Gawo #318, November 1, 2023

Atsogoleri Muutumiki Amafunsa Omwe Akutsatira "Kodi Mukutani Chani Kuti Mutsilize Bwino?"

Atsogoleri Muutumiki amalingalira za mmene azatsilizile ndicholinga chozisungira chindunji chawo mumadela olondola. Koma mwachangu amabwela kuzatumikila omwe akutsogolera powalimbikitsanso kuganizira za kutsiliza bwino. Ngakhale atsogoleri amakhala patsogoloko kawilikawili mu ulendo wawo wamoyo, koposa omwe akuwatsogolera, amaganizila za mau a Paulo Kwa omwe akuwatsogoleranso.

2 Timoteyo 4

6 Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga. 7 Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro. 8 Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake.

 

Atsogoleri muutumiki amafunsa "Mukuchita chani kuti mutsilize bwino?" ndicholinga chosunga dipo mmalingaliro .

"Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthilidwa ngati nsembe..." Paulo sakubisa dipo la utsogoleri muutumiki, ndi kudzipeleka ndi kudzikhuthula. Utsogoleri si otchipa. Koma chindunji chake pa kutsiliza bwino zikupangitsa dipo kuperekedwabasi. Atsogoleri muutumiki amafuna kutulutsa zopambana Kwa omwe akuwatsogolera kotero kuti amafunsa kuzipereka kwatunthu. Amaitanira ena ku kukula kwa pa Iwo eni komanso mumaphunziro kuphatikizanso maudindo akulu akulu a udindo.Koma amazindikira kuti maudindo aakulu amafunika kudzipatsa mwambo kochulukanso, luntha, ndi chindunji. Pomwe akumvetsetsa kuti si onse ofuna kupereka dipo, amaitana omwe akutsatira kuti akhale ofuna kupereka dipo, amaitana omwe akutsatira kuti akhale ofuna kupereka dipo powafunsa kuti alingalire za utsogoleri wa nthawi yaitali osati wa nthawi yochepa.

Atsogoleri muutumiki amakumbutsa omwe akuwatsogolera kuti dipo akulipira lero lizabweletsa phindu pammawa.

 

Atsogoleri Muutumiki amafunsa "Kodi mukuchita chani kuti mutsilize bwino?" Kodi  mathero.

"Nthawi yakunyamuka kwanga yayandika." Paulo amazindikira kuti nthawi anali nayo inali yochepa. Koma anali ndi kutsimikizika kuti chifukwa moyo wake unali wabwino, amalizanso bwino. Anakhala moyo wake onse ndi malingaliro a chitsilizilo cha moyo. Anakhala akufuna kufa kangapo pogendedwa  ndi miyala, kukwapulidwa kuponyedwa mmadzi. Ndipo anadabwanso kuti anakhala moyo nthawi yaitali chomwechi! Chifukwa ankakhala ndi malingaliro a kutsiliza kwake ,sadaope mathero. Atsogoleri muutumiki amathandiza omwe akuwatsogolera kuti asunge mathero mmalingaliro mwawo.Pamene pali ntchito zoti agwire, atsogoleri muutumiki amafunsa mafunso okhudzana ndi mtsogolo. "Kodi ukuona kuti uzakhala ulipati zaka zisanu zikubwelazi?" Kodi zizaoneka bwanji ukapitilira kuchita bwino pa zaka Zina khumi zikubwelazi?" Kodi ukuchita chani kuonetsetsa kuti ubale wam'banja uzakhalebe wamphamvu mtsogolo?" Mafunso onga awa amathandizila otsatila kuti asamangowona za ntchito zomwe akugwira tsopano lero, koma pa zoti azakwaniritse mmawa.

Atsogoleri muutumiki amakumbutsa omwe akuwatsogolera kuti maphindu anthawi yaitali ndi ofunika koposa kuchitabwino kwanthawi yochepa.

 

Atsogoleri Muutumiki amafunsa "Kodi mukuchita chani kuti mutsilize bwino?" Kodi asunge mphotho mmalingaliro.

"Mphotho yanga ikudikila...." Paulo amatha kuona mtsogolo pa mphotho ya moyo wake omwe anakhala bwino. Kuona uku kunapangitsa ululu omwe "podzipeleka nsembe" kumafunikandithu. Anakwanitsa kutsiliza bwino posunga mphotho mmalingaliro. Atsogoleri muutumiki sataya kufunika Kwa mphotho yakanthawi kochepa. Koma amatumikira omwe akuwatsogolera powathandizira kukhala a chindunji ndichidwi pa mphotho ya nthawi yaitali akatsiliza bwino.

Atsogoleri muutumiki amakumbutsa omwe akuwatsogolera kuti mphotho yopambana kwambiri imabwela pa nthawi ya kutha kwa moyo omwe anakhalabwino padziko.

 

Zoti tilingalire ndi kukambirana:

  • Kodi ndikupempha omwe akunditsatira kuti apeleka dipo lotani?Kodi ndakhala owona mtima kuwauza dipo loti apereke kuti akule muutsogoleri?Kodi ndingalimbikitse bwanji omwe akukula kuti aganizile mozama za nthawi yaitali osati nthawi yaifupi?Kodi ndingachite nawo bwanji omwe asakufuna kupereka dipo la kukula?
  • Kodi ndikuchita chani kuthandiza anthu omwe akutsatira kuti akhale ndi chindunji ndi chidwi pa phindu la nthawi yaitali?Kodi ndizifunsa mafunso anji Kwa omwe ndikuwatsogolera kuti ndiwathandize kukhala ndichidwi Cha pa phindu la nthawi yaitali?Kodi ndikauza wina liti za izi?
  • Kodi utsogoleri wanga wakhala wa pa chidwi Cha phindu la nthawi yaifupi kapena nthawi yaitali?Kodi ndingasinge motani zofunikila zobweretsa mphindu la nthawi yochepa koma mbali inayi ndikuthandiza omwe ndikuwatsogolera kukhala ndi chindunji pa chomwe chimabweretsa mphotho ya moyo wawo onse pokhala bwino padziko?

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

 

Jon Byler,

 

Muphunziro lotsatirali, tiona pa mutu wina watsopano.

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2023