Atsogoleri muutumiki amakhala ndikukhudzika, osati pa za kukula kwawo kokha, koma akufuna kuonanso omwe akuwatsogolera akukulanso. Ali pa bizinesi yokuza anthu! Choncho, amalabadila za kukula kwa iwo okha ndipo mwachangu amatembenuza chidwi chawo Ku kukula kwa omwe akuwatsogolera. Amakhala ndi masomphenya ochoka kwa Mulungu oti afikile dziko lawo ndipo amadziwa kuti sangakwanitse izi pawokha. Amaitana gulu kuti liwathandize, ndipo gululi limafunikila kuti nalo lizikula ngati likufuna kuzachita zamphamvu. Amakhala ndi kuona kofanana kwa omwe akuwatsogolera monga olemba buku la Ahebri analembala.
Ahebri 5
11 Tili ndi zambiri zoti tinganene pa zimenezi, koma ndi zovuta kukufotokozerani chifukwa ndinu ochedwa kuphunzira.
12 Ngakhale kuti pa nthawi ino munayenera kukhala aphunzitsi, pakufunikabe munthu wina kuti abwerezenso kudzakuphunzitsani maphunziro oyambira a choonadi cha Mulungu. Ndinu ofunika mkaka osati chakudya cholimba!
13 Aliyense amene amangodya mkaka okha, akanali mwana wakhanda, sakudziwa bwino chiphunzitso cha chilungamo.
14 Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima msinkhu, amene pogwiritsa ntchito nzeru zawo, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choyipa.
Atsogoleri muutumiki amakhumba kuona omwe akuwatsogolera akukula ndikuchitabwino ndikukhala ndikuthekela konse. Kotero, amafunsa mwakawilikawili otsatila awo, "Kodi mukukula motani"?
Atsogoleri muutumiki amafunsa "mukukula motani?" ndi cholinga cholimbikitsa kukula.
Olemba monvekabwino akuyembekezela kukula ndikupita patsogolo. Mwana wakhanda amayembekezeka kumwa mkaka, koma munthu okhwima akuyenera kumadya nyama. Atsogoleri muutumiki amayembekezela kukula kuchokela kwa omwe akuwatsogolera ndipo izi zimafunika kusintha. Atsogoleri muutumiki sakwanitsidwa ndi otsatila omwe amangopitiza kugwira ntchito pa mulingo omweomwewo. Amakhumba kukula ndipo amafunsa otsatila awo momwe akukulira kuti apeze mulingo wakusintha. Pongofunsa funso chabe kumathandiza otsatila kunvetsetsa kuti kukula ndikolimbikitsidwa ndi koyembekezeka.Pofunsa, "mukukula motani?" Atsogoleri muutumiki amalimbikitsa otsatila awo kudzuka ndikukuza kuthekela komwe sikunatulukile poyela.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "mukukula motani?" Kuti alimbikitse kutsimikizika.
Funso lokhudza kukula si lakamodzi kokha koma ndi lomwe atsogoleri muutumiki amagwilitsa ntchito kawilikawili. Olemba akuti chimodzi mwa maonekedwe a kukhwima ndi choti "pochigwilitsa ntchito kawilikawili aziphunzitsa okha...." Pomwe munthu wakula kumabeleka kusintha, koma kukula kotsimikizika ndi mfungulo wa kusinthika. Atsogoleri muutumiki amazindikila kuti anthu ambili mu udindo watsopano, amakula mwachangu pomwe aphunzila ntchito, koma amafikapo pomwe afikila mulingo winawake wakuthekela.Funso loti, "mukukula motani?" Limalimbikitsa otsatila kuti apitilize kukuza pomwe akuchitabwino ndi pomwe akutha kufikila.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "mukukula motani?" Pofuna kulimbikitsa kupitiliza.
Olemba akuwanetchela owelenga, "munthawi ino mumayenela kukhala aphunzitsi...." Choyembekezeka ndichoti ndi kukula ndi kukhwima kudzakhala kupasilana kwa zomwe aphunzila kuchoka kumbadwo wina kufikila Ku mbadwo wina. Atsogoleri muutumiki amaonetsetsa ndipo amakhumba kukula osati kwa mmodzi yekha yemwe akumutsogolera komanso kukula kwa omwe adzakhale akutsatila. Kotero, amafunsa otsatila awo, "mukukula motani?" Powakumbutsa kuti sikuti akuzikulitsa okha koma ndi cholinga cha omwe azawatsatile mtsogolo. Akhoza kufunsa funsoli munjila yachindunjinso "kodi ukuphunzitsa ndani kuti azatenge udindo wako?" Atsogoleri muutumiki amafunsa otsatila awo momwe akukulira kuti azathe kusiyila kwa ena zomwe akuphunzila.
|