Monga tinaonela muphunzilo lapitali atsogoleri muutumiki amaziunika myoyo yawo kuti aziwone ngati ahoza kuyamba kupanga zinthu zatsopano. Komanso amatsatila malamulo a Paulo ndi malingaliro a otsatila awo.
Aefeso 4
22 Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; 23 kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; 24 ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.
Paulo akuwuza aliyense "valani munthu watsopano" ngati choyenela kuchita mukukhala chomwe tinalengedwela kuti tidzakhale. Pali maluso atsopano amene akuyenela kukuzidwa, zizolowezi zatsopano zoti zipangidwe ndi machitidwe atsopano omwe akufunika kutengedwa. Atsogoleri muutumiki akupitilila kusakasaka njila zokwezela anthu awo. Awona kale madela omwe akuyenela "kuvulidwa" kapena kulekedwa. Akapeza zinthu zimene otsatila akuyenela kusiya kuchita, nthawi yomweyonso pali ufulu ofunsa chomwe chingayambilire. Amakhumba kukula ndi kutukuka kopitilila kwa omwe amawatsogolera! Ndi chimenechi mmalingaliro awo, atsogoleri muutumiki amafunsa omwe akuwatsogolera, "Kodi uyambe kuchita chani?" Kulimbikitsa zimenezi kuti zichitike.
Atsogoleri muutumiki amafunsa, "Kodi uyambe kuchita chani?" Kuti mbali yawo izindikilike ndikukuzidwa.
Atsogoleri muutumiki mopitilira amaika pasikelo magulu awo kuti kuthekela kwa aliyense kukuzidwe. Amafunsa aliyense payekha, "Kodi pali zinthu zomwe ungayambe kuchita zomwe zili mbali yako kwambili?" Izi zitha kuyamba pang 'onopang' ono tsikulili lonse kwa mphindi 30 mudela latsopano la udindo omwe ukugwilizana ndi mbali ya aliyense. Kapena likhoza kukhala dela latsopano kwathuthu kapena kusintha ntchito yonse ndicholinga choti dela lomwe Iwo amatha kuchita bwinolo lifike pooneka ndithu. Chindunji chatsopanochi chimabweletsa chidwi ndi kulimbika pa ntchitoyo ndipo zimapeleka phindu lalikulu kugulu lonse. Atsogoleri muutumiki amaika chindunji pa kukuza kuthekela kuli mwa anthu osati kukonza zolakwika.
Atsogoleri muutumiki amafunsa, "Kodi uyambe kuchita chani?" Kuti achulukitse utsogoleri.
Atsogoleri muutumiki amafunafunanso njila zopititsila omwe akuwatsogolera Ku milingo yopitilapiltila patsogolo ya utsogoleri. Chidwi chawo sichili pa "kungowakweza chabe" kukhala atsogoleri mubungwe, koma kuchulukitsa kukhwima ndi kuthekela kwa Iwo amene amatsatila Moonamtima.
Amafuna omwe akuwatsogolera apitilize kukuza "watsopano mwaiwo". Choncho, atsogoleri muutumiki amafunsa mafunso ngati kodi pali ntchito mubungwe zomwe mungakonde kudzakhala mtsogolomuno tsikulina? Kodi mungatsate njila zanji zomwe zingathandize kukonzekela udindo umenewo? Kodi ndi ntchito zatsopano ziti zomwe mungaonjezele pa zomwe mukugwila pano zomwe zingakonzekeletse pa udindo watsopano mukufunawo? Kodi pali njila zomwe ndingathandizepo? Pongofunsa mafunso amenewa chabe, mtsogoleri amapatsa kuganiza otsatila ndikumpangitsa kulingalira zambuyo, zonsezitu ndi mbali yokuza munthu. Atsogoleri muutumiki saona kuchitabwino kwawo pa mmene utsogoleri wawo wafikila, koma pa momwe omwe akuwatsogolera akulila ndikufikila.
Atsogoleri muutumiki amafunsa, "Kodi uyambe kuchuta chani?" Kuti akwanilitse masomphenya.
Atsogoleri muutumiki mopitilila amalumikiza udindo wa aliyense payekhapayekwa mu bungwe kumasomphenya amene bungwelo likuyendela. Ndipo mwakawilikawili amafunsa otsatila awo, "Kodi uyambe kuchitachani chomwe chizathandizile ife kukwanilitsa cholinga chathu chachikulu?" Pofunsa funsoli, Malingaliro atsopano azatulutsidwa ndipo kwa otsatilayo adzachitenga pamtima pake mozama molingana ndimasomphenya ndi udindo womwe alinawo opangitsa kuti zitheke.Atsogoleri muutumiki amakokela ena Ku kupangitsa masomphenya kutheka munjila zomwe zizalimbikitsa kukhuzika mumtima ndi umwini wa masomphenya.
|