Atsogoleri Muutumiki samangofuna kuthamanga bwino kokha, koma akufuna kutsiliza bwino. Amayamba ndi chitsilizilo mmalingaliro mwawo ndikutsogolera ndi chitsilizilo mmalingaliro mwawo. Amaganizila tanthauzo la mau a Paulo olembedwa pafupi ndi kutha kwa moyo wake.
6. Pakuti ndapelekedwa kale ngati nsembe yamadzi,ndipo nthawi ya kunyamuka kwanga yayandika.
7. Ndalimbana nako kulimbana kwabwino,ndamaliza makani a liwiro, ndasunga chikhulupiloro.
8. Tsopano andisungila korona wa chilungamo,amene Ambuye,oweluza wachilungamo,azandipatsa pa tsiku limenelo_osati ine ndekha ,komanso kwa onse omwe akhala akulindilira kubwela kwake.(2Timoteyo 4:6-8).
Pomwe Paulo amalingalira za mathero a ulendo wake, anakwanitsa kulemba zinthu zitatu zomwe anakwanilitsa, "Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiliza njilayo, ndasunga chikhulupiloro." Atsogoleri muutumiki amalingalira za mau awa a mtsogoleri wamphamvu pafupi ndi kutha kwa moyo wake. Amaphunzila kwa chitsanzo cha Paulo ndipo amasunga chindunji chawo podzifunsa okha, "Kodi ndikuchita chani kuti nditsilize bwino?"
Atsogoleri Muutumiki amafunsa "Kodi ndikuchita chani?" Kuti aike chindunji chawo pa maitanidwe awo.
"Ndalimbana nako kulimbana kwabwino." Paulo molimbamtima akutsimikiza molimbamtima kuti watsiliza maitanidwe omwe Ambuye anampatatsa. Panali nkhondo zambiri mkati mwa njira. Koma Paulo anakhalabe pachindunji cha maitanidwe ake omwe Mulungu anampatsa ndipo sanalole zowononga kusuntha moyo wake kunjira zina. Pamapeto pake ananena molimbamtima kuti wakwanilitsa cholinga chachikulu chomwe Mulungu analinacho pa moyo wake ndi utsogoleri wake. Atsogoleri amaphunzira kwa Paulo kusunga chindunji chawo pa zokhazo zomwe akuyenela kuchita. Amazindikira za cholinga chawo chachikulu ndipo kutsatila izo ndimoyo wawo wonse. Mugulu kapena bungwe lomwe akutsogolera, amaika mphamvu zofunikira posunga cholingacho mkati mwa chochitika chilichonse. Atsogoleri amalingalira za mathero kuti asunge chindunji cha maitanidwe pa zochitika za tsiku ndi tsiku.
Atsogoleri Muutumiki amafunsa, "Kodi ndikuchita chani kuti nditsilize bwino?" kuti aike chindunji chawo pa anthu mmalo mwawo.
"Ndatsiliza makani aliwiro". Paulo wasuntha kanenedwa kake kuchoka pa nkhondo kufika ku liwiro lothamanga ndipo akunena kuti wathamanga mpikisanowo mpaka kumapeto. Ankadziwabwino kuti kusiyira mmanja mwa ena kuti nawonso alowe mpikisano waliwirowo chinali mfungulo pa liwiro. Paulo pomwe amaphunzitsa Timoteo ndi enanso amgulu lake, zinawakonzekeletsa kuti athamange liwiro. Kotero,akutha kunena "osati ine ndekha, komanso omwe akhala akulindila kubwela kwake." Paulo anadziwa kuti palibe kupambana pa munthu opanda olowa mmalo. Sanakhale ndimantha oti m'badwo wobwelawo suzakwanitsa kupitiliza, amali atawasula bwino kale. Kunena za mtsogoleri wachitsanzo, Paulo anakwanitsa "Kukweza nsanja" popeleka mphamvu kwa ena.Atsogoleri muutumiki amaganizila za kumaliza bwino kuti aike chindunji chawo pa m'badwo otsatila wa atsogoleri ozalowa mmalo. Atsogoleri muutumiki amalingalira pa matsiliziro kuti azikimbutse okha kuti palibe kupambana popanda olowammalo.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "Kodi ndikuchita chani kuti ndimalize bwino?" Kodi aike chindunji chawo pa ngodya.
"Ndasunga chikhulupiloro." Paulo anali otsimikizika pakutha kwa moyo wake kuti sanataye chikhulupiloro chale. Anakhala chomwe anaphunzitsa ndipo anatha kunena sanatenge njila yophweka kuti akuluke munyengo zake zovuta. Sanasinthanitse zomwe amayenela kutsata kuti ayende mofewa ndikupambana. Atsogoleri muutumiki amalingalira pa chitsanzo cha Paulo ndikuyang' ana pa mathero kuti asunge chindunji chawo Cha tsiku ndi tsiku mwabwino. Sapeleka mulingo wa kupambana kwawo poona kukula kwa chuma nthawi yopuma pantchito koma pa zochitika za tsiku ndi tsiku zomwe zimasunga ngodya zawo. Ndipo pomwe akusungangodya pambali "amakweza mbendela" ya omwe awazungulira. Atsogoleri muutumiki amalingalira za mathero kuti asunge chindunji chawo pa zinthu zomwe ndi ngodya zawo. |