Gawo #311, July 12, 2023

Atsogoleri Muutumiki Amadzifunsa Okha: "Kodi Ndiyambe Kupanga Chani?"

Atsogoleri kawirikawiri amakuza mapulani ndi njila zomwe angatsatile kuti akwanilitse ndipo amayamba kuthamanga molunjika  ku cholinga. Koma atsogoleri muutumiki samafunsa chomwe angachite, koma chomwe akuyenela kuyamba kuchita. Amatsatanso mosamala malangizo a Paulo.

Aefeso 4

22 Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; 23 kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; 24 ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.

Paulo akulankhula poyamba za chomwe chikufunika "kuchivula" kapena kuchisiya.Tinaonapo kale pa izi ndi funso loti "kodi ndisiye kupanga chani? Pomwe zinthu zikuyendabwino mu dela limeneli, atsogoleri muutumiki tsopano ali ndi malire munthawi yawo ndipo akhoza kupita Ku malangizo a Paulo" kuvala umunthu watsopano" pofunsa funso linanso paokha, "Kodi ndiyambe kupanga chani?" Atsogoleri muutumiki ayambe(kapene kuposela mu) madela osachepela atatu.

Nthawi zonse nkoyenera kufunsa ...ndi kupangapo mochuluka mu madela atatu...

Atsogoleri muutumiki amafunsa "Kodi ndiyambe kupanga chani?" Kuti chindunji chawo chikhale pa kutsogolera mmalo mwa kuchita.

Atsogoleri onse amadzuka kukhala atsogoleri chifukwa amachita bwino madela okwanilitsa ntchito, amadziwa mmene angachitile kuti ntchito itheke! Koma pamene atsogoleri muutumiki adzuka  mu utsogoleri, amazindikila kuti akuyenela kuyamba kuika chindunji chawo pa kutsogolera ena mmalo mogwira ntchitozi. Kusuntha mmaganizidwe ndikofunikila kuti iwowo atule pansi "zida" zomwe anaphunzila kugwiritsa ntchito bwino  ndi kukhala achindunji potsogolera ena bwino. Paulo akukamba za kusintha "kaganizidwe ka mmalingaliro" asanalankhule za zomwe zikufunika "kuvala". Pomwe Atsogoleri muutumiki asiya kugwira ntchito okha, amayamba mochuluka ntchito yautsogoleri. Amatenga nthawi yambiri kugwilra ntchito pa kampani kuposa mu kampani. Atsogoleri muutumiki amayang'ana kalendala yawo kuti asiyanitse nthawi yomwe amatenga kutsogolera ndi nthawi yomwe amatenga kugwira ntchito. Kenaka amasintha kalendala yawo kufikila ataika chindunji chawo pa kutsogolera bwino.

Atsogoleri muutumiki amafunsa "kodi ndiyambe kuchita chani?" kuti zichita zomwe zimabweletsa phindu lochuluka.

Atsogoleri amphamvu amazindikila kuti si machitidwe onse amuutsogoleri amabweletsa zotsatila zofanana ku bungwe lawo. Pomwe asiya kupanga zinthu zina zomwe sizimabweletsa phindu, amatha kuyamba kupanga zinthu zambiri zomwe zimabweletsa kuzintha kwakukulu. Mtsogoleri otumikila angathe kuzindikila kuti kuganiza mwamasomphenya ndi chimodzi mwa zinthu zabwino zomwe angachite pa bungwe, ndipo amayamba kuika padela nthawi yapadela yoganiza. Wina akhoza kukhala ndi lingaliro loti kuchita bwino kwawo muutsogoleri ndi pomwe akusunga masomphenya mwabwino ndi mwachindunji ndi momvetsetseka bwino. Zotsatila zake, amayamba kupititsa nthawi yochuluka pa kugwila ntchito yofotokoza masomphenya Ku bungwe. Atsogoleri muutumiki amagwira ntchito molimbika kuti athane ndi zakumtima kwawo  ndipo amayamba kuchita zomwe ndi zofunika koposa zonse.

Atsogoleri muutumiki amafunsa "Kodi ndiyambe kuchita chani?" Kuti akuzebwino mphatso zawo.

Pomwe atsogoleri aphunzila kunena kuti 'ayi' ku madela omwe simphatso yawo kapena madela omwe akuyenela kupeleka kwa ena kuti agwile, amapeza kuti akutha kuika chindunji chawo mu madela omwe ali mbaliyawo. Izi zikusonyeza kuti azachita zambili za zomwe Iwo amatha kuzigwilabwino. Atsogoleri muutumiki amayambanso mwadaladala kukuza mphatso yawo. Izi zimachitika pomwe ayika padela nthawi, osati yoti ayesele kuthekela kwawo, koma kupititsa patsogolo kuthekelako. Amatenga nthawi yawo powelenga za madela omwe iwo amachitabwino, kulankhula ndi phungu wawo odalilika, ndi kuphunzila kwa ena omwe anapambana mu gawo limenelo. Amatenga nthawi yokuza mphatso yawo.

Zoti tilingalirepo ndi kukambirana

  • Ndisanayang'ane pa zomwe ndikufuna kuyamba kuchita, kodi ndaleka zinthu zomwe sindikufunika kumazichita kuti ndikhale ndi mpata wa madela ena okula? (Ngati sichoncho,bwelelaninso kuona maphunziro ambuyomu!)
  • Kodi munthawi yanga pannopa mbali ya utsogoleri ndiyochuluka motani ndipo nthawi yopita pogwirantchito ndi yochuluka motani? Kodi zingandithandize ndiziti panopa mu udindo wanga? Kodi ndichitechani kuti ndiyende molunjika cholinga?
  • Mu zonse ndimachita ngati mtsogoleri, kodi ndi zinthu zitatu kapena zinayi ziti zomwe zimabweletsa phindu lalikulu ku bungwe langa? Kodi ndichitechani kuti ndiyambe kuchita zinthu izi mochuluka?
  • Kodi ndi dela liti lomwe ndimalichicha bwino lomwe ndingayambe kuika chindunji ndi kulikuza? Kodi nditsatile ndondomeko ziti kuti ndikuze dela lomwe ndimatha kuchitabwino? Ndiyambe liti?

 

Mpaka nthawi ina, ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

 

Munkhani yotsatila, tiona za funso lofananilako lomwe atsogoleri muutumiki amafunsa ena: "Kodi uyambe kuchita chain?"

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2023

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online