jpeg

Gawo 274, December 9, 2020

Phokoso la Utsogoleri wa Chete…..mu Kulingalira

Atsogoleri otumikira amaphunzira kuti utsogoleri sikuti umangolankhula nthawi zonse. Amavomereza kuti nthawi zina, chomwe chimachitika mwa chete chingathe kukhala ndi kukhudza kochuluka kusiyana ndi zomwe zimachitika polankhula pagulu! Amagwira kuitana kwa wolemba bukhu la Maliro potenga nthawi mukulingalira kwa chete:
Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindilira modekha chipulumutso cha YEHOVA. Nkokoma kuti munthu asenze goli ali wamng’ono. Akhale pa yekha, natonthole, pakuti mulungu wamsenzetsa ilo, aike kamwa lake mfumbi; kapena chilipo chiyembekezo (Maliro 3: 26-29)
Uphungu uwu udalembedwa kwa anthu omwe amalilira chionongeko cha Yerusalemu, mzinda wawo waukulu. Mu nthawi ya mavuto amenewo maitanidwe akudza a kulindira modekha, nakhale payekha. Gawo ili silikuoneka kuti ndi loyenersa kugwiritsa ntchito pa utsogoleri! Koma lili ndi nunsu za choonadi kwa mtsogoleri wotumikira aliyense yemwe akufuna kuchepetsa liwiro ndi kumvetsera. Kulingalira kwa chete kungathe kuwumba moyo wa tsiku ndi tsiku wa mtsogoleri wotumikira mu njira zingapo.

Kulingalira kwa chete kumalimbikitsa kulindilira.

‘nkokoma kuti munthu ayembekeze modekha….’ Atsogoleri ndi anthu ochita ntchito, a zolinga  ndi zipambano. Amafuna kupita patsogolo! Mndandanda wa ‘zomwe akufuna kuchita’ umawaitana  mofuwula kuti achite kanthu ndipo kulindilira modekha nthawi zambiri sikumakhala ma mndandanda wawo!
Koma kulingalira mwa chete,‘ndi kwabwino’ ndipo kumadzetsa mapindu ochuluka. Nthawi ya chete imatonthoza moyo. Imapereka chindunji. Imakumbutsa mtsogoleri kuti Mulungu akulamulira, osakhala iwowo. Kulindira modekha kumapangitsa mtsogoleri kuchepetsa liwiro ndipo mosadziwika bwino kumankonzekeretsa ku ntchito. Atsogoleri ambiri, kuphatikizapo ine, amapeza phindu lalikulu mmoyo wodziletsa wa tsiku ndi tsiku wotenga mphindi zingapo kukhala chete asadayambe zochitika za tsiku. Atsogoleri otumikira amakonzekera ntchito polindilira mu kulingalira kwa chete

Kulingalira kwa chete kumalimbikitsa undekha.

‘Akhale yekha chete’ utsogoleri pafupifupi umachitika ndi ena. Atsogoleri amafuna kukhala ndi kugwira ntchito kudzera mwa ena. Atsogoleri ambiri samamva bwino kukhala okha. Undekha umadzetsa mafunso pa mbalambanda omwe mtsogoleri mwina sangafune kukumana nawo. Kukhala chete pa wekha usakuchita kanthu kapena opanda udindo kuti ziphimbe zamkati mwake zingathe kumpanga mtsogoleri kumva ngati ali maliseche ndipo wayaluka. Mafunso a zofuna zake, zolingalira ndi chitsogozo zimaumbika mu undekha. Kulingalira pa wekha kumathandiza mtsogoleri kuvomereza zomvaimva zake, ululu ndi zovuta.
Undekha umadzutsa mafunso olimba omwe nthawi zambiri timafuna kuwathawa kudzera mu phokoso  ndi zomwe tikukwaniritsa.
Lemba ili limalimbikitsa atsogoleri kusazemba undekha koma kuchita nawo ngati mphatso. Undekha ndi mphatso yomwe imakonzekeretsa mtima popanga ubale ndi ena. Atsogoleri omwe sadaphunzire kukhala paokha amakhala a phokoso, komanso owopsa omwe amaphimba kusatetezeka kwawo ndi ntchito yawo ya utsogoleri.
Atsogoleri otumikira amakonzekera kukumana ndi ena potenga nthawi paokha.


Kulingalira kwa chete kumalimbikitsa kusinkhasinkha.

‘Aike nkhope yake mfumbi….’ Chodabwitsa motani ichi? Palibe yemwe amakonda fumbi; timayesetsa momwe tingathere kulipewa ndi kulithawa. Koma Mulungu akutiwuza kutengako nthawi ‘yozikwilira’ tokha mu fumbi lowawa. Pomwe tikuima mu kulingalira kwa chete, timaona vuto la fumbi. Timamva ululu. Timalingalira. Timasinkhasinkha za mafunso okhwima a moyo.
Atsogoleri nthawi zambiri amafuna mayankho ku ululu wa ena ndi kufufuza njira zothetsera kuvutikako kapena mazunzo. Gawo ili likulimbikitsa ife kuti choyamba tiyenera kutenga nthawi yokhala chete nkhope yathu ili mu fumbi tisanachite kanthu. Atsogoleri otumikira amakonzekera kukumana ndi zosowa za omwe avulala poyamba mwa kachetechete kulingalira kaye ululu wawo.
Kulingalira mwa chete ndi ntchito yovuta! Siingangochitika mwa wamba makamaka mu nyengo ya zinthu zamakono ino. Koma utsogoleri wa chete umalankhula mofuula mukulingalira kwa bata. Atsogoleri otumikira amapita pamwamba potseka pakamwa!

Zina zomwe tingalingalirepo ndi kukambirana

  • Lingalirani mawu a wolemba Salimo, ‘Khala chete, nudziwe kuti ine ndine Yehova……’ (Masalimo). Ndi chifukwa chani tiyenera kukhala chete kuti tidziwe kuti iye ndi Mulungu? Chimachitika ndi chani momwe timazionera tokha ndi momwe timamuonera Mulungu pomwe takhala chete? Zimanena chani za ine ngati ndikuvutika kukhala bata?
  • Kodi ndimalingalira mwa chete nkomwe? Kokwanira? Kodi ndi kowirikiza motani komwe ndiyenera kulingalira tsiku lililonse, pasabata, nkupita kwa nthawi?  Ndi chani chomwe chikundilepheretsa kulingalira mwa chete? Kodi izi zidakhudza bwanji  utsogoleri  wanga?
  • Kodi ndi liti lomwe ndidakhala pandekha popanda kusokonezedwa ndi foni, email, kapena zina zomvetsera ndi kuwerenga?  Kodi ichi chimaonetsera chani za momwe ndimakhalira? Ndi njira iti yomwe ndiyenera kusintha?
  • Chimachitika ndi chani mkati mwanga pomwe ndili ndekha? Kodi ichi chimaonetsera kuti ndine ndani?
  • Kodi ndili ndi njira yolemba ndi kukumbukira maganizo anga, malingaliro ndi zomwe ndazindikira mu nthawi yomwe ndinali ndekha? Ngati sichoncho, kodi ndiyambe kusunga kabuku kolemba zochikitika mu nthawiyi?
  • Kodi pali kuopsa koti nthawi yanga yambiri yikumakhala yolingalira mwa chete ndi kuchita kanthu mwa pang’onopang’ono? Ngati ndi choncho, ndi chani chomwe ndiyenera kuchita kuti kulingalira ndi ntchito zichitike mofanana?

    Mu gawo lotsatira, tidzawona za phokoso la utsogoleri wa chete…..mu pemphero.

Kufikira nthawi ina, Ine wanu wa paulendo,

Jon Byler

Tumizani kwa anzanu omwe akufuna kutsatira chitsanzo cha Yesu potsogolera ngati otumikira. Angathe kulembatsa mwaulere komanso kuwona magawo akale. Mukafuna kupeza magawo akale, dinani apa.  Magawo awa amatanthauziridwa mchichewa ndi Abusa Joseph Saizi, josephsaizi2017@gmail.com
 

Reflections for Serving Leaders is published by Center for Serving Leadership and Jon Byler. Copyright, 2020

Modify your subscription    |    View online