Gawo #307, May 17 , 2023

Atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha: "Kodi ndikukula bwanji?"

Atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha: "Kodi ndikukula bwanji?"

Atsogoleri muutumiki amaika pamtima pawo kukula poti amanvetsetsa kuti kukula kwawo kumamasula kuthekela kochita zinthu komwe alinako.Amazindikilanso kuti kukula kwawo kumakhudza bungwe lomwe amatsogolera.Amazindikila kuti kuzikulitsa paokha ndi imodzi mwanjila yomwe angatumikilire omwe amatsatira. Amalingalira mwakuya pa zomwe Petulo anauza okulupilira onse:

2 Petro 3

18 Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.

Petulo akutiuza tonse kuti tipitilize kukula, ngati njila yopewela kuchoka pa "malo otetezeka" omwe anatchula pa vesi lambuyomu. Atsogoleri amakhala osamalitsa Ku kukula kwawo ndipo amadzifunsa okha kawirikawili, "Kodi ndikukula bwanji?"

Atsogoleri muutumiki amafunsa"Kodi ndikukula bwanji? "Pofuna kuona potsalira.

Petulo akuitanila atsogoleri Ku kukula mu "chisomo ndi chidziwitso..." Chidziwitso ndi dela limene atsogoleri ambili amazindikilira za kufunikila koti akule. Amapita mukalasi, amapezeka kumasemina, amanvela maphunzilo pawailesi, kapena kuwelenga mabuku kuti akuze chidziwitso chawo. Izi ndizopambana kwambili. Koma Paulo akuuza atsogoleri kuti aziika mulingo ofanana chidziwitso ndi chisomo. Chisomo ndi chamkatikati mwamunthu, chachikhalidwe, chamuntima. Zonse mutu ndi mtima zimafunikila ndipo ziziyendela pamodzi. Pamene kukula kwachitika mudela lokhalo lachidziwitso ndipo palibe kuyendela limodzi ndi khalidwe, zimapanga kusanva. pamene mtsogoleri wangokula mukhalidwe opanda kukula muchidziwitso, mitima yawo ingakhale pamalo abwino, komabe amasoweka zinthu zamuutsogoleri zomwe ndizofunika kwambili.

Atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha ngati akukula mmagawo onse. Amafunsa ngati khalidwe lawo lakhwima ndi kudziwa kwawo kwakula kuposa poyamba. Atsogoleri muutumiki amadziwa kuti amafunikila kudziwa kwammutu mwawo  ndi kuthekela muntima mwawo kuti achulukitse. Amalakalaka kuyendetsela pamodzi kudziwa  ndi maluso omwe akuwafuna kuti apite patsogolo muukadalo wawo, pamodzi ndi zinthu zokhudzana ndi mumtima wangwiro, chilungamo,kulimbamtima, ndi kuzichepetsa.

Atsogoleri muutumiki amafunsa: "Kodi ndikukula bwanji?" kuti atsimikize kolowera.

Atsogoleri muutumiki samangokhudzika kuti akukula Koma amafunanso kudziwa ngati akukula munjila yoyenela. Petulo akupeleka njila yakukula, "Kulani mu chisomo ndi chidziwitso cha Mbuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu." Akulozela kwa Yesu ngati chitsanzo chachikulu cha utsogoleri. Pomwe akhoza kupindula kuchokera Ku zipangizo zambili za utsogoleri zomwe sizokhuzana ndi zaumulungu, atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha funso lophweka, "Kodi ndikukhala ndikutsogolera monga Yesu kopambana mmene ndinalili chaka chatha?" Ngati yankho ndi "inde", Njila yoyenera Yatsimikizika.

Atsogoleri muutumiki amafunsa"Ndikukulabwanji? Kuti apeleke molondola"

Atsogoleri amakula pa zifukwa zosiyanasiyana.Ena akufuna kukwezedwa kapena kungofuna kuyendetsa bungwe lalikulupo.Ena amafina kuti Ena akhutile nawo chifukwa cha maudindo kapena maphuzilo awo a ukachenjede. Koma petulo akufotokoza momvekabwino kuti cholinga cha atsogoleri muutumiki kuti akule sikuzipatsa ulemelero okha Koma kwa Yesu. "Kwa iye kukhale ulemelero lero ndi kunthawi zosatha!" Atsogoleri muutumiki amakhudzika ndi zakukula mwawo, Koma zonse zokhuzana ndi utsogoleri wawo, si za Iwo eni, Koma za ena. Kukula kwawo kumakuza kuthekela komwe analandila kuchokela kwa mulengi wawo kotero zimabweletsa ulemelero kwa Iye. Kukula kwawo kumangowalola kutumikila mwabwino kuposa kale ndinso kubweletsa milingo yopamwamba yabwino yeyendetsela bungwe lomwe akutsogolera.

Zoti tilingalile ndikukambilana:

  • Kodi ndi mumadela ati omwe ndimaikapo chindunji chakukula kwanga?Kodi pali kufananitsa kwabwino. Pakati pa Kukula mukhalidwe ndi chidziwitso changa? Kodi ndimasankha mabuku? masemina ndi maphunzilo ndi malingaliro ofuna kuyanjanitsa zinthuzi?
  • Kodi Kukula kwanga kukunditengela kukhala ndikutsogolera mofananilako ndi Yesu? Ngati sichoncho,Kodi ndisinthe pati? Ngati ndichoncho,munjila iti yomwe izi zikutsimikizika kwa omwe andizungulira?
  • Kodi ndikukula kufuna kusangalatsa ena? Kodi ndikufuna kuti ndiziike ndekha  pamalo owonekabwino? Kodi ndikufuna kukwezedwa kapena udindo watsopano zomwe zili zozikuza ndikuzikonda?
  • Kodi ndikufunika chani mu ulendo wokula watsopano lino? Kodi ndikufunikila anthu ondiunikila? Mabuku? Masemina? maphunzilo antchito?

Mpaka nthawi ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Munkhani yotsatilayi, tiona mozama funso atsogoleri amafunsa ena, "Kodi mukukula bwanji?"

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2023

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online