Atsogoleri ambiri amaziona okha ngati anthu okhala ndi mayankho koma atsogoleri muutumiki amakhala okhudzika kwambiri za kufunsa mafunso oyenera koposa kukhala ndi mayankho oyenera. Kufunsa mafunso kumathandiza anthu kuganiza, kumathandiza anthu kukula ndiponso kumathandiza anthu kutsogolera.Kotero, atsogoleri mu utumiki amazikulitsa okha komanso ndi ena pophunzira kufunsa mafunso abwino a masomphenya amtsogolo a Iwo okha ndi omwe Iwo akuwatsolera. Mu phunziro iri tiona mozama mafunso omwe atsogoleri mu utumiki amadzifunsa okha ndi funso lolingana lomwe amafunsa omwe akutsatira. Funso loyambilira loti afunse choyambilira atsogoleri adzifunse okha Kuti, "Ndine ndani?" Paulo akuitanira funso iri pomwe akuti.
Aroma 12
3 Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani.
Paulo akuitana atsogoleri onse kuti aziganizire okha "modzichepetsa" Si nthawi zonse kumakhala kuzikonda ngati ukuganiza za iwemwini. Pomwe zachitika mwanjira yoonamtima nd ikudzichepetsa imodzi mwanjira zomwe atsogoleri amatumikilira anthu omwe akuwatsogolera ndi pomwe aganiza moyenera za chomwe Iwo ali. Atsogoleri mu utumiki amadzifunsa okha , "Ndine ndani?" kuti azindikire zithu zitatu za chomwe Iwo ali.
Atsogoleri mu utumiki amafunsa"Ndine ndani?".
Mtsaogoeri aliyense afunika uti azikike mu chomwe ali. Paulo akuwauza atsogoleri kuti kuti alingalire zoti Iwo ndi ndani. Akupanga izi mundime yomwe imakamba za mphatso zosiyanasiyana zomwe Mulungu wapereka kwa aliyense payekhapayekha. Yeselo la mtsogoleri aliyense ndiloti azindikire pa iwo okha mphatso zawo. Zimenezi zitha kutengera Ku kuganiza kwaboza komwe ndi kozikonda "koziwona kuti ndi opambana kwambiri koposa mulingo" Koma atsogoleri mu utumiki amadzifunsa okha, "ndine ndani?" Ndicholinga choti akhazikitse chomwe Iwo ali osati muzomwe Iwo amachita, koma mu zomwe ali. Akafunsa funso limeneri, amapewa kuziyelekeza ndi atsogoleri ena koma amakhala chindunji pa zomwe ali. Amazindikira kuti Mulungu amagawira mphatso koma chomwe ali chimatsamira mwa opereka mphatso, osati mphatsoyo.
Atsogoleri mu utumiki amafunsa "Ndine ndani"? kuti awonetsere mphamvu zawo.
Paulo akuwafunsa atsogoleri kuti alingalire pa "chikhulupiliro" kapena mphatso zomwe Mulungu wapereka kwa owo. Mundime,auyang'ana za kusiyana kwa mphatso zomwe Mulungu wapereka kwa anthu. Atsogoleri mu utumiki amaika maziko a chomwe Iwo ali pa ubale wawo ndi Mulungu koma amadzifunsa okha "Ndine ndani?" Kuti azindikire ndi kuonetsera mphamvu zawo. Amafufuza kuti azindikire ndi kutsimikiza mphatso zomwe Mulungu wapereka kwa Iwo. Amakhala ndi mtima ofuna kuphunzira za madela omwe Iwo ali a mphamvu ndicholinga chiti afike pothela pa mphamvu zawo. Amadziwa kuti Iwo angatsogolere mwabwino mu mbali yawo ya utsogoleri pomwe akugwiritsa ntchito mphamvu zawo zapadeladela zomwe ndi Mulungu anawapatsa.
Atsogoleri mu utumiki amafunsa "Ndine ndani?" Kuti awonetsele poyera zofooka zawo.
Paulo akuwafunsa atsogoleri kuti azifunse mwaiwo okha "modzichepetsa" Pomwe atsogoleri mu utumiki akuika chindunji chawopa mphamvu zawo, amadzifunsa okha funso lotere, " Ndine ndani?" Kuti awonetsele poyera chomwe iwo asali. Amavundukula chofooka chawo mu ulendo wa kuzizindikira wekha. Pomwe akuchita izi, saziyelekezera ndi ena omwe ali ndi mphatso zosiyana. Kapena safuna kukhala a mphamvu mu madela omwe iwo sadapatsidwe mphatso. Mmalo mwake, atsogoleri mu utumiki amalolera kufooka kwawo kuwatengele kwa ena omwe amachitabwino mphamvu zawo. Amalolera kufooka kwawo kuti kuwathandizire kumanga gulu lowumbika bwino.
Yambani ulendo ofunza mafunso oyenera podzifunsa wekha,"Ndine ndani?"
|