Atsogoleri a masomphenya nthawi zonse amakhala ndi chikumbumtima cha zosowa zipangizo kuti akwaniritse masomphenya. Zipangizozi zitha kukhala ndalama, anthu, maluso, kapena chidziwitso kapenanso zinthu zina.Atsogoleri kawirikawiri amayamba kufufuza zinthu izi kunja kwawo ndi kuyamba kuyang'ana uku ndi uku kuti akwanitse chosowa chomwe alinacho.Koma atsogoleri muutumiki amaphunzira kuchokera Ku funso lomwe Mulungu anafunsa Mose,"Kodi chili mudzanja lako ndi chani?"
Eksodo 4
2 Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?” Mose anayankha kuti, “Ndodo.”
3 Yehova anati, “Tayiponya pansi.” Mose anayiponya pansi ndipo inasanduka njoka ndipo anayithawa.
4 Kenaka Yehova anati kwa iye, “Igwire mtchira.” Ndipo Mose anayigwira mchira njokayo ndipo inasandukanso ndodo mʼdzanja lake.
5 Yehova anati, “Ukachite zimenezi ndipo akakukhulupirira kuti Yehova, Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo, wakuonekera iwe.”
Kulankhulana kwa pakati pa Mulungu ndi Mose kuli ndi zambili zoti atsogoleri muutumiki atsatile ndipo amachita bwino podzifunsa okha funso" Chili mudanza langa ndi chani?"
Atsogoleri muutumiki amafunsa "chili mudzanja langa ndi chani? "Kuti azindikile zipangizo.
Mose anali ndi ndodo mudzanja lake. lnali chinthu wamba chomwe Mose amayendela tsiku ndi tsiku, koma sanazindikileko kuti chinali chani. Iye ankangoti ndi ndodo yomwe aliyense amakhala nayo. Koma Mulungu anamufunsa kuti azindikile chomwe anali nacho.
Atsogoleri muutumiki amaphunzila kudzifunsa okha chomwe alinacho munthawi imeneyo pomwe akumana ndi chobetchela kapena chosowa. Kodi ndichitepo chani munyengo imeneyi? Kodi ndili ndi zipangizo zanji? Kodi ndikudziwa ndani yemwe angathandize? Mafunso onsewa amapeleka mpata ozindikila zipangizo zomwe sizikanadziwika. Mulungu anatenga chomwe Mose anapeleka ndi kugwiritsa ntchito kupanga zozizwa. Asanayang'ane kwina kufuna zipangizo, atsogoleri muutumiki amayang'ana chatsopano chomwe Iwo alinacho kale. Ndipo pomwe akupereka chabe zipangizozi kwa Mulungu, amapeza kuti ali ndi zokwana!
Atsogoleri muutumiki amafunsa "chili mu dzanja langa ndi chani?" Kuti ayambe kuzidalira.
Pomwe ndodo inasanduka njoka, Mose nthawi yomweyo amayenera kuti athawe. Koma Mulungu anamuuza kuti atole njokayo, chomwe Mose samadziwa kuti angakwanitse. Mulungu amafuna kuti iye akule mumoyo ozidalila ndikugonjetsa mantha. Atsogoleri mu utumiki amafunsa "chili mu dzanja langa ndi chani?" Ndicholinga chowonjezela nchito zatsopano kapena maudindo ena omwe onali asanakonzekele kuwachita.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "Chili mu dzanja langa ndi chani?" Kuti athane ndi moyo odalira.
Mose sanadzimve kukwanila pa ntchito yomwe anaitanidwa kuti agwile.iye amangoziona uti ndi mbusa oweta ziweto mchipululu opanda kanthu koti nkupeleka. Akanatha kuganiza kuti amasowa zambili zoposa zomwe anali nazo mdzanja lake kuti atsogolere.Anaziona yekha monga munthu ofuna mathandizo mmalo mokhala ndi kanthu koti apereke.Mchitidwe uwu odalira unaononga Atsogoleri ambili. Koma atsogoleri muutumiki amayamba awona kaye zomwe zilipo. Asadafunse "Kodi ndikufuna chani kwa iwe" Amafunsa "Kodi chili mudzanja langa ndi chani chomwe ndingakupatse?"
|