Atsogoleri ndi anthu omwe amachitapo kanthu ndipo ambili mwa Iwo Ali ndi ndandanda wautali wa zinthu zomwe akonza kuti achite kuti asinthe dziko lawo.Koma Atsogoleri muutumiki amaimikanso kaye ndikudzifunsa okha zomwe akuchita zomwe akuyenela kuti aziimike kaye!
Paulo akupereka malangizowa kwa Akhristu onse;
Aefeso 4
22 Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; 23 kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu.
24 ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.
Malangizo a Paulo akutiuza ife kuti mbali imodzi ya kukula mu chikhristu chathu ndi kusiya kupanga zinthu zina ndi kuyamba kupanga zinthu zina. Akupereka zitsanzo zingapo mu mavesi otsatilawa (25 -32) siyani bodza, yambani kunena zoona; siyani kuba, yambani kugwila ntchito kuti mudalitse ena; siyani kukamba zonyansa, yambani kukumana ndi zosowa za ena ndi lilime lanu. Pomwe machitidwe amenewa amagwilizana ndi kukula moyo wauzimu, Atsogoleri muutumiki amaphunzila kuyang'ana machitidwe awo kuti awone zoyenela "kuzichotsa" kapena kuzisiya.Amapanga izi pa zifukwa zitatu.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "Kodi ndisiye kupanga chani?" Kuti awone zoyambilira kupanga.
Kulamula kwa Paulo kuti "tichotse" zikukhudza zinthu zomwe nthawi zonse zimakhala zoipa kuzichita. Machitidwe olakwika chilungamo chake asiyidwe! Atsogoleri, komabe, kawilikawili amakumana ndi kakasi wapadelalela. Pa zinthu zingapo zabwino zomwe zikadachitika, Kodi ndichite chiti? Atsogoleri muutumiki amaphunzila kusiya kupanga zinthu zina ndicholinga choika chindunji chawo pa zinthu zomwe ndi zofunikila koposa zina. Amati "ayi" kuzinthu zomwe sizikufunikila kwenikweni ndi kuti "inde" Ku zinthu zomwe ndi zofunika kwambiri. Amazindikila kuti kutumikira ena kawirikawiri kumatanthauza "ayi".
Atsogoleri muutumiki amafunsa "Kodi ndisiye kupanga chani?" kuti achulukitse phindu.
Atsogoleri muutumiki amazindikila kuti ali ndi malile ndi nthawi yawo. Sangapitilize kupangila pangilabe zinthu. Pomwe zochita ndi maudindo zikuchuluka zimakhala zovuta kukhala ndichidwi pa ntchito yomwe ilipo ndipo phindu limachepa. Atsogoleri omwe amapitiliza kumangolandila maudindo kapena ntchito zina zisanathe amazigwetsa okha mukuzunzika komangogwilabe ntchito. Posakhalitsa amatopa kuthupi ndi muubongo ndipo sakwanitsa kutulutsa zabwino pa ntchito yogwilikayo. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kuyang'ana pa ntchito zawo pafupipafupi ndi kufunsa zomwe atha kuzisiya kupanga. Ngati ntchitoyo siyofunika kugwiridwa, amangoisiya. Ngati kofunika kugwira Koma igwiridwe ndiwina, amapereka kwa ena. Pomwe Atsogoleri muutumiki asiya kupanga zinthu zomwe samayenera kuzichita, amatha kupindula Ku zinthu zomwe ayenela kumazichita.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "Kodi ndisiye kupanga chani?" Kuti apatse mphamvu ena.
Atsogoleri kawirikawiri amachita zinthu zambiri zomwe ena akadazigwira akadazigwira bwino. Amazilungamitsa pamachitidwe awo ndi mfundo zothyakuka bwino zomwe zimawachitila ubwino, akugwirantchito molimbika ndipo zochita zawo ndi mbali imodzi ya ntchito zomwe anapatsidwa kuti azigwira. Koma Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti akapitiliza kuchita zinthu zomwe ena amugulu mwawo akanatha kuchita, samangoonetsela kufunikila ndikuthekela kwa Iwo eni Koma amafuna kuti ena akule ndikutukuka. Pomwe akaniza ena mwayi okula , atsogoleri amaziika okha mu malo opanikizika a udindo osatha. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kudzifunsa okha chomwe ayenela kusiya kugwira kuti azindikile madela omwe angapatsile ena. Amakhala odekhabwino kufunsa funso, ndikupanga dongosolo la kupatsila ena ntchito kwa bwino. Ngati maphunziro akufunika, amaika zimenezi pa ndandanda "wazoti zichitidwe". Atsogoleri muutumiki amaphunzila kukhala ndi ndandanda "wa zosafunika kuchitidwa" motsatana ndi "zoti zichitidwe."
|