Gawo #315, September 20, 2023

Atsogoleri Muutumiki Amadzifunsa Okha: "Kodi Ndikutsatila Ndani?"

Atsogoleri amatumikila! Amaikiza zinthu mwa ena pomwe akuganiza, kulota komanso kupanga mapulani. Komanso amatsatila ndipo amaikizidwa zinthu ndi ena. Izi zimachitika pomwe akuwelenga mabuku, zokambilana zomwe analinazo amanvela. Atsogoleri Muutumiki amaonetsetsa mosamala omwe akuwatsatila. Amalingalira za nzeru zomwe zili mu mavesi awa:

1 Akorinto 11:1

Tsatilani chitsanzo changa monga inenso nditsatila chitsanzo Cha Khristu.

Miyambo 13:20

Oyenda ndi anthu a nzeru nayenso adzakhala munthu wanzeru; Koma oyenda ndi zitsiru adzapwetekeka.

Zimatengela yemwe atsogoleri akutsatira! Atsogoleri Muutumiki amadzifunsa okha funso; "Kodi ndikutsatila ndani?" kuonetsetsa kuti ali oyenela kufunsa ena kuti awatsatile.

Atsogoleri Muutumiki amafunsa, "Kodi ndikutsatila ndani?" Kuonetsela kudzichepetsa kopitilira.

Paulo akufunsa ena kuti amutsatile "Monga ndikutsatila... Khristu." Akukwanitsa kuitana ena kuti amutsatile chifukwa nayenso ndi otsatila wabwino. Akuonetsela kuti matsatidwe ndi oyambilira utsogoleri usanafike. Atsogoleri omwe akuona kuti sakutsatila wina aliyense atha kunena kuti "Ine ndimunthu odzipanga ndekha." Amalankhula za omwe amawatsatila ngati mulingo wa kufunikila kwawo muutsogoleri. Atsogoleri otelewa ndi oumamtima ndi opusa! Atsogoleri Muutumiki amatsogilera komanso amazindikira kuti atsatire. Modzichepetsa amazindikira kuti malingaliro awo ambiri, mfundo ndi khalidwe zimatengedwa kuchokela Kwa ena. Amazindikila kuti ngakhale angatsegule bungwe latsopano kapena bizinesi, akumanga pamapewa a ena omwe anapita Iwo asanabwele ndipo aphunzira kuchokera Kwa omwe awazungulira. Amamvetsetsa kuti ngati saphunzila kutsatira moyenera, sangaitane ena kutsatira moyeneranso. Atsogoeri Muutumiki amadzifunsa okha omwe akutsatira kufuna kuonetsetsa kuti akukhalabe ophunzitsika ndi odzichepetsa. Amakhala ndi chindunji kwambili ndi omwe akutsatira koposa ndani akutsatira.

Atsogoleri Muutumiki amafunsa , "Kodi ndikutsatila ndani?" Kuonetsetsa kukula kopitilira.

Chapamtima Cha atsogoleri muutumiki ndi kukula kuzikuza Iwo Eni. Amawelenga mabuku, kumvetsela zoulutsidwa pawailesi, amapeza kholo muuzimu, komanso amatenga nawo mbali kumaphunzilo a masemina. Amazindikira kuti kukula kwawo kumakhudza Iwo omwe akuwatsatira. Amazindikira madela omwe Iwo eni akufunika akule ndikusakasaka anthu omwe angawatsatile kuti awathandizile kukula mudela limenelo. Komanso atsogoleri muutumiki amaonetsetsa kuti akukula mudela loyenela. Miyambo akutiuza motsindika kuti omwe timachezelana ndi kulumikizana nawo amakhudza chomwe tingakhale. "yendani ndi anzeru ndipo mukhale wanzeru" Atsogoleri Muutumiki amafunafuna atsogoleri owaposa omwe samangoonetsela kuthekela kokuza madela omwe akufunsa akule komanso awonetsenso khalidwe lomwe akufunsa atengele. Amafuna atsatire omwe ali ndi nzeru osati omwe amangooneka ngati akuchitabwino. Atsoleri muutumiki amaumba kukula kwawo posankha omwe akumutsatila.

Atsogoleri Muutumiki amafunsa, "Kodi ndikutsatila ndani?" kuonetsetsa kupitilira Kwa zotsatira

Paulo akuuza ena, "tsatilani chitsanzo changa monga inenso nditsatila." Akuzindikila kuti akakhala otsatila wabwino, aikizanso mu miyoyo ya ena. Pomwe modzichepetsa akuvomeleza kuti nayenso ndi otsatila, ali ndi kulimba mtima kouza ena kuti atsatire. Atsogoeri amamvetsetsa kuti sangauze ena kuti atsatire bwino pokhapokha nawonso atsatira bwino. Akufuna kukhala ndi kuikiza ndi kusinthanso miyoyo ya ena, kotero amadzifunsa okha yemwe akumutsatila asanauze ena kuti atsatire.

Zoti tilingalire ndi kukambirana:

  • Kodi pakadali pano omwe akupanga zinthu zamphamvu zomwe zingasithe kuganiza kwanga, zochitika zanga, ndi kutsogolera kwanga ndi ndani? Kodi ndasankha anthu amenewa mwadala kapena izi zinangochitika mosaganizira? Kodi ndikukhutila bwanji ndi anthu omwe ndawaika pandandanda kuti nditsatile? Kodi ndisinthe pati?
  • Kodi ndimunjila ziti zomwe utsogoleri wanga, ngati zilipo, utsogoleri wanga ukuonetsela kuti sindine "mtsogoleri-ozipanga ndekha?" Kodi poyela ndimalemekeza ena omwe akuikiza zinthu mmoyo mwanga? Kodi mwachangu ndimalemekeza ndikutsata nzeru zomwe ndimapeza mukuwelenga, kupanga nawo masemina, ndizina zotero
  • Kodi ndi mmagawo ati omwe ndikufunika kukula kwambili? Kodi ndianthu onga ati omwe ndingaphunzire Kwa Iwo mudela lopelewelari? Kodi miyoyo yawo ndikhalidwe lawo ndi chitsanzo chabwino kwaine? Kodi ndindondomeko ziti ndingatenge kuti ndiwatsatire?
  • Kodi ndimafunsa ena kuti anditsatile ndisanadzifunse ndekha yemwe ndimatsatira? Kodi zimenezo zakhudza bwanji utsogoleri wanga? Kodi ndikufunika kusintha nditatha kulingalira mozama za Ichi?

Mpaka nthawi Ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tiona funso atsogoleri muutumiki amafunsa ena, "Kodi mukutsatira ndani?"

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2023

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online