December 20, 2023

Moni Wa Khilisimasi 2023

Ndikufuna mu nthawi into ndikufunileni Inu,banja lanu ndi omwe mumawatumikila Khilisimasi yodalitsika.Munthawi imeneyi ya chaka timayamba taima Kaye kuti tikondwelele kubadwa Kwa Yesu yemwe anasintha mbiri yakale mu njira zambiri.Chitsanzo chake Cha kuvutika ,kudzichepetsa ndi kupereka moyo wake chifukwa cha ena zinationetsa njila yosiyana yapadeladela ya yotsogolera.Patatha zaka za kuwunikila ndi kulingalira komanso kudunafuna kutsatila chitsanzo chake,ndikutha kuona kuti pakadali zambiri zoti tiphunzire!

Ndikuchitenga  chamwai kuyenda ndi Inu pa ulendo wokhala ngati Iye.Ndikufuna ndikuthokozeni potenga nthawi yanu kuwerenga malingaliro amenewa Kwa chaka chapitachi.Ndipo Kwa onse omwe alimbikitsa ena kuti ayambe kulandila,ndakuthokozani kwambiri! Nthawi zonse, malingaliro anu komanso maganizo anu ndiolandiridwa omwe ndiothandiza kupititsa patsogolo kapena maganizo a mitu yomwe ingakhale yothandiza kwa Inu.

Ndikufunanso kuthokoza omwe amathandiza kuti zimenezi zikufikeni pa masabata awiri aliwonse.Linda Boll ndi Milonica Stahlwert omwe amaonetsetsa kuti zomwe ndalemba zilibwino.Brian Drewery yemwe amagwila ntchito ya makomputa kuti maphunziro onse azituluka ndikutumizidwa Kwa Inu.Ndipo Gabriel Mandrazo ndi Grace Kacheto omwe amapereka nthawi yawo mwaulele kumasulira zimenezi mu chiyankhulo Cha Spanish ndi Chichewa.Ndine oyamika chifukwa cha wina aliyense wa iwo.

Ndikukhulupilira muli ndi holiday ya khrisimasi yopambana!Ndikhala ndikupita ku Kenya chaka chino kukakondwelera Khrisimasi ndi akubanja Kwa mkazi wanga komwe ndikukhulupilira kuti mbuzi yamoyo sikalephela kufa mkati mwa phwando!

Ambuye akudaliseni pomwe mukupitiliza ulendo wanuwanu wa utsogoleri!

Ndine wanu chifukwa cha Yesu,

Jon Byler

Kuti muone maphunziro a m'buyomu, dinani apa.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2023