Gawo #303, March 8, 2022

Atsogoleri Muutumiki Amadzifunsa Okha: "Kodi Ndikukhala Ndani?"

Atsogoleri Muutumiki amagwiritsa ntchito mafunso pounika ulendo wawo wautsogoleri ndikulimbikitsa omwe akuwatsatira kuchita chimodzimodzi. Khalidwe lofunsa mafunso limathandiza atsogoleri muutumiki kukhala odziwa kuti alibe mayankho onse komanso kuti nawonso ali pa ulendo wawo wautsogoleri. Amafunsa "Ndine ndani?" Pokhazikitsa chomwe ali monga tinaonera muphunziro lapitali. Kenaka Amadzifunsa Okha "Kodi Ndikukhala Ndani?" Pofuna kulondoloza njira yomwe akutsata.

2 Akorinto 3

18 Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.

Atsogoleri mu utumiki amakhumba kuyenda motsata "ulemelero ochulukirachulukira" ndipo amasiya kuona zomwe izi zikutanthauza pa moyo wawo ndi utsogoleri.

Atsogoleri Muutumiki amafunsa"Kodi Ndikukhala Ndani? "Polondoloza njira yoyenera.

Atsogoleri onse akuyenda pa ulendo, ndipo amaika zinthu zogwirika ngati mulingo wa kuchitabwino kwawo. Amaika chidwi pa masomphenya ndi zotsatira ndipo amaika maganizo ochepa pa Iwo wokha ngati anthu. Atsogoleri akuyenda, kawirikawiri mwachangu! Koma atsogoleri muutumiki amayenda mwapanq 'ono panq' ono kwakanthawi ndithu pofunsa ngati akutsata njira yoyenera. Iwo "akusinthika" ndi kuphunzira kudzifunsa okha kuti akukhala otani. Molimbamtima akudzifunsa okha, "Kodi Ndikukhala okonda? Opanda tsankho? Wachifundo? watchelu? Owonamtima? Posiyanitsa ndi chaka chathachi, Kodi pali kusintha kwanji pamoyo wanga? Mafunso amenewa amakhala chikwangwani pa ulendo omwe mtsogoleri akuyenda ndipo atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha mafunsowa potsimikiza ngati akutsata njira yoyenera.

Atsogoleri muutumiki amafunsa "Ndikukhala ndani?" Kuti atsimikize chindunji.

  Paulo akiputikumbutsa Ife"Tionetsele ulemelero wa Ambuye... "Apa akutanthauza nkhani ya chindinji. Atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha za chindunji cha ulendo wawo. Sakhala ndimantha kufunsa ," Kodi Ndikukhala munthu odziwika kwambiri pa mawailesi akanema, kwa atolankhani? manyuzipepala kapena Yesu? Kodi izi zikukhudza bwanji moyo wanga ndi utsogoleri? Kodi ndikupereka moyo wanga mochuluka molunjika kwa Iye ndikufunafuna mayankho kuchoka kwa Iye za zobetchela zomwe ndikukumana nazo pa utsogoleri? "Atsogoleri muutumiki amadzifunsa okha mafunso okhwima pofuna kuonetsetsa kuti chindunji chawo chili munjila yoyenera.”

Atsogoleri muutumiki amafunsa "Ndikukhala ndani?" Kuti atakase kusintha.

Paulo akuonetsela kuti kusintha kwathu kukhale ndi "ulemelero wochulukilachulukila". Atsogoleri muutumiki amakhala kaye duu polingalira za chomwe akukhala kuti kukula kwawo kutakasidwe. Amaunguza njila yomwe akutsata ndi chindunji ndi ngati nkofunikira,kukonza ndi kuchepetsa. Podzifunsa mafunso Iwo eni, Atsogoleri muutumiki amatakasila kukula kwa Iwo eni. Pomwe pafunika kutero amaika zofunika kuti akule zomwe zimakhala chindunji cha phunziro  lamtsogolo mu ziphunzitsozi.

Atsogoleri muutumiki amaphunzira kudzifunsa okha funsoli" Kodi Ndikukhala Ndani?"

Pakapita kanthawi. Amaika padela nthawi yoganiza kudzela mmayankho awo ndipo kawirikawiri amaona kuti ndizothandiza kuyamba asiya kaye ntchito zawo ndikudzifunsa kaye mafunsowa. Ikani nthawi ndi tsiku nkati mwa ndondomeko za ntchito zanu kuti muyambe kudzifunsa funsoli ndikulingalira.

Zoti tilingalire ndikukambirana

  • Ndikamayanq'ana chaka chapitachi moyo wanga,Kodi ndapanga kukusintha kotani pa chomwe ndili pano? Kodi ndikuyenda munjira yomwe ndikufunika kuyenda? Kodi ndingatsilize motandi ndime iyi, kuyambira chaka chathachi,Ndikukhala....? Kodi mamuna wanga kapena mkazi wanga kapena mzanga wapafupi nane akuti chani za chomwe ndikukhala?
  • Kodi chindunji changa chili kuti? Kodi ndimatenga kuti zomwe zimandipanga kukhala chomwe ndili, chitsogozo, maganizo, ndi nzeru? Kodi Ndikukhala munthu wachindunji pa Yesu kapena kwinako? Kodi ndandanda wanthawi wanga ukuti bwanji za chindunji changa? Kodi ndikufunika kusintha pati ndi pati?
  • Kodi kusintha kwanga kungatakasidwe motani? Potsamira pa mayankho a mafunso ambuyo,kodi ndikuyenera kusintha pati pa moyo wanga? Kodi ndiuze ndani za zinthu izi?

Mpaka nthawi ina, ine wanu wapaulendo,

Jon Byler

 

Muphunziro lotsatirali, tionanso funso lomweli atsogoleri muutumiki amafunsira ena,"Kodi ukukhala ndani?"

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatila
chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira.Angathe kulembetsa mwaulere komanso kuona magawo akale.mukafuna kupeza magawo akale , dinani apa.Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi abusa Grace Kacheto Saizi, gracekacheto@yahoo.com

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2022

Unsubscribe   |   Modify your subscription   |   View online