Okondedwa mzanga, Kachikena tili ndi mwayi okondwera pa Khrisimasi mphatso ya mtengo wapatali yomwe Mulungu adapereka kwa ife. Kubadwa, moyo, kufa ndi kuuka kwa Yesu kudasintha mbiri komanso miyoyo yathu. Chitsanzo cha utsogoleri chomwe Yesu adapereka chikupitilirabe kukhala chitsanzo kwa atsogoleri osawerengeka pa dziko la pansi. Chikondi chake cha nsembe, kutumikira kosadzikonda, kudzichepetsa kozama, kulimba mtima podzudzula, ndi kukhudza kodekha zikutiit anila tonse a ife kukudzipereka kwakukulu potumikira. Pomwe dziko la pansi likuvutika ndi mlili wa Covid-19 pamwamba pa kugawanika pa ndale, makangano pakati pa anthu, ngozi zodza kamba ka chilengedwe atsogoleri omwe amakhala, amakonda ndi kutsogolera ngati Yesu akufunika kuposa kale. Pemphero langa mu nyengo ya Khrisimasiyi ndi loti yense wa ife adzuke ndi kuchita chomwe tingathe mu gawo lathu la dziko la pansi polenga malo omwe anthu angathe kupita patsogolo. Ndikuyamikira kwambiri inu ngati awerengi a magawo awa ndi kuyembekezera kuti adzapitilira kukudalitsani mchaka chatsopano. Ndikuthokoza abusa Joseph Saizi kamba ka ntchito yawo yotanthawuzira magawowa yomwe amachita mwaulere ndi mtima owona. Chonde muyamike nane Mulungu kamba ka iwo! Khrisimasi yopambana! Ine wanu wa paulendo, Jon Byler
|