Atsogoleri muutumiki amafuna Iwo amene ali otsatila kuti asangophunzila zoti azichita, koma momwe angaganizile pa Iwo okha. Kotero amafunsa mafunso amphamvu a iwo amene akuwatsatila ndikugwiritsa ntchito kukuza utsogoleri wawo. Atsogoleri muutumiki amayang'ana funso lomwe Mulungu amafunsa Mose "chili mudzanja lako ndi chani?" Chiyamba amadzifunsa okha "chili mudzanja langa ndi chani?" Kenaka polingalila zomwe funsoli likutathauza kwa Iwo amene amawatsatila ndikuwafunsa funsoli.
Eksodo 4
2 Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?” Mose anayankha kuti, “Ndodo.”
3 Yehova anati, “Tayiponya pansi.” Mose anayiponya pansi ndipo inasanduka njoka ndipo anayithawa.
4 Kenaka Yehova anati kwa iye, “Igwire mtchira.” Ndipo Mose anayigwira mchira njokayo ndipo inasandukanso ndodo mʼdzanja lake.
5 Yehova anati, “Ukachite zimenezi ndipo akakukhulupirira kuti Yehova, Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo, wakuonekera iwe.”
Atsogoleri amafunsa funso la otsatila awoli pa zolinga zitatu.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "chili mudzanja lako ndi chani?" Kuti avumbulutse kuthekela.
Munkhaniyi Mulungu anaona kuthekela komwe Mose anali nako, koma Mose sanaone! Mulungu sanampatse Mose ndandanda wazinthu zomwe anaona, koma mmalo mwake amafunsa funso. Akufuna Mose awone ndodo mosiyana ndikale. Atsogoleri muutumiki amafunsa funso lotele ndi cholinga choti otsatila awo azindikile mphatso zomwe ali nazo mwa iwo okha. Angathe kubweleza kufunsa kangapo funsoli kapenanso kuonjezelapo "palinso chani chomwe mulinacho?" mayankho ena anapelekedwa kale. Atsogoleri muutumiki amakhumba otsatila awo kuti sali anthu "wamba" chabe, Koma anthu omwe analengedwa munjila yapadeladela pa cholinga chapadeladela.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "chili mudzanja lako ndi chani?" Kuti amasule luso loganiza.
Mulungu amamuitana Mose kuti agwilitse ntchito ndodo yake munjila yatsopano ndipo kaganizidwe kake kamayenela kuti kasinthe. Atsogoleri muutumiki amapanga chisankho choti mmalo mopeleka yankho Ku mavuto, angatumikile bwino pofunsa wina, "ungachite chani kuti uthane ndi vutoli?" kapena "kodi ungapititse bwanji patsogolo chitidwe umenewu?" Amakuza anthu pofunsa funso kufikila kupanga zinthu pawokha komwe kuli mkati mwawo kwayamba kuonetseledwa.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "chili mudzanja lako ndi chani?" Kuti akanize moyo odalira.
Atsogoleri amakumana ndi yeselo loti iwo akhale yankho. Mulungu analitu nawo mayankho kwa Mose! Koma Mulungu amafunsa Mose funso pofuna kumpanga kuti aganize. Anafuna Mose kuti akuze kuganiza pa iye yekha osati kudalila pamunthu kuti amuuze zochita. Mulungu anasankha kugwiritsa ntchito chomwe chinali mudzanja LA Mose mmalo moti amupatse china chake chatsopano. Atsogoleri muutumiki amaphunzila kwa Mose pofunsa ndi chani chili mudzanja lako? Munjila zomwe zimathandiza otsatila kukhala ndi moyo osadalira mtsogoleri. Iyi ndi njira yopangila ophunzila yomwe ikhonza kutenga kanthawi kabwino kapadela koma pan'gonopandono mtsogoleri muutumiki amathandiza otsatila kuti azitha kuganiza pa iwo okha, kupanga zisankho ndi kuchitapo kanthu. Amatumikila pofunsa mafunso omwe amakakamiza otsatila kuziona okha kuti ali ndi mayankho. Atsogoleri muutumiki ali ndi mayankho koma kawirikawiri amatumikila pofunsa mafunso mmalo moulula zochita. |