Gawo #316, October 04, 2023

Atsogoleri Muutumiki Amafunsa Otsatila: "Kodi Mukutsatira Ndani?"

Atsogoleri muutumiki amapereka lingaliro lokhuzika kwa omwe akutsatira. Komanso amalingalira zomwe mavesi otsatilawa amatanthauza Kwa omwe amawatsogolera.

1 Akorinto 11:1

Tsatilani chitsanzo changa monga inenso nditsatila chitsanzo cha Khristu.

Afilipi 3:17

Abale, nonsenu pamodzi mudzinditsatira ine, ndipo inu muli ndi chitsanzo, phumzirani kwa amene akukhala moyo motsatira momwe timakhalira.

Paulo poyamba ndi otsatila, koma mwachangu akuuza ena kuti atsatire chitsanzo chake. Akufuna kuti ena asankhe bwino omwe akutsatira. Atsogoleri Muutumiki amafunsa omwe akuwatsogolera, "Kodi mukutsatira ndani?" Ndicholinga choti otsatila awo akule mukuthekela kwawo kotsatira.

Atsogoleri Muutumiki amafunsa, "Kodi mukutsatira ndani?" kuti apangitse kuzindikira.

Paulo akufotokoza momvekabwino kuti tizakhala tikutsatira winawake ndipo akulimbikitsa omwe akuwelenga kuti apange chisankho chabwino. Akudziwa kuti anthu ambiri salingalira mozama za omwe akufunsa kuwatsatira. Akhoza kutsatira omwe akumva Kwa anzawo. Akhoza kuona pa mauthenga a mmafoni, munyimbo kapenanso muzampila ndikuganiza kuti anthu otchuka kwambiri nde abwino kuwatsatira. Mosaganizila,moyo wawo ukusintha chifukwa cha omwe akuwatsatira. Atsogoleri muutumiki amafunsa omwe akutsatira kuti azilingalira mozama popanga chisankho pomwe akufunsa "Kodi mukutsatira ndani?" Ndi kuzindikilitsidwa mozama otsatila akhoza kuyamba kupanga zisankho zabwino za omwe angatsatire.

Atsogoleri Muutumiki amafunsa "Kodi mukutsatira ndani?" Kulimbikitsa chindunji.

Paulo akulimbikitsa omwe akutsatira Ikani maso anupa... Akukhumba kuti otsatila ake akhale ndi chindunji choonekabwino. Akumvetsetsa kuti malingaliro athu amatsatila maso athu, zochitika zathu zimatsatira maganizo athu, ndipo zizolowezi zathu zimatsatira machitidwe athu. Atsogoeri muutumiki amalimbikitsa omwe akutsatira kuti asunge chindunji cholondola pofunsa "Kodi mukutsatira ndani?" Atsogoleri Muutumiki amayang'ana mwayi oyika omwe akutumikira ngati zitsanzo zowonelapo mu bungwe lomwe amatumikila. Amaona izi "Omwe amakhala momwe timachitira" Ndipo pomwe apeza athu oterewa, amalimbikitsa ena kuti aziona pa Iwo. Pomwe mtsogoleri muutumiki sangadziwe komwe otsatila angaphunzilirepo, akhoza kugawana nawo izi pogwiritsa ntchito misonkhano, nthawi zina kupereka zitsanzo za omwe akupanga bwino.

Atsogoleri Muutumiki amafunsa omwe akutsatira "Kodi mukutsatira ndani?" Kuti awone umodzi.

Paulo akulimbikitsa otsatila ake kuti "abwele pamodzi mukutsatira..." Akuonapo kulumikizana pakati pa kutha kutsatira bwino ndi omwe atizungulira. Akukhulupilira mu mphamvu ya kukhala pamodzi kuti tiumbe chindunji chathu. Mtsogoleri aliyense amafuna chiyanjano Cha omwe angawalimbikitse ndi kuwabetchela kuti akhale bwino. Muli mphamvu mukutsatira limodzi, osati mu timagulu topatukana kapena topanga zosiyana, koma mumagulu a ena omwe amakhala mu zikhulupiliro zimodzi ndi masomphenya amodzi. Atsatira amafuna chiyanjano chimodzi ndipo atsogoleri muutumiki ali ofuna kuwafunsa osati funso loti akutsatira ndani likha komanso kuwathandiza kuganiza za omwe asankha owazungulira pomwe akutsatira.

Mtsogoleri muutumiki amamvetsela bwino kumayankho amafunso amenewa kuti amunvetsetse bwino munthu ndiponso kuti adziwe mmene angawatumikilire bwino. Ndipo monga Paulo, mtsogoleri muutumiki sakhala omangika kuuza ena kuti awatsatile chifukwa nawonso amatsatila bwino!

Zoti tilingalire ndi kukambirana

  • Kodi ndifunse munthu wanji kapena anthu anji, "Kodi mukutsatira ndani?" Ndipo ndipange izi nthawi iti?
  • Nditatha kukamba nawo lingalirani pa mafunso otsatilawa kuti muone bwino zomwe munanva.
  • Kodi ndinaphunzila chani za omwe ndikuwatsatira?
  • Kodi chinandidabwitsa ndichani muzokambiranazi?
  • Kodi mayankho awo asintha motani njira yomwe ndimatsata powatsogolera? Kodi ndichitepo kanthu liti?
  • Kodi nditsate ndondomdko ziti kuti ndiwalimbikitse kutsatira bwino?
  • Kodi ndine omasuka kuzipereka ndekha ngati chitsanzo chabwino kwa ena? Kodi izi zingakhudze bwanji utsogoleri wanga?

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2023