jpeg

Gawo #330, May 22, 2024

Barnaba: Kutumikira Ndi Gulu

Barnaba anali mtsogoleri ochita zamphanvu mu mpingo oyamba, koma sanatumikire yekha. Barnaba anatumikila ndi gulu. Pafupifupi chitsanzo chilichonse pa Barnaba pakumakhala iyeyo ndi munthu winanso pamodzi naye. Izi zitha kuonekela bwino ku mpingo wa ku Antiokea pomwe Barnaba anatumizidwa kuti akapeleke utsogoleri kutsatila kutsegulidwa Kwa mpingo waung'ono kumeneko. Poyamba analimbikitsa okhulupilira. Koma nthawi yomweyonso anapita ku Tarsasi kuti akampeze Paulo ndikubwela naye ku Antiokea. Pamodzi anagwila ntchito kuti alimbikitse mpingo umenewu ndi kumanga gulu la atsogoleri lomwe patsogolo pake linatumiza Barnaba ndi Saulo pa ulendo omwe unakhala ulendo oyamba wa kodzala mpingo.

Machitidwe a Atumwi 13

1 Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. 2 Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, “Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira. ” 3 Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.

Barnaba anatumikira ena potumikira ndi ena. Akutipatsa  chitsanzo  cha momwe atsogoleri otumikila amamangila magulu pozungulira pawo omwe amathandiza kuti masomphenya ndi cholinga cha bungwe zikwanilitsidwe.

Kutumikila ndi gulu kumaonetsela Kusiyanasiyana.

Barnaba anazindikira kuti amafunikira Saulo; anazindikiranso kuti ankafunikira ena a mugulu lomwelo kuti athandizile kumanga mpingo umenewu. Gulu la ku  Antiokea linali losiyanasiyana. Munali mphatso zosiyanasiyana, anthu a mitundu yosiyana siyana ndi ochokela ku maiko osiyanasiyana komanso chodziiwikilatu osiyanasiyana umunthu wawo. Wina aliyense wa iwo anabweletsa mphamvu zapadela yosiyana ndi maonedwe osiyanasiyana a zinthu kugululo.

Atsogoleri wena amayesetsa kumanga magulu a anthu ofanana ndi Iwo, anthu oti adziona zinthu momwe iwo amaonela osapeleka mpata wa maganizo osiyana. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira mphamvu yomwe umatuluka mu Kusiyanasiyana. Amazindikira kuti sipadzakhala mtsogoleri owumbika bwino, koma angathe kupanga gulu lowumbika bwino. Amatsimikizika za mphatso zosiyanasiyana ndi malingaliro osiyanasiyana omwe ena amabweletsa ku magulu awo ndipo mwadaladala amafuna kumanga magulu kuchokela mu kuthekela komwe aliyense alinako.

Kutumikira ndi gulu kumapindula chitsogozo

Pamodzi gulu lidamva chitsogozo Cha Mulungu ndipo anatha kuyambapo kuchita chinthu chomwe chinali pamtima pawo chokuza mpingo kufikila madela ena. Chisankho chawo chimayenela kutengela mpingo kufikila madela onse a dzikolapansi. Munali mphamvu muchitsogozo chowe anatenga chifukwa samagwila ntchito payekhapayekha. Anamvetsela limodzi ndipo anathanso kuyendela limodzi.

Atsogoleri ambiri amapeza kuti ndi chinthu chosavuta kupanga chisankho pawokha ndi kuika njila zoti bungwe litsatire pawokha. Zimaoneka zachangu ndi zosavuta kuika njila motero. Koma atsogoleri muutumiki amazindikira kuti gulu limapereka nzeru zapamwamba. Atsogoleri muutumiki amagwira ntchito kudzela mmagulu kuti akwanilitse cholinga cha bungwe. Amazindikira kuti sangathe kuchita bwino kapena sangathe kuchitabwino koposa pawokha. Magulu awo amapereka nzeru zofunikira ndi maganizo omwe amawathandiza kupanga ziganizo zabwino zolingana ndi cholinga cha Mulungu pa kupezeka kwawo.

Kutumikira ndi gulu kumapewetsa chisokonezo

Kutsatira chisankho cha gulu, atsogoleri akulu akulu awiri anachoka pa mpingopo koma mpingowo unapitilirabe kukulabwino! Si mphatso ndi maitanidwe okha a Barnaba ndi Paulo zomwe zinaperekedwa kukatumikira dziko, koma atsogoleri omwe anatsalira ku Antiokea anakuzidwanso kufika milingo ina yatsopano ya ulamuliro ndi udindo Izi zinatheka chifukwa anagwila ntchito ngati gulu. Pamene palibe gulu pomwe mtsogoleri wachoka, kawilikawili ntchito imagwa. Koma atsogoleri muutumiki amadziwa kuti kupindula kokhazikika kumabwela ngati amanga magulu omwe angathe kumapitilirabe pomwe Iwo anyamuka. Amazindikira kuti pomwe palibepo kugwila ntchito ndigulu, sipadzakhala ntchito yopitilira. Kotero amasankha Kutumikira pomanga magulu.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi njira yomwe Barnaba anatumikilira ndi gulu zikundibetchela bwanji ine ngati mtsogoleri?Kodi ndingachitepo chani msabatayi kuti ndikhale monga Iyeyu?
  • Lingalirani pa gulu lanu lomwe liripo pano, Kodi muli Kusiyanasiyana kotani mugulu langa? Kodi tili ndi malingaliro onse ndi kuthekela mwa anthu zomwe zikufunikira panopa? Kodi ndi kuthekela kotani,ngati kulipo,komwe kukusowekela kuchoka mugulu?
  • Kodi ndili ndi zolinga zofunda kupanga ndondomeko zofikila patsogolo pa ine ndekha kapena limodzi ndi gulu?Kodi ndi munjila iti yomwe izi zikukhudza utsogoleri wanga? Kodi ndingachitepo chani kuti ndilimbitse kuthekela kwa gulu langa kopanga zisankho zanzeru?
  • Kodi chingachitike ndichani kugulu langa lero nditangoti ndapita mwadzidzidzi? Kodi gulu langa ndinaliwumba  zenizeni kuti lipitilize masomphenya popanda ine? Ngati sichoncho,kodi ndikuyenera kutsatila ndondomeko ziti kuti ndiwathandizile kukhala okonzeka?
  • Barnaba anamanga gulu lomwe linamumasula kuti apite ku maitanidwe apamwamba ndi aakulu.Kodi ndikukonzekeletsa gulu langa kuti lindimasule? Kodi zoti zichitike zioneka bwanji kwa ine?

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona momwe Barnaba anatumikilira ndi kulambira.

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024