Atsogoleri amagwila ntchito molimbika ndipo amapanga zithu kutheka.Iwo ndi anthu ochitapo kanthu! Koma atsogoleri amphanvu amazindikilanso kuti kuganizia za ntchito yawo ndi mbali ya ntchito yawo. Amazindikila kuti zomwe amaganiza zimakhudza zomwe amachita. Paulo akuwabetchela atsogoleri kuti akhale ndi chidwi Ku cholinga cha kaganizidwe kawo.
Afilipi 4
8 Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka.
Paulo akutilangiza kuti "tiganize za zinthu ngati zimenezo" Atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha "Kodi ndikuganiza chani?" pa zifukwa zingapo.
Atsogoleri Muutumiki Amadzifunsa "Kodi ndikuganiza chani"? kuti tizikhala ndi nthawi yoganiza.
Paulo akutiitanila ku kuganiza za kaganizidwe kathu! Akufuna awonetsetse kuti tizipeza kanthawi koganiza. Pomwe kuganiza sikumaoneka ngati ntchito yogwilika, atsogoleri muutumiki amazindikila kuti nthawi yoganiza siyopanda phindu, ndipo simangopita padela. Atsogoleri akuyenela kuima kaye ndikuganiza. Akuyenela kubwelela mbuyo ndi kuona mmene zilili. Akuyenela kuona zambuyo, kuona mmene zilili panopa ndi kuona zamtsogolo. Amadzifunsa okha choyamba, "Kodi ndikuganiza?" Atsogoleri muutumiki amazindikila kuti utumiki sikungogwila ntchito kokha. Amayamba achoka kaye pantchiptopo ndikuganiza za ntchito yawo.
Atsogoleri muutumiki amadzifunsa "Kodi ndikuganiza chani", kuti akhale ndichindunji cha nthawi yoganiza.
Paulo akutiuza kuti tiganizile pa "zinthu izi" Akupeleka ndandanda wazinthu zomwe "ndizapamwamba komanso zotamandika" kuganiza nthawi yoganiza ndizofunika,koma ngati cholinga cha nthawi yoganiza chili munjila yolakwika, ndizosapindulitsa. Sinthawi yonse yakuganiza ili yofanana. Pali madela ena amene mtsogoleri muutumiki akhoza kuganiza zokhudza iye zomwe zitha kubweletsa phindu lochuluka kubungwe. Zimenezi zitha kukhala kuganiza za mtsogolo, kuonanso zanjila zomwe angapelekele ntchito kwa anthu ndimaudindo moyenela, kuonanso gawo la mmene akuyendetsela utsogoleri wake ndi momwe kusintha mmene zikuyendela zingakhuzile njila yomwe bungwe likutenga, Kuganiza za njila zokwezela magawo oyendabwino,ndi zina zotero. Atsogoleri muutumiki amaika chidwi cha kaganizidwe kawo pa zinthu zomwe zimabweletsa zotsatila zabwino.
Atsogoleri muutumiki amadzifunsa, "Kodi ndikuganiza chani?" Kuti afotokoza nthawi yawo yoganiza.
Atsogoleri muutumiki amaganiza za kaganizidwe kawo kuti akhoza kufotokozela ena za zomwe akuganiza. Amatumikila amena akuwatsogolera pogawana nawo zinthu zomwe Iwo akuganiza. Mwadala amagawana nawo zomwe akuganiza ndipo ndichifukwa chani akuganiza choncho. Onse omwe amanva zomwe mtsogoleri akuganiza amapindula Ku kunvetsetsa bwino mtima ndi malingaliro a mtsogoleri ndi njila yomwe akuyendela. Amaphunzilanso momwe atsogoleri amaganizila zomwe zimakwezanso kaganizidwe kawo. Ena omwe amanvetsela amasula maganizidwe a mtsogoleri ndipo amabweletsa maganizo owonjezela zomwe zimakweza kuganiza. Ena mubungwe amayenela adziwe zomwe mtsogoleri akuganiza kuti athandize kugwila ntchito zimene zikufunika. Atsogoleri muutumiki samangoganiza; amatumikila magulu awo powafotokozela zomwe akuganiza.
Tengani mphindi imodzi yoti mulingalire za zinthu izi! |