ndimunjila ziti zomwe mphatso zanga zimalimbikitsaena? Kodi ndingazindikire bwanji moyenela gawo la mphatso zanga pomwe ndikutumikilanso ena?
  • Kodi mwa chikumbumtima ndimapereka mphatso zanga ku cholinga cha gulu, kapena ndimaona kuti mphatso zanga ndi zofunika kwambiri kuposa cholinga cha gulu? Kodi zimenezi zikukhudza bwanji utsogoleri wanga?
  • Ngati ndili onga "Paulo mumphatso zanga ,kodi ndingachite chani kuti ndivomeleze gawo la "Barnaba" pa gulu langa lero?

Mpaka nthawi Ina,ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Barnaba anatumikilira ndi kulephela!

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024