Atsogoleri muutumiki amatenga nthawi yoganiza, komanso amalingalira pa zomwe Paulo analemba kwa omwe akutsatila.
Afilipi 4
8 Potsiliza, abale, muziika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosilirika.
Atsogoleri muutumiki amazindikila udindo wawo yoganiza kenako ndikuonanso kwa omwe akutsatila.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "Kodi mukuganiza chani?" Kuti alimbikitse Kuganiza.
Atsogoleri ena amayembekezela kuti ndi Iwo okha omwe amatha kuganiza; otsatila amangochita zomwe auzidwa. Koma atsogoleri muutumiki sakhutitsidwa ndi anthu omwe amangochita zomwe auzidwa osaganizapo. Amafuna kukuza kuthekela koganiza kuli mwa omwe akuwatsogolera. Cholinga chawo sikukuza otsatila, koma kuuza atsogoleri ambiri oganiza! Amafufuza za zomwe akuganiza pofuna kuonetsetsa kuti akuganiza. Funso limalimbikitsa kuganiza kwambiri. Kukhala ndi oganiza ambili mubungwe ndi kupambana kwa onse!
Atsogoleri muutumiki amafunsa "mukuganiza chani?" Kuti ayike poyela kuganiza.
Atsogoleri muutumiki amafuna adziwe zomwe otsatila awo akuganiza. Ndipo pamene akumva mayankho, amaphunzila kuchokera kwa iwo komanso amawaphunzila. Ganizo lochokela kwa otsatila kutha kupeleka kaonedwa katsopano ka zinthu kwa mtsogoleri yemwe kawirikawiri amaona zinthu mosemphana. Mtsogoleri yemwe akutumikila atha kukhala ndi zolinga zabwino, koma osamvetsetsa kuti zomwe akuchitazo zimakhuza motani omwe ali oyambilira kuchita mfundo zatsopanozo. Kumphunzila zomwe otsatila amaganiza zikhozanso kuthandiza mtsogoleri otumikila kumvetsetsa kuti chatsopano chofunika kuchitika ndi chani kwa munthuyo. Anthu ambiri sagawana zomwe akuganiza pokhapokha atadziwa kuti mtsogoleri wawo Akufuna kudziwa zomwe akuganiza. Atsogoleri muutumiki amanena mpmvekabwino kuti akufuna kudziwa zomwe ena akuganiza. Amanvetsela mwachidwi kwa omwe amawatsatira ndipo amalingalira za kufunika kwa zomwe akuganiza.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "Mukuganiza chani?" Kuti akulitse kuganiza.
Atsogoleri muutumiki sachitamantha ndi ena omwe amaganiza! Mmalo mwake,amakhala ndizolinga zofunafuna kukuza kuthekela kuganiza kwa ena. Amafunsa otsatila, "Kodi mukuganiza chani?" Kuwathandiza kukula. Mwadaladala amakokela Atsogoleri omwe akuwakuzawo kwa atsogoleri ena omwe akuganiza mchipinda pamodzi. Otsatila amaphunzila kuganiza pomwe akuona ena mmene akuthanira ndi nkhani zokhuza utsogoleri. Pomwe akumva kaganizidwe ka atsogoleriwo, kaganizidwe ka atsopanowo kamakula. Ichi ndi chipambano kwa mtsogoleri muutumiki ndi yemwe akutsatila, onse amakula pamodzi pomwe mafunso oyenera afunsidwa!
Tengani kamphindi lero kufunsa wina yemwe amatsatira utsogoleri wanu, "Kodi mukuganiza chani?" Kenaka mumvetselebwino ndikukula mukuganiza kwanu kuti muwatumikire bwino. |