Atsogoleri Choyambilira amadzifunsa okha,"Ndine ndani?" Koma tsopano amaona pa iwo amene akuwatsatira ndikuwafunsa funso lofanana, "Ndinu ndani?" Atsogoleri amakonda iwo amene akuwatsatira ndipo khumbo lawo pa owatsatira ndi lomwe iwo amakhumba pa iwo. Amaitanira kuti nawonso aphunzire kuzidziwa okha, mphamvu zawo komanso zifoooko zawo.Amafuna otsatira awo kuti nawonso atsatire zomwe Paulo adalangiza:
Aroma 12
3 "Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani." Atsogoleri otumikira amathandiza otsatira awo kuti aganize pa iwo okha ndi "moona mtima"pofunsa kuti" Ndinu Ndani?"
Atsogoleri muutuiki amafunsa "Ndinu ndani?" Kuti akhazikitse chomwe Ali.
Atsogoleri muutumiki samazindikira otsatira awo powona udindo wawo chabe. Amazindikira kuti munthu aliyense ndi osiyana ndi nzake kuposela pa zomwe amachita. Amasakasaka kuphunzira kumudziwa munthu wina aliyense amene amamutsogolera mozama. Amakhala mu kalasi ya iwo amene akuwatsogolera. Ndi chokhumba chenicheni kuti adziwe amafunsa"Ndinu ndani?" Kuposela pa funso lokhudzana ndi ntchito yomwe amagwira, atsogoleri muutumiki kawirikawiri amafunsa mafunso ngati, "Chimakupangitsani kuseka ndi chani? Chimakupangitsani kulira ndichani? Ndimunthawi yotani yomwe moyo wanu umafikapo pomvabwino?" Atsogoleri muutumiki nawonso amafuna owatsatira kuti adzimvetsetsetse pawokha. Amafunsa otsatira awo "Ndinu ndani?" Kuti alimbikitse kuzilingalira pawokha pa chomwe iwo ali.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "Ndinu ndani?" Kuti awonetsere kuthekera kwa mphamvu.
Atsogoleri muutumiki amazindikira kuti wina aliyense wa otsatira awo ali ndi mphatso yosiyana ndi nzake yomwe Mulungu anawapatsa. Amafunsa, "Ndinu ndani?" Kuti azindikire kuthekera kwa mphamvu zawo. Sakhala ndimantha pofunsa, "Kodi mumakonda kuchita chani mukakhalapo? Kodi chomwe chimakulimbikitsani kwambiri ndichani? Kodi mungakonde kuchita chani mwapafupipafupi? Atsogoleri muutumiki amakhala ofuna kuikiza nthawi yawo ndi mphamvu zawo kuti azindikire kuthekera kwakukulu komwe kuli mwa anthu omwe akuwatsogolera chifukwa amasamaladi za munthu. Pomwe pakufunika kutero ndi pomwe pali potheka, amakhala ofuna kusintha udindo wa munthu kuti ugwirizane ndi kuthekera kwa mphamvu zake. Amakhala ndi chidwi pa kuthekera kwa mphamvu zomwe zili pa iwo amene akuwatsogolera ndi kusakasaka kuika pa mulingo wabwino kuthekera komwe iwo akuona mwa munthu aliyense.
Atsogoleri muutumiki amafunsa "Ndinu ndani?" Kuti awonetsere zofooka.
Atsogoleri muutumiki amafunsa moterenso, "Ndinu ndani?" Kuti awonetsere poyera zofooka zomwe zili mwa omwe akuwatsogolera. Monga akudziwa pawokha, kuti palibe munthu angangale wamphamvu magawo onse. Atsogoleri muutumiki sawonetsela poyera zofooka za wena ndicholinga choipa kapena chowagwetsa mphwayi. Mmalo mwake, amathandiza otsatira awo kuti amvetsetse zofooka zawo kuti amange gulu lamphamvu. Pozindikira dela lawo lofooka, otsatira azakhala ofuna kupatsira wina ntchito wa mugulu lawo amene ndi mphatso yake. Kotero, atsogoleri muutumiki amafunsa otsatira awo "ndimadela ati antchito zanu amene simukondweletsedwa nawo? Ndimadela ati antchito yanu omwe wina wa mgulu mwanu akhoza kuwagwira bwino?" Amamvetsela mosamala mayankho omwe akubwela ndi kutumikira pothandizira otsatira kuti azindikire njira zomwe ena akhoza kuthandizira pa zofooka zawo.
Atsogoleri muutumiki amapitiliza ulendo wawo ofunsa mafunso oyenera pomafunsa omwe akuwatumikira,"Ndinu ndani?" |