Gawo #304, March 22, 2023

Atsogoleri mu utumiki amafunsa otsatira awo: Kodi Mukukhala ndani?"

Atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha mafunso ovuta za chomwe Iwo akukhala. Pomwe akupeza chenicheni ndi chitsogozo za chindunji chawo, amatumikilanso iwo amene akuwatsogolera powalimbikitsa kuti ayende ulendo ofanana ozindikira. Amakhumba kuti malangizo a Paulo akhale othandiza osati kwa miyoyo yawo yokha komanso kwa Iwo owatumikira.

2 Akorinto 3

18 Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.

Atsogoleri muutumiki amalakalaka kutulutsa chabwino mwa otsatira awo.

Akhumba kusinthika komwe kuli mu vesi tawerengayi. Ndipo sakhala ndimantha kufunsa mafunso mwandale omwe adzatsogolera ena pa ulendo wawo wautsogoleri. Amazindikira  kuti kufunsa mafunso osati kupeleka mayankho  zimapanga omwe akuwatsogolera kuti akule ndi kuyamba pawokha kuganiza  ndi kulingalira. Amatumikira pofunsa omwe akuwatsatira, "Kodi mukukhala ndani?" Pomwe ndipothandiza amakhala ofuna kupereka zomwe apeza pawokha koma amakhala ofuna kungopelekha funso kwa munthu ndikuwalola kuti alingalire pawokha. Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti funso iri ndi lozama kwa moyo wa wina wake koma osati njira yomuyeza munthu mmene akuchitila! Pomwe akufunsa mozichepetsa funsoli la omwe akutsatila, amalingalira cholinga chawo pofuna kuonetsetsa kuti khumbo lawo kulabadiladi za munthu wina ndi khumbo lofuna kuwaona akukula. Amakana fufunsa funsoli ngati njila yofuna kuyang'anilapansi mavuto omwe alipo. Amatumikira mwachikondi posamalira mulingo omasukilana umene munthu amaonetsa poyankha mafunso. Pomwe akutengera ena kuganiza za funso, amalifunsa ndi zolinga zingapo mkati mwawo.

Atsogoleri muutumiki amafunsa "Kodi mukukhala ndani?" Kuti awonetse chitsogozo.

Poyenera kutero atsogoleri muutumiki atha kuyitanira omwe akutsatira kuti alingalire ulendo wa kukula kwawo pofunsa, Kodi mukukhala wapabanja\kholo\mtsogoleri wa mmudzi\ogwirantchito yemwe mukufuna mutakhala? Kodi pali njira zomwe ndingakuthandizileni kuti muyende munjira yomwe mukufuna kupita? Kodi kuli zotchinga msewu zomwe ndingachotse munjira yanu? Atsogoleri muutumiki amazindikira omwe akuwatsatira ngati akuyenda mozindikila kapena mosazindikila. Amafunsa funso ndicholinga choti owatsatira azindikire za komwe akupita. Funso limayang'ana mmene aliyense aliri payekha ndipo siliyang'ana za udindo pa ulendo koposela komwe akupita.

Atsogoleri muutumiki amafunsa "Mukukhala ndani?" Kulozela chindunji.

Atsogoleri muutumiki amadziwa mchitidwe wa Iwo eni pofuna kumasula chindunji choyenera, choncho atha kufunsa iwo otsatira "Kodi yemwe akukhudza mtima wanu ndani? Kodi mumapita kuti kokafunsa nzelu ndi zoti muchite? Kodi izi zikukuthandizani mu njira yomwe mukufuna kutsata? Funso limagwirantchito ngati chokumbutsa kwa otsatira kuti chindunji ndichofunika zedi polondoloza njira.

Atsogoleri muutumiki amafunsa "Kodi mukukhala ndani?" Kuti amasule kusinthika.

Cholinga cha mtsogoleri otumikira ndi kuumba, kulimbikitsa ndi kumasula munthu yemwe akutsatira. Amakhumba chabwino chamoyo wawo, osati mudela lomwe akutumikira pabungwe pokha koma mumoyo wawo onse. Amatumikira omwe akuwatsatira powathandizila kukhala anthu omwe analengedwa kudzachala. Kotero, amafunsa, "Kodi mukukhala ndani?" kuwalimbikitsa kudziwa mphamvu ya kusinthika mumyoyo ya iwo eni.

Zoti tilingalirepo ndikukambirana:

  • Kodi ndili ndi chikondi chokwanira ndi kukhudzika kwa amane ndikuwatsogolera pakuwafunsa "Kodi mukukhala ndani?" Ngati sichoncho,Kodi izi zikusonyeza chani za ntima wanga ndipo ndikuyenela kusintha chani? Ngati ndichoncho, Kodi ndizayamba liti kuwafunsa funso limeneri?
  • Ndisadafunse aliyense funso limeneli "Kodi mukukhala ndani?" Kodi ndili ndi zolinga zobisika za chifukwa chomwe ndikuwafunsila funso lotele? Kodi cholinga changa chowathandiza ndichenicheni ndipo Kodi  chikuposa kukhumudwa kwanga pa momwe akugwilira ntchito?
  • Kodi ndili ofuna kungofunsa chabe funso la ena osati kulamula yankho kwa iwo? Kodi ndine ofuna kupereka zomwe ndaona  pokhapokha ngati ndafunsidwa kutero ndi munthuyo?

Mpaka nthawi ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

Muphunziro lotsatirali, tizaona pa funso lomwe atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha: "Chili mudzanja langa ndi chani?"

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2023

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online