Gawo #323, January 31, 2024

Dzikolapansi Lokoma: Milingo Imafotokozedwa

Chilengedwe cha Mulungu chinali chopambana, malo okongola odzala ndi moyo ndi kukongola. Anthu analengedwa mwamtengo wapatali. Kusiyanasiyana muchilengedwa kunaikidwa, ndipo ntchito inali ya cholinga. Nyama,zomela,ndi anthu ankakhala moyo okoma pomwe ankakhala pamodzi mwaufulu. Mu kukhala motelomo, Mulungu anaika malamulo omveka bwino.

Genesis 2

16 Ndipo Yehova Mulungu analamula munthu uja kuti, “Uzidya zipatso za mu mtengo wina uliwonse mʼmundamu; 17 koma usadye zipatso za mu mtengo wodziwitsa chabwino ndi choyipa, popeza ukadzadya za mu mtengowu udzafa ndithu.”

Mulungu analenga dzikolapansi la ufulu, koma anaikanso malire, anaika Milingo ngati chophatikizila kukometsa dziko.Atsogoleri otumikila chimodzimodzi amafotokoza bwino Milingo Kwa omwe akuwatsogolera.

Milingo yofotokozedwa bwino imabweretsa kukoma povomeleza cholinga

Kodi Mulungu anaika bwanji choletsa ufulu omwe anampatsa Adamu? Kodi ankaduna kukaniza kunjoya pa Adamu pa chipatso chabwino? Funso limeneli linali pamtima pa mdani lomwe limabweletsa kugwa kwa munthu. Cholinga Cha Mulungu sichinali choletsa koma choulula malire. Mulungu ankafuna kuti Adamu akhale moyo okoma pokhala mkati mwa mulingo wa malire womwe anakhazikitsa. Adadziwa kuti kuphwanya mulingowo kubweletsa imfa, kutsutsana ndi moyo okoma. Atsogoleri otumikila amafotokoza Milingo ya malire ndi chifukwa chomwecho; amafuna dziko lawo likome. Cholinga chawo sichoti akanize ufulu koma kulimbikitsa moyo okoma.

Milingo yofotokozedwa bwino imabweretsa kukoma povomeleza zotsatila

Ngakhale chikhalidwe chathu chauchimo chimadana ndi kuuzidwa zochita,mkati mwathu timakhala tikuziwa kuti dziko lathu limakhalabwino ndi Milingo yoyenelera. Tili ndi malile a liwiro lapamsewu ndi malamulo a apolosi apamsewu pa cholinga chabwino. Tili ndi malamulo akhudzana ndi umbava omwe anapangidwa ndi cholinga chotiteteza ife ndi katundu wathu. Timamvetsetsa kuti mwana wa zaka ziwiri sangavutike ngati sadziwa tanthauzo la "ayi!" Mumadela momwe tikukhala, zimakhalabwino ngati pali kunvetsetsana kumodzi pa zochita zomwe ndi zovomelezeka kapena zosavomelezeka. Pomwe chikhalidwe chathu chakana mchitidwe wa kugawana milingo yamalire. Zimamveka mwamphamvu kunena kuti "chomwe ukuchiona kuti chikuthandiza utha kupanga" koma zotsatila ndi chisokonezo.

Chimodzimodzinso mmatchalitchi ndi mmabizinesi momwe milingo sinafotokozedwe bwino. Atsogoleri muutumiki amalingalira pa chikonzero cha Mulungu ndi kusakasaka kutsatila Milingo ya miyeso yofotokozedwa bwino mudela lawo la utumiki. Amakhala ndi masomphenya a magulu  amphamvu ochitabwino pomwe aliyense amagawana milingo yomweyo ndipo amakhala ndi choyankha ku Milingo imeneyo. Atsoleri muutumiki amazindikira chokhumba chamkati kuti ambiri akuyenela kufikila zomwe zikuyembekezeka kuti zichitike ndi Iwo. Choncho, amakweza zoyembekezekazo pamwamba ndi powonekela kuti anthu adzuke ndikuchitapo kanthu.

Milingo yofotokozedwa bwino imabweretsa kukoma povomeleza zoikamo

Atsogoleri muutumiki amavomereza udindo wawo ofototoza milingo kwa omwe akuwatsogolera. Izi kawilikawili zimaonetseledwa mu ndondomeko zomwe amazitsatila (ma  values) zomwe anazifotokoza bwino. Atsogoleri otumikila amalimbika kuti apeze ndondomeko zoti zizitsatidwa mubungwe lawo zomwe zimapeleka chithunzithunzi Cha bungwe lawo kuti ndilotani kwenikweni. Amalankhulana ndi gulu lawo za matanthauzo a ndondomeko zawo ndi kufotokoza za omwe  sakutsata ndondomekozo. Amakweza bungwe pofotokoza kuti milingo yamalile ndi iti ndipo aliyense, kuphatilizapo Iwo eni, akuyenela kutsatila milingoyo. Amabweletsa pamodzi zochita za onse pamodzi kuti abweretse kusintha,makamaka kusintha kwa khalidwe. Pomwe pali kunyalanyaza posaduna kusintha, mtsogoleri otumikila akhoza kumumasula munthuyo kuchoka mubungwe lawo. Amatumikila bungwe pofotokoza ndi kugwilitsitsa kutsatila Milingo.Popanga izi, anthu amakhala mokoma!

Zoti tilingalire ndi kukambirana:

  • Kodi cholinga chofotokozela bwino milingo ya malire yakhala ikuphwanyidwa bwanji mukuona kwanu? Lingalirani makamaka mmaganizidwe mudela Ili muchikhalidwe chanu, mubanja lanu, ndi mubungwe lomwe Inu mumatsogolera. Kodi kuganiza koteleku kwakhudza bwanji Inu ngati mtsogoleri? Munjila ziti zomwe mungakonze kaganizidwe kanu kuti mulingane ndi cholinga cha Mulungu?
  • Lingalirani momwe zotsatila zingakhalire ngati wina aliyense mubungwe lanu atamatsatila izi ndi kukhala motsatila ndondomeko za pabungwepo kapena milingo yoikidwa. Lembani mfundo zosachepela zitatu.
  • Kodi muzapangapo chani Inu ngati mtsogoleri kuti mufotokoze bwino mfundo kapena milingo yoikidwa munyumba mwanu, mubungwe kapena mudela mwanu? Kodi muchitapo chani kuti muzindikilitse aliyense mfundozi? Kodi mungakambe nkhani zotani zomwe zikuonetsela kuti ndondomeko sizikutsatidwa? Lembani ndandanda ziwiri kapena zitatu zomwe mutsate ndi madeti omwe muzachite zinthuzo.

Mpaka nthawi Ina ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona chokometsela china cha dzikolapansi lokoma: Maubale Alemekezedwa.

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2024