jpeg

Gawo 275, January 6, 2021

Phokoso la utsogoleri wa chete..mu pemphero

Pomwe mukupemphera, ndi zochuluka bwanji zomwe ndi kulankhula kwanu? Nthawi zambiri timaganiza za kulankhula mu pemphero, kulumikizika ndi Mulungu kudzera njira imodzi. Zoona zake ili ndi gawo la pemphero ndipo liyenera kuwirikizidwa!
Koma kamba ka gawo ili, tikufuna kulingalira pa zomwe zimatanthauza mpemphero potsatira malangizo omwe akuperekedwa mu Mlaliki 5:2, ‘Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali ku mwamba , iwe uli pansi; chifukwa chake mawu ako akhale owerengeka.’ Mlembi wa mawu awa akulimbikitsa ife tonse kuphunzira kudziletsa mmapemphero athu kwa Mulungu.
‘Chifukwa chake mawu ako akhale owerengeka!’ Ichi ndichoyenera makamaka kwa atsogoleri omwe nthawi yawo yambiri amalumikizana   ndi mawu. Amalankhula momveka bwino, molimbamtima, komanso pafupipafupi pogawana masomphenya ndi maloto awo  ndi ena. Ndi chosadabwitsa kuti mtsogoleri angadze mapaso pa Mulungu mwanjira yomweyo, ndi mawu ambiri! Chobetchera kwa atsogoleri otumikira ndi kuphunzira kutsogoleri chininu mpemphero, ndi mawu ochepa. Pomwe akupanga izi, amaphunzira mphamvu ya chinunu mpemphero.

Kukhala chete mpemphero kumaonetsera kugonja.
‘Usafulumire kunena kanthu….’  Munthu yemwe amalankhula nthawi zambiri amalamulira zokambirana. Ndi chifukwa chake ndi kovuta kwambiri kukhala chete! Munthu yemwe ali wachangu kulankhula nthawi zambiri amalamulira nyengo. Atsogoleri makamaka amafuna kukhala olamulira ndi kuwonetsera ichi polankhula, nthawi zambiri mofuula! Atsogoleri adazolowera kuwonetsera njira, kupereka malangizo ndi kuwuza ena kuchitapo kanthu. Pomwe ndi nthawi ya pemphero, atsogoleri mwachibadwidwe amafuna kuchititsa Mulungu monga momwe amachitira ndi ena- ndi mawu ambiri! Koma chete amati, ‘Ine sindikulamulira, Ine sindine bwana!’
Kukhala chete kumaonetsa machitachita ogonjera. Chosamvetsetseka nchakuti, kugonjera kumasowekera kulimba mtima kwambiri. Kumaonetsera kudalira mwa Mulungu mmalo modzidalira wekha. Atsogoleri otumikira amaonetsera kugonjera mpemphero pokhala  chete pamaso pa Mulungu.

Kukhala chete mpemphero kumalimbikitsa kumvetsera.
‘Chifukwa chake mawu ako akhale owerengeka! Sitingalankhule ndi kumvetsera nthawi yomweyo. Pomwe tasiya kulankhula, timatha kumvetsera. Pomwe takhala chete, timayamba kumva phokoso lomwe lakhala lilipo kwa nthawi yaitali, koma sitimamva chifukwa tidalunjika pa zinthu zina. Pomwe mtsogoleri  akhala chete ndikosavuta kumvetsera. Ndi mochuluka bwanji momwe timamumva Mulungu?  Nthawi zambiri sitimamva chifukwa sitimaima ndi kumvetsera!
Atsogoleri otumikira amaphunzira kuti Mulungu nthawi zambiri amadikira kulankhula kufikira titakhala chete! Amafuna kudzipatsa okha mwambo pokhala chete ndi kumva liwu lake. Atsogoleri otumikira amaphunzira kumvetsera pokhala chete pamaso pa Mulungu.

Kukhala chete mpemphero kumalankhula malambiro.  
‘Pakuti Mulungu ali ku mwamba , iwe uli pansi.’ Pamene tikhala chete, timayamba kuzindikira kuti Mulungu ndi ndani ndipo kuti ife ndife ndani. Timaona ukulu ndi mphamvu zake. Ichi chimasintha momwe timadzionera tokha ndi ntchito yathu ya utsogoleri. Kuzindikira za chomwe Mulungu ali kumadzetsa kuwona kosiyana  ndipo kumatimasula ife nkuyamba kulambira Mulungu. Timagwada mkulambira. Atsogoleri otumikira amaonetsera kulambira pomwe mwakachetechete alowa mkupezeka kwake.
Nchachidziwikire, pali nthawi zambiri zomwe mawu ndi oyenera mpemphero. Yesu adapereka, ‘..mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misonzi…..’ (Ahebri 5:7). Koma ambiri a ife sitimavutika kulankhula, timavutika kukhala chete! Kukhala chete mpemphero sikophweka, ndikovuta. Atsogoleri otumikira amafuulira kwa Mulungu pofuna chisomo chake kuti chiathandize kukhala chete mpemphero. Amadzipatsa okha mwambo kutenga gawo la nthawi yawo ndi Mulungu mu chete.
Pomwe  atsogoleri otumikira akukula mukugonjera ndi kuphunzira kumvetsera, amapeza kuti kukhala chete kumathandizira kukusunthira chifupi ndi Mulungu mkulambira. Ndipo pomwe akukula, amachulukitsa kuchititsa kwawo ndi omwe akuwatsogolera. Utsogoleri wa chete umalankhula mofuula mpemphero! Atsogoleri otumikira amapita pamwamba potseka pakamwa!

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • Ndi ndani yemwe amalamulira zokambiranan zanga mpemphero: Mulungu kapena ine? Kodi izi zimakhudza bwanji ubale wanga ndi Mulungu? Zimakhudza bwanji utsogoleri wanga?
  • Kodi ndimamva liwu la Mulungu mowirikiza ndi momwe ndimafunira? Ngati ayi, kodi ndi chifukwa choti iye samalankhula kapena ine ndi amene sindimamvetsera? Ndi chani chomwe ndiyenera kusintha?
  • Nthawi zambiri timawunguza moyo wathu wa pemphero powona kuti timakhala nthawi yochuluka bwanji tikulankhula. Koma kodi ndi nthawi yochuluka bwanji yomwe ndimakhala chete ndi Mulungu? Kodi ndi yokwanira? Ngati ayi, ndi chani chomwe ndiyenera kusintha?  Ndi chani chomwe chimandipangitsa ine kuvutika kukhala chete mpemphero?
  • Anthu ena amapemphera ‘mwachinunu’ kutanthauza kuti samalankhula mawu omveka  kwa Mulungu, ‘amangolankhula ‘ kudzera mmalingaliro. Kodi zikutanthauza chani kwa munthu ameneyu pa zakukhala chete mpemphero?


Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatira chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembatsa mwaulere komanso kuwona magawo akale. Mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.  Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi Abusa Joseph Saizi, josephsaizi2017@gmail.com
 

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2021

Modify your subscription    |    View online