jpeg

Gawo #328, April 24, 2024

Barnaba: Kutumikila Ndi Chilimbikitso

Nditati ndikufunseni kuti mutchule atsogoleri 10 a mumpingo wa  chipangano chatsopano, ndikukaika ngati Barnaba angapezekepo. Pomwe, anatumikila mpingo munjila zodabwitsa. Anali yemwe anapangitsa kuti Paulo alandilidwe mumpingo. Barnaba anathandiza kuti mpingo ukhazikitsidwe pomwe otsatila a Yesu anatchedwa koyamba Akhristu ndipo anali pa gulu loyamba lomwe linatumidwa kupita kukatumikila ku madela a mitundu ndi zikhalidwe zina. Anamudalila pomupatsa ndalama zochuluka ndipo anali mbali ya konsolo ya ku Yelusalemu yomwe inkapeleka thandizo mofanana Kwa okhululilira amitundu yakunja. Anagwila ntchito yaikulu mu miyoyo ya olembamba mabuku a Chipangano Chatsopano awili: Paulo ndi Marko. Mu phunziro ili tiona njila zomwe Barnaba anatumikilira mpingo ndi kuphunzila kuchokela mu chitsanzo chake. Koyamba kumva za Barnaba ndi nthawi inene mpingo unangongazikitsidwa kumene ku Yerusalemu.

Machitidwe a Atumwi 4

36 Yosefe, wa fuko la Levi, wochokera ku Kupro amene atumwi anamutcha Barnaba, kutanthauza kuti mwana wachilimbikitso, 37 anagulitsa munda wake ndipo anadzapereka ndalamazo kwa atumwi. (Chichewa Chatsopano Bible)

Pomwe anatchulidwa koyamba, tikupeza kuti dzina lake lenileni linali Yosefe, koma atumwi anali atamutchula kale dzina lina lotchedwa Barnaba chifukwa cha mmene ankalimbikitsila ena. Pomwe tilibe zolembedwa zomwe Barnaba anachita mbuyo asanatchulidwe, Pali machitidwe ambili omwe akutionetsa momwe Barnaba anatumikilira ndi chilimbikitso.

Barnaba analimbikitsa pokhulupilira mwa okanidwa.

Paulo amakhala ali otsogolera kuzunza mpingo ndipo cholinga chake chinali chokupha ndi kuika mundende omwe amatsatila Yesu. Ngakhale pomwe anatembenukadi, pomwe Paulo anabwela ku Yerusalemu, mpingo unali ndimantha ndikumuopa ndipo sukanamulandila Iye ngati m'bale mwa Ambuye (Welengani Machitidwe 9:26-27). Koma Barnaba anakhulupilira mwa Paulo ndipo anathandizila kuti amubweletse mumpingo wa ku Yerusalemu. Tangoganizilani momwe Paulo anamvela mkati mwake pamene ankanvetsela Barnaba akulemekeza ndi kulandila maitanidwe ake! Pokhulupilira mwa osavomelezeka mumpingo, Barnaba anatumikilira mpingo pobweletsa Odzala mipingo wamkulu kuposa aliyense! Atsogoleri omwe akutumikila amalimbikitsa pokhulupilira mwa okanidwa.

Barnaba analimbikitsa pokhulupilira mwa osazindikilika.

Chitangotha kumene chizunzo cha mpingo omwazika wa okhululilira, kagulu kochepa ka a Greek kanabwela ku chikhulupiliro mu Antiokea. Okhulupilira a chi  Greek anangobwela kumene muchikhulupiliro china chilichonse chomwe chinalipo munthawi imeneyo a mtundu wa chi Yuda munalibe. Anali osadzikilika  ndi osadziwika. Atsogoleri ampingo wa ku Yerusalemu unatumiza olimbikitsa odalilika wawo, Barnaba, kuti akafufuze zomwe amanvazo. Iye "anakondwa ndi kuwalimbikitsa..."(Machitidwe 11:23). Taganizani momwe okhulupilira amenewa anamvela mkati mwawo chifukwa cha kupita kwa Barnaba kukawalimbikitsa ndi kuwavomeleza. Barnaba anakhala kumeneko Kwa chaka chimodzi kupanga gulu la  anthu amenewa kuti afike potchedwa Akhristu oyamba ndi kukhala malo omwe uthenga wabwino unachokela ndikufalikila ku dziko madele onse otsala a dziko lapansi. Pokhulupilira mwa okhulupilira omwe anali asanazindikilike ku Antiokea Barnaba anatumikilira mpingo pomanga gulu lomwe  linakhala maziko a kukhazikitsa Kwa uthenga ku dziko lonse lapansi. Atsogoleri muutumiki amalimbikitsa pokhulupilira mwa osazindikilika.

Barnaba analimbikitsa pokhulupilira mwa omwe ndiolephela.

Marko,msuweni wake wa Barnaba, anapita ndi Paulo ndi Barnaba pa ulendo wawo oyamba okadzala mipingo, koma Marko anabwelela.Anazisiya! Kenako, pomwe anakonzeka kupita pa ulendo wawo wachiwili Paulo momvetsetseka sanafune kumutenga Marko, koma Barnaba anakhulupilira kuti ampatsenso mpata Marko (Werengani Machitidwe 15:37-39). Tangoganizani momwe Marko anamvela mkati mwake pomwe amanva Barnaba akulimbikila kuti ampatsenso mpata lachiwili! Pokhulupilira mwa omwe ali olephela, Barnaba anatumikila mpingo posunga kuthekela kwa utsogoleri komwe kunali mwa olemba buku la Marko. Atsogoleri muutumiki amalimbikitsa pokhulupilira mwa olephela.

Barnaba anatumikilira pokhulupilira mwa anthu omwe ena amaona zovuta kukhulupilira mwa iwo. Ndipo akuonetsa atsogoleri muutumiki mphamvu ya kukhulupilira kotero mwa ena.

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi Barnaba anali pa chiophyezo chotani pokhulupilira mwa Paulo, Marko ndi akhulupilira atsopano a chi Greek ku Antiokea? Kodi chinamutakasa ndi chani kuti apange chiganizo choika moyo wake pachiophyezo? Kodi chimakubwezelani mbuyo ndi chani kuti musakhulupilire anthu angati amenewa?
  • Lingalirani momwe Barnaba anakhulupilira mwa okanidwa,osazindikilika ndi olephela.Kodi pali pamene mukupezekapo pa magawo atatuwa? Kodi analipo wina, Onga Barnaba yemwe anakhulupilira mwa Inu ndi kukulimbikitsani? Ngati ndi choncho, Kodi mungapange chiyani kuti muonetsele kuthokoza Kwa Iwo?
  • Kodi ndindani mmoyo mwanu yemwe akupezeka pa magawo amenewo (osavomelezeka,osazindikilika ,olephela)? ndipo mungachitepo chani kuti mutumikile ndi chilimbikitso ngati Barnaba?
  • Kodi chilimbikitso Cha Barnaba chikubetchela motani pa Inu ngati mtsogoleri? Kodi mungachite chani msabatayi kuti mukhale monga Iye?

 

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Munkhani yotsatilayi, tiona momwe Barnaba anatumikilira ndi Kupeleka.

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa. Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024